2 Mafumu 4:1-44

4  Mayi wina yemwe anali mmodzi wa akazi a ana+ a aneneri, anafika kwa Elisa n’kulankhula mokweza kuti: “Mtumiki wanu yemwe anali mwamuna wanga anamwalira. Inu mukudziwa bwino kuti mtumiki wanuyo anali woopa+ Yehova. Tsopano kwabwera wangongole+ kudzatenga ana anga onse awiri kuti akakhale akapolo ake.”  Ndiyeno Elisa anamuyankha kuti: “Ndiye ndikuchitire chiyani?+ Tanena, uli ndi chiyani m’nyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti: “Ine kapolo wanu ndilibe chilichonse m’nyumba mwanga, ndili ndi kamtsuko ka mafuta kokha basi.”+  Elisa anati: “Pita ukabwereke zotengera zopanda kanthu kwa anthu amene ukukhala nawo pafupi. Usakabwereke zochepa ayi.  Ukakatero, iwe ndi ana akowo mukalowe m’nyumba ndipo mukatseke chitseko. Ndiyeno uzikathira mafutawo m’zotengerazo. Zimene zadzaza uzikaziika pambali.”  Atamuuza zimenezi, mayiyo ananyamuka. Iye ndi ana ake atakadzitsekera m’nyumba, anawo an’kamuikira zotengera zija pafupi, iye n’kumathiramo mafuta.+  Zotengera zija zitadzaza, mayiyo anauza mwana wake kuti: “Bweretsa chotengera china.”+ Koma mwanayo anayankha kuti: “Palibenso chotengera china.” Pamenepo mafuta aja analeka.+  Kenako anapita kwa munthu wa Mulungu woona uja kukamuuza zomwe zinachitikazo. Munthu wa Mulungu woonayo anati: “Pita ukagulitse mafutawo ndi kubweza ngongole zako,+ ndipo ndalama zotsalazo zithandize iwe ndi ana ako.”+  Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu.+ Kumeneko kunali mayi wina wodziwika. Mayiyo anaumiriza+ Elisa kuti adye chakudya. Nthawi zonse Elisa akamadutsa, anali kupatukira kumeneko kukadya chakudya.  Patapita nthawi, mayiyo anauza mwamuna wake+ kuti: “Tsopano ndikudziwa kuti munthu amene amadzera kuno nthawi zonse uja, ndi munthu woyera wa Mulungu.+ 10  Tiyeni tim’mangire kachipinda kapadenga*+ kukhoma.* M’kachipindamo timuikire bedi, tebulo, mpando, ndi choikapo nyale,+ kuti akabwera azikhala mmenemo.”+ 11  Monga mwa nthawi zonse, tsiku lina Elisa anabwera, ndipo analowa m’kachipinda kapadengako n’kugona mmenemo. 12  Ndiyeno Elisa anauza mtumiki wake Gehazi+ kuti: “Itana mayi wachisunemu+ uja.” Choncho iye anamuitana kuti adzaime pamaso pa Elisa. 13  Ndiyeno Elisa anauza Gehazi kuti: “Muuze kuti, ‘Mwavutika ndi kutisamalira,+ kodi tingakuchitireni chiyani?+ Kodi pali chinachake choti tikakunenereni kwa mfumu,+ kapena kwa mkulu+ wa asilikali?’” Koma mayiyo anayankha kuti: “Ayi, ndilibe vuto lililonse, chifukwa ndikukhala mwamtendere pakati pa anthu a mtundu wanga.”+ 14  Elisa anati: “Ndiye timuchitire chiyani?” Gehazi anayankha kuti: “Mayiyutu alibe mwana wamwamuna,+ ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.” 15  Nthawi yomweyo Elisa anati: “Muitane.” Choncho Gehazi anamuitana ndipo mayiyo anaima pakhomo. 16  Ndiyeno Elisa anati: “Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino mudzakhala mukuyangata mwana wamwamuna.”+ Koma mayiyo atamva anati: “Iyayi mbuyanga, munthu wa Mulungu woona! Musandinamize ine kapolo wanu.” 17  Komabe, monga mmene Elisa ananenera, mayiyo anatenga pakati n’kubereka mwana wamwamuna+ nthawi ngati yomwe ija chaka chotsatira.+ 18  Mwanayo akukula, tsiku lina anapita kwa bambo ake kumunda pamodzi ndi antchito okolola, monga mwa nthawi zonse.+ 19  Kumeneko mwanayo analira kwa bambo ake kuti: “Mutu wanga ine! Mayo ine mutu wanga!”+ Kenako bambo akewo anauza wantchito wawo kuti: “M’nyamule mwanayu upite naye kwa mayi ake.”+ 20  Wantchitoyo ananyamuladi mwanayo n’kupita naye kwa mayi ake. Mayi akewo anamukhazika pamwendo mpaka masana, kenako mwanayo anamwalira.+ 21  Ndiyeno mayiyo ananyamula mwanayo n’kukamugoneka pabedi+ la munthu wa Mulungu woona+ uja. Atatero anatuluka n’kutseka chitseko. 22  Kenako anaitana mwamuna wake ndipo anmuuza kuti: “Nditumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi wamkazi. Ndikufuna ndithamangire kwa munthu wa Mulungu woona uja.”+ 23  Mwamuna wakeyo anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukufuna kupitako lero? Lero si tsiku lokhala mwezi+ kapena pasabata.” Koma mayiyo anayankha kuti: “Palibe kanthu.” 24  Ndiyeno mayiyo anakwera bulu wake wamkazi+ n’kuuza wantchito wake kuti: “Kwera bulu utsogole. Uzithamanga, usayende pang’onopang’ono chifukwa cha ine, pokhapokha ndikakuuza.” 