2 Mafumu 25:1-30

25  M’chaka cha 9+ cha ufumu wa Zedekiya, m’mwezi wa 10,+ pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ ku Yerusalemu pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo. Anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo ndipo anamanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+  Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.  M’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,+ njala+ inafika poipa kwambiri mumzindawo, ndipo anthu a m’dzikolo analibiretu chakudya.+  Ndiyeno khoma la mzindawo linabooledwa,+ ndipo amuna onse ankhondo anathawa usiku kudzera pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu.+ Akasidi+ anali atazungulira mzinda wonsewo, ndipo mfumuyo inayamba kuthawa+ kulowera cha ku Araba.+  Gulu lankhondo la Akasidi+ linayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo linaipeza+ m’chipululu cha Yeriko.+ Pamenepo gulu lonse lankhondo la mfumuyo linabalalika n’kuisiya yokha.  Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ n’kupita nayo ku Ribila+ kwa mfumu ya Babulo, kuti akaiuze chigamulo chake.  Iwo anapha ana a Zedekiya iye akuona,+ kenako Zedekiyayo anam’chititsa khungu.+ Atatero anamumanga ndi maunyolo amkuwa+ n’kupita naye ku Babulo.+  M’mwezi wachisanu, pa tsiku la 7 la mweziwo, kutanthauza m’chaka cha 19+ cha Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+  Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba zonse za mu Yerusalemu,+ ndi nyumba ya munthu aliyense wotchuka.+ 10  Kenako gulu lonse lankhondo la Akasidi, lomwe linali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, linagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+ 11  Anthu ena onse amene anatsala mumzindamo, ndi anthu amene anapita kumbali ya mfumu ya Babulo, ndiponso anthu ena onse,+ Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+ 12  Ena mwa anthu onyozeka+ a m’dzikolo, mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi alimi ogwira ntchito mokakamizidwa.+ 13  Zipilala+ zamkuwa zimene zinali m’nyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wake kupita nawo ku Babulo.+ 14  Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu, ndi ziwiya zonse+ zamkuwa zimene ansembe anali kugwiritsira ntchito potumikira. 15  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa zomwe zinali zagolide weniweni,+ komanso zomwe zinali zasiliva weniweni.+ 16  Koma panalibe njira yodziwira kulemera kwa mkuwa wa zipilala ziwiri zija, chosungiramo madzi chimodzi chija, ndi zotengera zokhala ndi mawilo zimene Solomo anapangira nyumba ya Yehova. Panalibe njira yodziwira kulemera kwa mkuwa wa ziwiya zonsezi.+ 17  Chipilala chilichonse kutalika kwake chinali mikono 18,+ ndipo mutu+ wake unali wamkuwa. Mutuwo kutalika kwake kunali mikono itatu, ndipo maukonde ndi makangaza*+ amene anazungulira mutuwo, onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa. 18  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri, ndi alonda atatu a pakhomo.+ 19  Mumzindawo anatengamo nduna imodzi ya panyumba ya mfumu imene inali kuyang’anira amuna ankhondo. Anatenganso amuna asanu kuchokera pa anthu amene ankatha kuonana ndi mfumu mwa amuna amene anali mumzindamo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe anali kusonkhanitsa ankhondo a m’dzikolo, ndi amuna 60 mwa anthu a m’dzikolo amene anali mumzindawo.+ 20  Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa+ n’kupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 21  Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo+ ku Ribila m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+ 22  Ndiyeno Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anasankha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani,+ kuti akhale mtsogoleri wa anthu+ amene anatsala m’dziko la Yuda, amene mfumuyo inawasiya mmenemo. 23  Akuluakulu onse a magulu ankhondo+ ndi asilikali awo atamva kuti mfumu ya Babulo yasankha Gedaliya, nthawi yomweyo anapita kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Akuluakuluwo anali Isimaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti Mnetofa, ndi Yaazaniya mwana wa Amaakati, pamodzi ndi asilikali awo. 24  Gedaliya analumbirira+ akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kukhala atumiki a Akasidi. Khalani m’dzikoli n’kumatumikira mfumu ya Babulo, ndipo zinthu zikuyenderani bwino.”+ 25  Tsopano m’mwezi wa 7,+ Isimaeli+ mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, anapita kwa Gedaliya pamodzi ndi amuna 10. Isimaeli anali wa m’banja lachifumu. Iye pamodzi ndi amunawo anapha Gedaliya+ ndi Ayuda ndiponso Akasidi amene anali naye pamodzi ku Mizipa.+ 26  Zitatero, anthu onse, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu ndi akuluakulu a magulu ankhondo, ananyamuka n’kupita ku Iguputo,+ chifukwa anayamba kuopa Akasidi.+ 27  M’chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 12, pa tsiku la 27 la mweziwo, chaka chimene Evili-merodaki+ mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima+ Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende. 28  Kenako anayamba kulankhula naye zinthu zabwino, ndipo anakweza* ufumu wake kuposa mafumu ena amene anali naye limodzi ku Babulo.+ 29  Yehoyakini anavula zovala zake za kundende,+ ndipo nthawi zonse anali kudya chakudya+ pamaso pa mfumuyo masiku onse a moyo wake. 30  Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya+ kuchokera kwa mfumuyo, masiku onse a moyo wake.

Mawu a M'munsi

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Kapena kuti “anaika mpando wake wachifumu pamwamba.”