2 Mafumu 17:1-41

17  M’chaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoshiya+ mwana wa Ela anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya+ kwa zaka 9.  Hoshiya anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, koma osati ngati mmene anachitira mafumu a Isiraeli amene anakhalapo iye asanakhale.+  Iye ndiye amene Salimanesere+ mfumu ya Asuri+ anabwera kudzamuthira nkhondo. Chotero Hoshiya anakhala mtumiki wake n’kuyamba kupereka msonkho+ kwa iye.  Koma mfumu ya Asuri inaona kuti Hoshiya anali kuichitira chiwembu,+ chifukwa chakuti iye anatumiza amithenga kwa So mfumu ya Iguputo,+ ndiponso sanapereke msonkho kwa mfumu ya Asuri monga anali kuchitira zaka zam’mbuyo. Choncho mfumu ya Asuri inam’manga n’kumutsekera m’ndende.+  Ndiyeno mfumu ya Asuri inabwera kudzachita nkhondo ndi dziko lonselo, kenako inazungulira mzinda wa Samariya+ kwa zaka zitatu.  M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+  Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ana a Isiraeli anachimwira+ Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa m’dziko la Iguputo+ n’kuwachotsa m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, ndipo anayamba kuopa milungu ina.+  Iwo anapitiriza kuyenda motsatira malamulo+ a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, ndiponso motsatira malamulo amene mafumu a Isiraeli anapanga okha.  Ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo,+ ndipo anapitiriza kumanga malo okwezeka+ m’mizinda yawo yonse, kuyambira kunsanja+ ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. 10  Iwo anapitiriza kudziikira zipilala zopatulika+ ndi mizati yopatulika+ paphiri lililonse lalitali,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 11  Pamalo okwezeka onsewo, iwo anapitiriza kufukizapo nsembe yautsi, mofanana ndi mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa m’dzikolo chifukwa cha Aisiraeliwo. Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa zokwiyitsa+ Yehova. 12  Anapitiriza kutumikira mafano onyansa.*+ Ponena za mafano amenewa, Yehova anawauza kuti: “Musachite zimenezi.”+ 13  Yehova anali kuchenjeza+ Aisiraeli+ ndi Ayuda+ kudzera mwa aneneri ake onse+ ndi wamasomphenya aliyense,+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo sungani malamulo anga,+ mogwirizana ndi chilamulo chonse+ chimene ndinalamula makolo anu,+ ndi chimene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”+ 14  Koma iwo sanamvere. M’malomwake anaumitsa makosi awo,+ ngati mmene makolo awo anaumitsira makosi awo. Makolo awowo sanasonyeze chikhulupiriro+ mwa Yehova Mulungu wawo. 15  Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anapangana ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso+ zimene iye anali kuwachenjeza nazo. M’malomwake anayamba kutsatira mafano opanda pake+ ndipo iwowo nawonso anakhala opanda pake.+ Anatsatira mitundu imene inawazungulira, imene Yehova anawalamula kuti asamachite zofanana nayo.+ 16  Anasiya malamulo onse+ a Yehova Mulungu wawo n’kudzipangira zifaniziro ziwiri za ana a ng’ombe,+ zopangidwa ndi zitsulo zosungunula,+ komanso mzati wopatulika.+ Anayamba kugwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kutumikira Baala.+ 17  Iwo anapitiriza kuwotcha* pamoto+ ana awo aamuna ndi aakazi, kulosera+ ndi kuwombeza.*+ Anapitirizanso+ kuchita zoipa* pamaso pa Yehova ndi cholinga chomukwiyitsa.+ 18  Chotero Yehova anawakwiyira kwambiri+ Aisiraeli ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Sanasiye aliyense kupatulapo fuko la Yuda lokha.+ 19  Komabe, nawonso Ayudawo sanasunge malamulo a Yehova Mulungu+ wawo, koma anayenda motsatira malamulo amene Aisiraeli+ anapanga. 20  Chotero Yehova anakana mbewu yonse+ ya Isiraeli ndipo anawasautsa n’kuwapereka m’manja mwa olanda katundu, mpaka iye anawathamangitsa pamaso pake.