2 Mafumu 6:1-33

6  Tsopano ana+ a aneneri anauza Elisa kuti: “Taonani, malo+ amene tikukhala pamaso panu pano tikupanikizanapo.+  Tiyeni tipite ku Yorodano, kuti aliyense akatengeko mtengo woti tikamangire+ malo okhala.” Choncho Elisa anati: “Pitani.”  Ndiyeno wina anati: “Tiyeni mupitire limodzi ndi atumiki anu.” Elisa atamva anati: “Chabwino, ndipita nawo.”  Choncho iye anapita nawo limodzi. Atafika ku Yorodano iwo anayamba kudula mitengo.+  Munthu wina akudula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka+ n’kugwera m’madzi. Pamenepo munthuyo anayamba kulira kuti: “Kalanga ine mbuyanga!+ Nkhwangwayo inali yobwereka!”+  Munthu wa Mulungu woonayo anafunsa kuti: “Yagwera pati?” Iye anamusonyeza pamene inagwera. Nthawi yomweyo Elisa anadula kamtengo n’kukaponya pamalopo ndipo nkhwangwayo inayandama.+  Ndiyeno anamuuza kuti: “Itenge.” Munthuyo anatambasula dzanja lake msangamsanga n’kuitenga.  Tsopano mfumu ya Siriya+ inayamba kuchita nkhondo ndi Isiraeli. Chotero inakambirana ndi atumiki ake+ kuti: “Tikasonkhane pamalo akutiakuti.”+  Kenako munthu wa Mulungu woona+ uja anatumiza uthenga kwa mfumu ya Isiraeli, wakuti: “Samalani kuti musadutse pamalo akutiakuti+ chifukwa Asiriya akupita kumeneko.”+ 10  Pamenepo mfumu ya Isiraeli inatumiza anthu kumalo amene munthu wa Mulungu woona uja anaiuza.+ Elisa anachenjeza+ mfumu ya Isiraeli ndipo sinapiteko. Izi zinachitika kangapo, osati kamodzi kapena kawiri kokha. 11  Choncho mfumu ya Siriya inapsa mtima kwambiri+ chifukwa cha zimenezo, moti inaitanitsa atumiki ake ndipo inawafunsa kuti: “Ndiuzeni, ndani pakati pa ife amene ali kumbali ya mfumu ya Isiraeli?”+ 12  Ndiyeno mmodzi wa atumiki ake anati: “Palibe, mbuyanga mfumu, koma mneneri Elisa+ amene ali ku Isiraeli, ndi amene amauza+ mfumu ya Isiraeli zinthu zimene inuyo mumalankhula kuchipinda kwanu.”+ 13  Choncho mfumuyo inati: “Amuna inu pitani mukaone kumene ali, kuti nditumizeko anthu akamutenge.”+ Kenako mfumuyo inauzidwa kuti: “Ali ku Dotana.”+ 14  Nthawi yomweyo mfumuyo inatumizako mahatchi, magaleta ankhondo, ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu.+ Iwo anafikako usiku ndipo anazungulira mzindawo. 15  Mtumiki+ wa munthu wa Mulungu woona atadzuka m’mawa n’kutuluka panja, anangoona kuti gulu lankhondo lazungulira mzindawo ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo. Nthawi yomweyo mtumikiyo anadandaulira mbuye wake kuti: “Kalanga ine mbuyanga!+ Titani?” 16  Koma iye anati: “Usaope,+ popeza ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.”+ 17  Kenako Elisa anayamba kupemphera+ kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso+ chonde kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa+ linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo+ oyaka moto. 18  Asiriyawo atayamba kupita kumene kunali Elisa, iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Chonde chititsani khungu mtundu uwu.” Chotero iye anawachititsa khungu+ malinga ndi mawu a Elisa. 19  Tsopano Elisa anawauza kuti: “Njira yake si imeneyi ndipo mzinda wake si umenewu. Nditsatireni, ndikulondolerani kwa munthu amene mukufuna.” Koma anawapititsa ku Samariya.+ 20  Atangofika ku Samariya, Elisa anati: “Yehova, atseguleni maso anthuwa kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso awo ndipo anaona+ kuti ali pakatikati pa Samariya. 21  Mfumu ya Isiraeli itangoona anthuwo, inafunsa Elisa kuti: “Kodi ndiwaphe?+ Ndiwaphe kodi bambo?”+ 22  Koma Elisa anati: “Musawaphe. Kodi mukufuna kupha anthu amene mwawagonjetsa ndi lupanga ndi uta n’kuwagwira?+ Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa.+ Kenako apite kwa mbuye wawo.” 23  Chotero mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu ndipo anayamba kudya ndi kumwa. Atatha anawauza kuti azipita ndipo anapita kwa mbuye wawo. Kuchokera pamenepo, magulu a achifwamba+ a Asiriya sanabwerenso ku Isiraeli. 24  Pambuyo pake Beni-hadadi mfumu ya Siriya anasonkhanitsa asilikali ake onse ndipo anapita kukazungulira+ mzinda wa Samariya. 25  Patapita nthawi, mu Samariya+ munagwa njala yaikulu. Asiriyawo anapitirizabe kuzungulira mzindawo mpaka mtengo wogulira mutu wa bulu+ unafika pa ndalama 80 zasiliva, ndipo zitosi za nkhunda+ zodzaza manja awiri* mtengo wake unafika pa ndalama zisanu zasiliva. 26  Mfumu ya Isiraeli ikuyenda pamwamba pa khoma, mayi wina analankhula mokweza kwa mfumuyo kuti: “Ndithandizeni mbuyanga mfumu!”+ 27  Mfumuyo inayankha kuti: “Ngati Yehova sakukuthandiza ndiye ine ndingakuthandize ndi chiyani?+ Kodi ndingakuthandize ndi zochokera popunthira mbewu, mopondera mphesa, kapena moyengera mafuta?” 28  Ndiyeno mfumuyo inam’funsa kuti: “Vuto lako ndi lotani?” Mayiyo anayankha kuti: “Mayi uyu anandiuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye lero, ndipo mwana wanga timudya mawa.’+ 29  Choncho tinaphika+ mwana wanga n’kumudya.+ Tsiku lotsatira ndinauza mayiyu kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye.’ Koma iye anakam’bisa.” 30  Mfumuyo itamva mawu a mayiyo, nthawi yomweyo inang’amba+ zovala zake, ndipo pamene inali kuyendabe pamwamba pa khomalo, anthu anaona kuti inali itavala chiguduli* mkati. 31  Kenako inapitiriza kulankhula kuti: “Mulungu andilange mowirikiza, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati ukhalebe pa iye lero!”+ 32  Tsopano Elisa anali atakhala m’nyumba mwake pamodzi ndi akulu+ pamene mfumu inatumiza mthenga kwa iye. Mthengayo asanafike, Elisa anauza akuluwo kuti: “Kodi mwaona kuti mwana wa munthu wopha anthu+ uja watumiza munthu kuti adzandidule mutu? Muonetsetse kuti mthengayo akangofika mutseke chitseko ndipo muchitsamire kuti asathe kulowa. Kodi mapazi a mbuye wake si amene akumveka+ pambuyo pakewo?” 33  Elisa ali mkati molankhula nawo, mthenga uja anafika, ndipo mfumu inati: “Tsokali lachokera kwa Yehova.+ Kodi pali chifukwa choti ndipitirizire kuyembekezera Yehova?”+

Mawu a M'munsi

Zitosi za nkhunda zodzaza manja awiri zinali zokwana pafupifupi gawo limodzi la magawo atatu a lita.
Ena amati “saka.”