2 Mafumu 22:1-20

22  Yosiya+ anali ndi zaka 8 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya.  Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda m’njira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.+  M’chaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, mfumuyo inatuma Safani+ mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu yemwe anali mlembi, kuti apite kunyumba ya Yehova. Inam’tuma ndi mawu akuti:  “Pita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe,+ ukamuuze kuti asonkhanitse pamodzi ndalama zonse+ zimene zikubwera kunyumba ya Yehova,+ zimene alonda a pakhomo+ atolera kwa anthu.  Azipereke kwa ogwira ntchito+ osankhidwa a m’nyumba ya Yehova, kuti akazipereke kwa amene akugwira ntchitoyo m’nyumba ya Yehova, kuti amate ming’alu ya nyumbayo.+  Aziperekenso kwa amisiri, kwa omanga nyumba, ndi kwa amisiri omanga ndi miyala, komanso agulire matabwa ndi miyala yosema kuti akonzere nyumbayo.+  Koma anthu amene akupatsidwa ndalamawo asafunsidwe mmene ayendetsera ndalamazo,+ chifukwa akugwira ntchito mokhulupirika.”+  Kenako Hilikiya+ mkulu wa ansembe anauza Safani+ mlembi+ kuti: “Ndapeza buku la chilamulo+ m’nyumba ya Yehova!” Choncho Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani, ndipo iye anayamba kuliwerenga.  Tsopano Safani mlembi anapita kwa mfumu n’kuiuza kuti: “Atumiki anu akhuthula ndalama zimene anazipeza m’nyumbayo, ndipo akuzipereka kwa ogwira ntchito osankhidwa a m’nyumba ya Yehova.”+ 10  Kenako Safani mlembi anauza mfumuyo kuti: “Pali buku+ limene wansembe Hilikiya wandipatsa.” Ndiyeno Safani anayamba kuwerenga bukulo pamaso pa mfumu. 11  Mfumuyo itangomva mawu a m’buku la chilamulolo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.+ 12  Kenako mfumuyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi, ndi Asaya+ mtumiki wa mfumu, kuti: 13  “Pitani mukafunse+ kwa Yehova m’malo mwa ineyo, m’malo mwa anthuwa, ndi m’malo mwa Yuda yense. Mukafunse zokhudza mawu a m’buku limene lapezekali, chifukwa mkwiyo wa Yehova+ umene watiyakira ndi waukulu, popeza makolo+ athu sanamvere mawu a m’buku ili. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”+ 14  Chotero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani, ndi Asaya anapita kukalankhula ndi Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe anali wosamalira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi,+ ndipo Hulidayo anali kukhala kumbali yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 15  Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Amuna inu, kauzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti: 16  “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka+ pamalo ano ndi anthu ake,+ kukwaniritsa mawu onse+ a m’buku limene mfumu ya Yuda yawerenga,+ 17  chifukwa chakuti andisiya n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho mkwiyo wanga wayakira malo ano ndipo suzimitsidwa.’”’+ 18  Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ponena za mawu amene wamvawo,+ 19  chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Yehova utamva zimene ndanena zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chodabwitsa ndi temberero,+ unang’amba+ zovala zako n’kuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva,” ndiwo mawu a Yehova.+ 20  “N’chifukwa chake ndidzakugoneka+ pamodzi ndi makolo ako, ndipo ndithu udzaikidwa m’manda ako mu mtendere.+ Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndikulibweretsa pamalo ano.”’” Choncho iwo anabweretsa mawuwo kwa mfumuyo.

Mawu a M'munsi