2 Mafumu 23:1-37

23  Kenako mfumuyo inatumiza uthenga kwa akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasonkhana kwa mfumuyo.+  Ndiyeno mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova pamodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu onse okhala ku Yerusalemu, ansembe,+ aneneri, ndi anthu onse kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu.+ Tsopano mfumuyo inayamba kuwawerengera+ mawu onse a m’buku+ la pangano+ limene linapezeka m’nyumba ya Yehova.+  Mfumuyo inaimirira pafupi ndi chipilala+ ndipo inachita pangano+ pamaso pa Yehova, kuti adzatsatira+ Yehova ndi kusunga malamulo ake+ ndi maumboni* ake.+ Adzachita zimenezi ndi mtima wonse+ ndi moyo wonse,+ mwa kutsatira mawu a pangano olembedwa m’bukulo.+ Choncho anthu onsewo anavomereza panganolo.+  Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ansembe ena, ndi alonda a pakhomo+ kuti atulutse m’kachisi wa Yehova ziwiya zonse zimene anapangira Baala,+ mzati wopatulika,+ ndi khamu lonse la zinthu zakuthambo.+ Itatero, inakazitentha kunja kwa Yerusalemu pamalo otsetsereka a ku Kidironi,+ ndipo inabweretsa phulusa lake ku Beteli.+  Mfumuyo inachotsa ntchito ansembe a milungu yachilendo, amene mafumu a Yuda anawaika kuti azifukiza nsembe yautsi pamalo okwezeka m’mizinda ya Yuda ndi malo ozungulira Yerusalemu. Inachotsanso ntchito ansembe ofukiza nsembe yautsi kwa Baala,+ kwa dzuwa, kwa mwezi, kwa magulu a nyenyezi, ndi kwa khamu lonse la zinthu zakuthambo.+  Kuwonjezera apo, mfumuyo inatulutsa mzati wopatulika+ umene unali m’nyumba ya Yehova, ndipo inapita nawo kuchigwa* cha Kidironi kunja kwa mzinda wa Yerusalemu n’kukautentha+ kuchigwacho. Itatero, inauperapera n’kuwaza fumbi lake pamanda+ a ana a anthu.  Inagwetsanso nyumba za mahule achimuna a pakachisi+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, mmene akazi anali kulukiramo akachisi a mahema a mzati wopatulika.  Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera m’mizinda ya Yuda. Inawaitanitsa kuti isandutse malo okwezeka kukhala osayenera kulambirako, kumene ansembewo ankafukizako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba.+ Inagwetsa malo okwezeka a pazipata amene anali pakhomo la pachipata cha Yoswa mkulu wa mzindawo. Chipata cha Yoswacho chinali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pachipata cha mzindawo.  Koma ansembe+ a malo okwezekawo sankabwera kuguwa lansembe la Yehova ku Yerusalemu. M’malomwake, ankadya mikate yopanda chofufumitsa+ pakati pa abale awo. 10  Mfumuyo inachititsa kuti ku Tofeti,+ m’chigwa cha ana a Hinomu+ kukhale kosayenera kulambirako, kuti munthu aliyense asawotcheko* mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi pamoto,+ pomupereka kwa Moleki.+ 11  Komanso inachititsa kuti mahatchi amene mafumu a Yuda anawapereka kwa dzuwa, asiye kulowa m’nyumba ya Yehova kudzera m’chipinda chodyera+ cha Natani-meleki, nduna ya panyumba ya mfumu, chimene chinali pakhonde. Nawonso magaleta a dzuwa+ inawatentha pamoto. 12  Kenako mfumuyo inagumula maguwa ansembe amene anali padenga la chipinda chapadenga+ cha Ahazi, amene mafumu a Yuda anamanga. Inagumulanso maguwa ansembe+ amene Manase anamanga pamabwalo awiri a nyumba ya Yehova. Itatero, inawaperapera komweko ndipo fumbi lake inakaliwaza kuchigwa* cha Kidironi. 13  Malo okwezeka amene anali kutsogolo+ kwa Yerusalemu kudzanja lamanja* la Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo+ mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti+ chonyansa cha Asidoni, Kemosi+ chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu+ chonyansa cha ana a Amoni, mfumuyo inawasandutsa osayenera kulambirako. 14  Inaphwanyaphwanya+ zipilala zopatulika ndipo inagwetsanso mizati yopatulika. Pamalo pamene panali zimenezi inadzazapo mafupa a anthu. 15  Komanso guwa lansembe limene linali ku Beteli+ ndi malo okwezeka amene Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa Isiraeli+ anamanga, ngakhale guwa lansembe limenelo ndi malo okwezekawo, mfumuyo inagumula. Kenako inatentha malo okwezekawo n’kuwaperapera mpaka kusanduka fumbi. Inatenthanso mzati wopatulika. 16  Yosiya atatembenuka, anaona manda amene anali m’phirimo. Choncho anatumiza anthu kuti akatenge mafupa m’mandawo, ndipo anawatentha+ paguwa lansembelo kuti alisandutse losayenera kulambirapo, mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene munthu wa Mulungu woona uja, amene analengeza+ zinthu zimenezi, ananena. 