25  Chotero mayiyo anayenda n’kukafika kwa munthu wa Mulungu woona uja paphiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu woonayo ataona mayiyo chapatali, anauza mtumiki wake Gehazi kuti:+ “Taona, mayi wachisunemu uja uyo! 26  Thamanga ukakumane naye. Ukamufunse kuti: ‘Kodi muli bwino? Mwamuna wanu ali bwanji? Nanga mwana wanu ali bwanji?’” Mayiyo anayankha kuti: “Onse ali bwino.” 27  Mayiyo atafika kwa munthu wa Mulungu woona paphiripo, nthawi yomweyo anam’gwira mapazi.+ Gehazi ataona zimenezo, anabwera pafupi kuti am’kankhe mayiyo.+ Koma munthu wa Mulungu woonayo+ anamuuza kuti: “Musiye,+ mtima wake ukum’pweteka kwambiri.+ Koma Yehova wandibisira,+ sanandiuze.” 28  Kenako mayiyo anati: “Kodi ndinakupemphani mwana mbuyanga? Kodi ine sindinanene kuti, ‘Musandipatse chiyembekezo chabodza’?”+ 29  Nthawi yomweyo Elisa anauza Gehazi+ kuti: “Kokera chovala chako m’chiuno ndipo uchimange.+ Tenga ndodo yangayi+ uzipita. Ukakumana ndi munthu aliyense panjira usamupatse moni,+ ndipo munthu akakupatsa moni, usamuyankhe. Ukaike ndodo yangayi pankhope ya mwanayo.”+ 30  Pamenepo mayi wa mwanayo anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu+ sindikusiyani.”+ Choncho Elisa ananyamuka n’kupita pamodzi ndi mayiyo. 31  Gehazi anatsogola ndipo anaika ndodo ija pankhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena chizindikiro chosonyeza kuti ali moyo.+ Chotero iye anabwerera kukakumana ndi Elisa n’kumuuza kuti: “Mwana uja sanauke.”+ 32  Kenako Elisa analowa m’nyumbamo ndipo anapeza mwana wakufayo atam’goneka pabedi lake lija.+ 33  Ndiyeno Elisa analowa m’chipindamo n’kutseka chitseko. M’chipindamo analimo awiriwiri.+ Atatero anayamba kupemphera kwa Yehova.+ 34  Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada n’kuweramira mwanayo.+ Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, manja ake anawaika pa manja a mwanayo. Anakhalabe chowerama choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kufunda. 35  Anayambanso kuyenda uku ndi uku m’nyumbamo. Atatero anapitanso kukaweramira mwanayo. Pamenepo mwanayo anayamba kuyetsemula mpaka maulendo 7, kenako anapenya.+ 36  Ndiyeno Elisa anaitana Gehazi n’kumuuza kuti: “Itana mayi wachisunemu uja.”+ Gehazi anaitana mayiyo ndipo anabweradi kwa Elisa. Elisayo anauza mayiyo kuti: “Nyamulani mwana wanu.”+ 37  Pamenepo mayiyo anapita kwa Elisa n’kugwada pamapazi ake, n’kumuweramira mpaka pansi.+ Kenako ananyamula mwana wakeyo ndipo anatuluka naye.+ 38  Pambuyo pake, Elisa anabwerera ku Giligala,+ ndipo m’dzikolo munali njala.+ Tsopano ana+ a aneneri anakhala pamaso pake.+ Patapita nthawi, iye anauza mtumiki wake kuti:+ “Teleka mphika waukulu kuti uwaphikire chakudya ana a aneneriwa.”+ 39  Choncho wina anapita kutchire kukathyola masamba,+ ndipo anapezako kamtengo koyanga, n’kuthyolapo mphonda zakutchire kudzaza pachovala chake. Atatero anabwera nazo n’kuziduladula. Kenako anazithira mumphika uja, koma iwo sankazidziwa bwinobwino. 40  Pambuyo pake anazikhuthula n’kupatsa ana a aneneriwo kuti adye. Atangoyamba kudya chakudyacho, analankhula mokweza kuti: “Inu munthu wa Mulungu woona,+ muli poizoni mumphikamu!”+ Ndipo sanathenso kudya. 41  Ndiyeno Elisa anati: “Bweretsani ufa.” Atathira ufawo mumphikamo, ananena kuti: “Apatseni anthuwa kuti adye.” Atatero, mumphikamo munalibenso chakupha chilichonse.+ 42  Ndiyeno kunabwera munthu wina kuchokera ku Baala-salisa.+ Iye anabweretsera+ munthu wa Mulungu woonayo mkate wa zipatso zoyambirira kucha,+ mitanda 20 ya mkate wa balere,+ ndi tirigu* watsopano m’thumba lake. Choncho Elisa anati: “Gawira anthuwa kuti adye.”+ 43  Koma woperekera chakudyayo anati: “Ndingagawire bwanji chakudya chimenechi anthu 100?”+ Elisa ananena kuti: “Gawira anthuwa kuti adye, pakuti Yehova wanena kuti, ‘Anthuwa adya mokwanira chakudyachi, ndipo chitsala.’”+ 44  Munthuyo atamva zimenezi, anagawira anthuwo chakudyacho. Iwo anadya mpaka chakudyacho chinatsala, mogwirizana ndi mawu a Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “kapatsindwi.”
Ena amati, “chipupa” kapena “chikupa.”
Kapena “balere.”