+ 21  Anang’amba Isiraeli kumuchotsa kunyumba ya Davide ndipo iwo analonga ufumu Yerobowamu mwana wa Nebati.+ Yerobowamuyo anasiyitsa Aisiraeli kutsatira Yehova n’kuwachimwitsa ndi tchimo lalikulu.+ 22  Ana a Isiraeli anapitiriza kuyenda m’machimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye, 23  mpaka Yehova anachotsa Isiraeli pamaso pake+ monga momwe ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Isiraeli anachoka m’dziko lake n’kupita ku Asuri, ndipo ali komweko mpaka lero.+ 24  Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo,+ Kuta, Ava,+ Hamati,+ ndi Sefaravaimu+ n’kuwakhazika m’mizinda ya Samariya,+ m’malo mwa ana a Isiraeli. Anthuwo anatenga Samariya n’kumakhala m’mizinda yake. 25  Atayamba kukhala mmenemo, iwo sanaope+ Yehova. Choncho Yehova anatumiza mikango+ pakati pawo ndipo inapha ena a iwo. 26  Chotero mfumu ya Asuri inalandira uthenga wakuti: “Mitundu imene munaichotsa kwawo n’kukaikhazika m’mizinda ya ku Samariya, sikudziwa chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo, moti iye wakhala akutumiza mikango pakati pawo+ imene ikuwapha, popeza palibe amene akudziwa chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo.” 27  Pamenepo mfumu ya Asuri inalamula kuti: “Mutumize wansembe mmodzi+ mwa anthu amene munawagwira. Mumutumize kuchokera kumeneko, kuti apite kukakhala m’dzikolo n’kukaphunzitsa anthuwo chipembedzo cha Mulungu wa m’dzikolo.” 28  Choncho mmodzi mwa ansembe amene anatengedwa kuchokera ku Samariya, anabwera n’kuyamba kukhala ku Beteli.+ Iye anakhala mphunzitsi pakati pawo wowaphunzitsa mmene angaopere Yehova.+ 29  Koma mtundu uliwonse unapanga mulungu wake+ n’kukamuika m’kachisi m’malo okwezeka amene Asamariya anamanga. Mtundu uliwonse unachita zimenezi m’mizinda imene unali kukhala. 30  Anthu a ku Babulo anapanga Sukoti-benoti, a ku Kuta+ anapanga Nerigali, ndipo a ku Hamati anapanga Asima. 31  Aava+ anapanga Nibazi ndi Tarataka, pamene Asefaravaimu+ anali kuwotcha ana awo aamuna pamoto+ powapereka nsembe kwa Adarameleki ndi Anameleki, milungu ya Sefaravaimu. 32  Anthuwo ankaopa Yehova, koma anatenga anthu wamba a mitundu yawo n’kuwasandutsa ansembe+ a malo okwezeka, kuti aziwatumikira m’kachisi wa m’malo okwezeka. 33  Ankaopa Yehova+ koma ankalambira milungu yawo,+ mogwirizana ndi chipembedzo cha mitundu imene anawatengako.+ 34  Mpaka lero akutsatirabe zipembedzo zawo zakale.+ Palibe amene ankaopa Yehova+ ndipo palibe amene ankatsatira malamulo ake, zigamulo zake,+ ndi chilamulo+ chimene Yehova analamula ana a Yakobo.+ Yakoboyo Mulungu anamusintha dzina n’kumutcha Isiraeli,+ 35  pamene Yehova anachita nawo pangano+ n’kuwalamula kuti: “Musamaope milungu ina.+ Musamaigwadire kapena kuitumikira kapenanso kupereka nsembe kwa iyo.+ 36  Koma Yehova amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi mphamvu zazikulu, ndi dzanja lotambasula,+ ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene muyenera kumugwadira+ ndi kupereka nsembe kwa iye.+ 37  Muonetsetse kuti nthawi zonse mukutsatira+ malamulo,+ zigamulo,+ ndi chilamulo chimene anakulemberani,+ ndipo musamaope milungu ina. 38  Musaiwale pangano limene ndapangana nanu,+ ndipo musamaope milungu ina.+ 39  Koma muziopa Yehova+ Mulungu wanu, popeza iye ndi amene adzakupulumutseni m’manja mwa adani anu onse.”+ 40  Koma iwo sanamvere. M’malomwake ankachita zinthu motsatira chipembedzo chawo chakale.+ 41  Mitundu imeneyi inali kuopa Yehova,+ koma inali kutumikira zifaniziro zawo zogoba. Mpaka lero, ana awo ndi zidzukulu zawo akuchitabe mmene makolo awo ankachitira.

Mawu a M'munsi

Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”
Mawu ake enieni, “Kudutsitsa pamoto.”
Mawu akuti “kuwombeza” akutanthauza kufuna kudziwa zam’tsogolo, kapena kufufuza ngati zochitika kapena zinthu zinazake zikulosera kuti m’tsogolo mudzachitika zabwino kapena zoipa.
Kapena kuti “anatsimikiza mtima kuti achite zinthu zoipa.”