17  Kenako iye anati: “Kodi chipilala chimene ndikuchiona apocho n’cha chiyani?” Pamenepo amuna a mumzindawo anamuyankha kuti: “Ndi manda+ a munthu wa Mulungu woona amene anachokera ku Yuda,+ n’kulengeza zinthu zotsutsa guwa lansembe la ku Beteli, zimene mwachita inuzi.”+ 18  Choncho iye anati: “Musiyeni apume.+ Musalole aliyense kudodometsa mafupa ake.” Chotero iwo sanakhudze mafupa akewo limodzi ndi mafupa a mneneri+ amene anachokera ku Samariya. 19  Yosiya anachotsanso akachisi onse+ a m’malo okwezeka amene anali m’mizinda+ ya ku Samariya, amene mafumu+ a Isiraeli anamanga kuti akwiyitse Mulungu.+ Iye anawachitira zofanana ndi zonse zimene anachita ku Beteli.+ 20  Chotero iye anapha ansembe onse+ a m’malo okwezeka n’kuwapereka nsembe pamaguwa ansembe kumeneko. Kenako anawotcha mafupa a anthu pamaguwa ansembewo.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu. 21  Tsopano mfumuyo inalamula anthu onse kuti: “Chitirani pasika+ Yehova Mulungu wanu, malinga ndi zimene zalembedwa m’buku la panganoli.”+ 22  Pakuti pasika ngati ameneyu anali asanachitikepo kuyambira masiku a oweruza amene anaweruza Isiraeli,+ ngakhalenso masiku onse a mafumu a Isiraeli ndi mafumu a Yuda.+ 23  Koma m’chaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, iwo anachitira Yehova pasika ameneyu ku Yerusalemu.+ 24  Yosiya anachotsanso anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera+ zam’tsogolo. Anachotsanso aterafi,*+ mafano onyansa,+ ndi zonyansa+ zonse zimene zinali m’dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu, kuti atsatire mawu a chilamulo+ amene analembedwa m’buku+ limene wansembe Hilikiya analipeza panyumba ya Yehova.+ 25  Panalibenso mfumu ina iye asanakhale mfumu imene inabwerera+ kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse,+ ndi mphamvu zake zonse, mogwirizana ndi chilamulo chonse cha Mose. Ngakhale pambuyo pake sipanakhalenso mfumu ina ngati iyeyo. 26  Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene unayakira Yuda,+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anawachititsa, n’kukwiyitsa nazo Mulungu.+ 27  Koma Yehova anati: “Yuda+ nayenso ndim’chotsa pamaso panga+ monga mmene ndinachotsera Isiraeli,+ ndipo ndithu ndidzakana ngakhale mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala pamenepo.’”+ 28  Nkhani zina zokhudza Yosiya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 29  M’masiku ake, Farao Neko+ mfumu ya Iguputo inabwera kudzathandiza mfumu ya Asuri pamtsinje wa Firate,+ ndipo Mfumu Yosiya inapita kukamenyana ndi mfumu ya Iguputoyo,+ koma mfumuyo inapha Yosiya+ ku Megido+ itangomuona. 30  Choncho atumiki ake ananyamula mtembo wake pagaleta kuchokera ku Megido n’kupita nawo ku Yerusalemu+ kumene anakauika m’manda ake. Kenako anthu a m’dzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya n’kumudzoza ndi kumulonga ufumu m’malo mwa bambo ake. 31  Yehoahazi anali ndi zaka 23+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina, ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 32  Iye anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake akale anachita.+ 33  Kenako Farao Neko+ anamanga+ Yehoahazi ku Ribila+ m’dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Ndiyeno Farao Neko analamula+ dzikolo kuti lim’patse matalente 100 a siliva+ ndi talente imodzi ya golide.+ 34  Kuwonjezera apo, Farao Neko anaika Eliyakimu+ mwana wa Yosiya kukhala mfumu m’malo mwa Yosiya bambo ake, n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Atatero anatenga Yehoahazi n’kupita naye ku Iguputo, kumene anakafa pamapeto pake.+ 35  Yehoyakimu anapereka siliva+ ndi golide kwa Farao. Koma ankakhometsa msonkho+ anthu a m’dzikolo kuti apereke silivayo kwa Farao, monga mmene anamulamulira. Iye anatenga siliva ndi golide kwa anthuwo kuti apereke kwa Farao Neko, malinga ndi msonkho umene munthu aliyense+ ankayenera kupereka. 36  Yehoyakimu anali ndi zaka 25+ pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Ruma, ndipo dzina lawo linali Zebida mwana wa Pedaya. 37  Iye anapitiriza kuchita zoipa+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake anachita.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “zikumbutso.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Mawu ake enieni, “Asadutsitse pamoto.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Kutanthauza kum’mwera, munthu akayang’ana kum’mawa.
Kutanthauza phiri la Maolivi, makamaka mbali ya kumadzulo kwenikweni, yomwe imatchedwanso kuti phiri la Chokwiyitsa.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.