2 Mafumu 18:1-37

18  M’chaka chachitatu cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Hezekiya+ mwana wa Ahazi,+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu.  Hezekiya anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abi mwana wa Zekariya.+  Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Davide kholo lake anachita.+  Hezekiya ndiye anachotsa malo okwezeka,+ kugwetsa zipilala zopatulika,+ ndi kudula mzati wopatulika.+ Iye anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa+ imene Mose anapanga,+ chifukwa pofika masiku amenewo, ana a Isiraeli anakhala akufukiza nsembe+ yautsi kwa njoka yamkuwayo, ndipo inkatchedwa fano la njoka yamkuwa.+  Iye anadalira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ Panalibenso mfumu ina yofanana naye pamafumu onse a Yuda+ amene anakhalapo iye asanakhale mfumu, ngakhalenso amene anakhalapo iye atafa.+  Hezekiya anapitiriza kumamatira Yehova.+ Sanasiye kum’tsatira, koma anapitiriza kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose.+  Yehova anakhala naye,+ ndipo kulikonse kumene ankapita anali kuchita zinthu mwanzeru.+ Anapandukira mfumu ya Asuri n’kukana kuitumikira.+  Iye ndiye anapha Afilisiti+ mpaka ku Gaza+ ndi kumadera ake, kuyambira kunsanja ya alonda+ mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.  Tsopano m’chaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, kutanthauza chaka cha 7 cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Salimanesere+ mfumu ya Asuri anabwera ku Samariya n’kuzungulira mzindawo.+ 10  Pamapeto pa zaka zitatu, Asuriwo analanda mzindawo.+ Anaulanda m’chaka cha 6 cha Hezekiya, kutanthauza chaka cha 9 cha Hoshiya mfumu ya Isiraeli. Chotero Samariya analandidwa.+ 11  Pambuyo pake mfumu ya Asuri+ inatenga Aisiraeli n’kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala,+ ndi ku Habori+ pafupi ndi mtsinje wa Gozani, ndiponso m’mizinda ya Amedi.+ 12  Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeliwo sanamvere+ mawu a Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake,+ ngakhalenso zonse zimene Mose+ mtumiki wa Yehova anawalamula.+ Iwo sanamvere kapena kuzichita. 13  M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo. 14  Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Ndachimwa. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.”+ Chotero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente* 300 a siliva+ ndi matalente 30 a golide. 15  Ndiyeno Hezekiya anapereka siliva yense amene anali panyumba ya Yehova,+ ndiponso amene anali pa chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ 16  Pamenepo Hezekiya mfumu ya Yuda anachotsa zitseko za kachisi wa Yehova+ ndi mafelemu ake, zimene iye anazikuta+ ndi golide, n’kupereka golideyo kwa mfumu ya Asuri. 17  Kenako mfumu ya Asuri+ inatuma Tatani,*+ Rabisarisi,* ndi Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inawatumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iwo anapitadi n’kukaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 18  Kenako anayamba kuitana mfumu mofuula, ndipo kunabwera Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika. 19  Choncho Rabisake+ anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+ 20  Iwe wanena kuti (koma ndi mawu a pakamwa chabe), ‘Ine ndili ndi nzeru+ ndi mphamvu zofunika pankhondo.’ Kodi ukudalira ndani popandukira+ ine? 21  Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika+ loti munthu ataligwira kuti limuchirikize, lingamucheke m’manja. Umu ndi mmene Farao+ mfumu ya Iguputo alili kwa onse omudalira. 22  Ngati amuna inu mungandiuze kuti, ‘Tikudalira+ Yehova Mulungu wathu,’+ kodi si iye amene Hezekiya+ wam’chotsera malo ake okwezeka+ ndi maguwa ake ansembe, n’kuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada patsogolo pa guwa lansembe ili, la ku Yerusalemu’?”’+ 23  Tsopano ubetcherane+ ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti ndione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.+ 24  Kodi ungathe bwanji kubweza bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga,+ pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta+ ndi okwera pamahatchi?+ 25  Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza+ kuti, ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo, ndipo ukaliwononge.’” 26  Pamenepo Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya, Sebina,+ ndi Yowa+ anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu m’chilankhulo cha Asiriya+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe m’chilankhulo cha Ayuda,+ kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.” 27  Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene mawuwa kwa mbuye wanu yekha ndi kwa inuyo? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, kuti adye chimbudzi chawo+ ndi kumwa mkodzo wawo limodzi nanu?”+ 28  Choncho Rabisake akadali chiimire, anapitiriza kulankhula mokweza m’chilankhulo cha Ayuda,+ ndipo anati: “Imvani mawu a mfumu yaikulu,+ mfumu ya Asuri. 29  Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni anthu inu, chifukwa sangathe kukulanditsani m’manja mwanga.+ 30  Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Mosakayikira Yehova atilanditsa,+ ndipo mzindawu superekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 31  Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Ndigonjereni, ndipo bwerani kwa ine. Aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu,+ komanso aliyense azimwa madzi a m’chitsime chake,+ 32  kufikira ine nditabwera kudzakutengerani kudziko lofanana ndi dziko lanulo+ kuti mukhalebe ndi moyo osafa. Ndidzakutengerani kudziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate+ ndi minda ya mpesa,+ dziko la mitengo ya maolivi a mafuta ndiponso la uchi.+ Musamvere Hezekiya chifukwa akukunyengererani ndi mawu akuti, ‘Yehova atilanditsa.’+ 33  Kodi pali mulungu wa mitundu ina amene wakwanitsa kupulumutsa+ mtundu wake m’manja mwa mfumu ya Asuri?+ 34  Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu,+ Hena,+ ndi Iva?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+ 35  Ndi mulungu uti pakati pa milungu yonse ya mayiko, amene walanditsa dziko lake m’manja mwanga,+ kuti Yehova athe kulanditsa Yerusalemu m’manja mwanga?”’”+ 36  Anthuwo anangokhala chete+ osamuyankha,+ chifukwa lamulo lochokera kwa mfumu linali lakuti: “Musamuyankhe.”+ 37  Koma Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyang’anira banja lachifumu, Sebina+ mlembi, ndi Yowa+ mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atang’amba zovala zawo+ n’kumuuza mawu a Rabisake.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Kapena kuti “mkulu wa asilikali.”
Kapena kuti “mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu.”
Kapena kuti “mkulu wa operekera chikho.”