2 Mafumu 5:1-27

5  Tsopano munthu winawake dzina lake Namani,+ mkulu wa gulu la asilikali a mfumu ya Siriya, anakhala munthu wofunika pamaso pa mbuye wake. Iye anali wolemekezeka, chifukwa Yehova anapulumutsa Siriya+ kudzera mwa iyeyo. Munthuyo anasonyeza kuti anali wamphamvu ndi wolimba mtima, ngakhale kuti anali wakhate.  Tsopano magulu achifwamba a Asiriya+ anapita kudziko la Isiraeli komwe anakagwirako kamtsikana n’kupita nako kwawo.+ Kenako kamtsikanako kanayamba kutumikira mkazi wa Namani.  Patapita nthawi, kamtsikanako kanauza+ mbuye wake wamkazi kuti: “Mbuyanga akanapita kwa mneneri+ amene ali ku Samariya, akanam’chiritsa khate lake.”+  Pambuyo pake mbuye wake anauzidwa zimene kamtsikana ka ku Isiraeli kaja kananena.+  Ndiyeno mfumu ya Siriya inauza Namani kuti: “Nyamuka, ndikupatsa kalata upite kwa mfumu ya Isiraeli.” Choncho iye ananyamuka atatenga+ matalente* 10 a siliva, masekeli 6,000 a golide,+ ndi zovala 10.+  Kenako Namani anabweretsa kalatayo+ kwa mfumu ya Isiraeli. Kalatayo inati: “Pa nthawi imene mukulandira kalatayi, ndatumiza kwa inu mtumiki wanga Namani, kuti mum’chiritse khate lake.”  Mfumu ya Isiraeli itawerenga kalatayo, nthawi yomweyo inang’amba+ zovala zake n’kunena kuti: “Kodi ine ndine Mulungu,+ wotha kupha munthu kapena kum’siya wamoyo?+ Munthu uyu wanditumizira wodwala kuti ndim’chiritse khate lake. Taonani amuna inu kuti munthuyu akufuna kukangana nane.”+  Elisa munthu wa Mulungu woona atangomva kuti mfumu ya Isiraeli yang’amba zovala zake,+ anatumiza uthenga kwa mfumuyo, wakuti: “N’chifukwa chiyani mwang’amba zovala zanu? Muuzeni abwere kwa ine kuti adziwe kuti ku Isiraeli kuli mneneri.”+  Chotero Namani anabwera ndi mahatchi ake ndi magaleta ake ankhondo ndipo anaima pakhomo pa nyumba ya Elisa. 10  Koma Elisa anatuma mthenga kukamuuza kuti: “Pita ukasambe+ maulendo 7+ mumtsinje wa Yorodano, kuti mnofu wako ubwerere mwakale ndi kuti iweyo+ ukhale woyera.” 11  Namani atamva zimenezi anapsa mtima+ n’kunyamuka kuti azipita, ndipo anati: “Ine ndinati,+ ‘Abwera kudzaima pafupi ndi ine n’kuitana dzina la Yehova Mulungu wake. Kenako ayendetsa dzanja lake uku ndi uku pamwamba pa malo amatendawo n’kundichiritsa khate langali.’ 12  Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko+ si yabwino kuposa madzi+ onse a mu Isiraeli? Kodi sindingasambe mmenemo n’kuyeretsedwa?”+ Atatero anatembenuka n’kumapita, ali wokwiya kwambiri.+ 13  Tsopano atumiki ake anamutsatira ndipo anamufunsa kuti: “Bambo wanga,+ kodi mneneriyo akanakuuzani kuti muchite chinthu chachikulu, simukanachita? Nanga bwanji poti wangokuuzani kuti, ‘Kasambeni ndi kuyeretsedwa’?” 14  Namani atamva zimenezi, anatsetserekera ku Yorodano n’kukamira maulendo 7, mogwirizana ndi mawu a munthu wa Mulungu woona+ uja. Pambuyo pake, mnofu wake unabwerera mwakale moti unakhala ngati mnofu wa kamnyamata,+ ndipo anakhala woyera.+ 15  Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.” 16  Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira,+ sindilandira.”+ Ndiyeno Namani anayamba kum’kakamiza kuti alandire, koma iye anakanabe. 17  Pamapeto pake, Namani anati: “Ngati mukukana, chonde ine mtumiki wanu, mundipatseko dothi+ lotha kunyamulidwa ndi nyulu* ziwiri, chifukwa sindidzaperekanso nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse kwa milungu ina, koma kwa Yehova basi.+ 18  Pa nkhani yotsatirayi, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu: Ndikakalowa m’kachisi wa Rimoni+ pamodzi ndi mbuyanga, nditam’chirikiza+ mbuyangayo pomugwira dzanja pamene akugwadira+ Rimoni, ine n’kugwada nawo m’kachisi wa Rimoni, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani imeneyi.”+ 19  Elisa atamva zimenezi anamuuza kuti: “Pita mu mtendere.”+ Choncho iye anachoka ndipo anayenda kaulendo ndithu. 20  Kenako Gehazi,+ amene anali kutumikira Elisa, munthu wa Mulungu woona+ uja, ananena mumtima mwake kuti: “Mbuyanga wangomusiya Namani+ Msiriya uja osalandira zimene anabweretsa. Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndim’thamangira kuti ndikatengeko zinthu zina kwa iye.”+ 21  Ndiyeno Gehazi anathamangira Namani. Namani ataona kuti munthu akum’thamangira, nthawi yomweyo anatsika pagaleta lake kuti akumane naye. Kenako anati: “N’kwabwino?”+ 22  Gehazi anayankha kuti: “Inde n’kwabwino. Mbuyanga+ wandituma+ kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri,+ kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+ 23  Pamenepo Namani anamuuza kuti: “Chabwino. Tenga matalente awiri.” Anamuumiriza+ mpaka anam’mangira matalente awiri a siliva m’matumba awiri, ndi zovala ziwiri. Anapereka zinthuzo kwa atumiki ake awiri kuti am’nyamulire. 24  Atafika ku Ofeli, nthawi yomweyo Gehazi anawalandira katunduyo ndipo anamuika m’nyumba.+ Kenako anauza amunawo kuti azipita, ndipo iwo anapitadi. 25  Ndiyeno Gehazi anapita kukaima pafupi ndi mbuyake.+ Kenako Elisa anam’funsa kuti: “Kodi unapita kuti, Gehazi?” Iye anayankha kuti: “Ine mtumiki wanu sindinapite kulikonse.”+ 26  Pamenepo Elisa anati: “Kodi mtima wanga sunali nawe limodzi pamene munthuyo anali kutembenuka ndi kutsika pagaleta lake kuti akumane nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira siliva, zovala, minda ya maolivi, minda ya mpesa, nkhosa, ng’ombe, antchito aamuna, kapena antchito aakazi?+ 27  Tsopano khate+ la Namani limamatira iweyo ndi mbadwa zako mpaka kalekale.”*+ Nthawi yomweyo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa, atachita khate loyera kuti mbuu.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.