2 Mafumu 15:1-38

15  M’chaka cha 27 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Azariya*+ mwana wa Amaziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu.  Azariya anayamba kulamulira ali ndi zaka 16, ndipo analamulira ku Yerusalemu+ zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu, ndipo dzina lawo linali Yekoliya.  Azariya anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Amaziya bambo ake anachita.+  Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+  Pomaliza pake, Yehova anaichititsa khate mfumuyo+ moti inakhalabe yakhate+ mpaka tsiku limene inamwalira. Iyo inali kungokhala m’nyumba mwake osagwiranso ntchito.+ Pa nthawiyi, Yotamu+ mwana wa mfumuyo ndiye anali kuyang’anira nyumba ya mfumu ndi kuweruza+ anthu a m’dzikolo.  Nkhani zina zokhudza Azariya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.  Pambuyo pake, Azariya anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anamuika m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Kenako Yotamu mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.+  M’chaka cha 38 cha Azariya+ mfumu ya Yuda, Zekariya+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa miyezi 6.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova monga anachitira makolo ake.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 10  Ndiyeno Salumu mwana wa Yabesi anam’chitira chiwembu+ Zekariya n’kumupha+ ku Ibuleamu,+ ndipo iye anayamba kulamulira m’malo mwake. 11  Nkhani zina zokhudza Zekariya, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 12  Izi zinakwaniritsa mawu a Yehova+ amene anawalankhula kwa Yehu, akuti:+ “Ana+ ako aamuna adzakhala pampando wachifumu wa Isiraeli mpaka m’badwo wachinayi.” Ndipo zinaterodi.+ 13  Salumu mwana wa Yabesi, anakhala mfumu m’chaka cha 39 cha Uziya+ mfumu ya Yuda. Iye analamulira ku Samariya kwa mwezi umodzi wathunthu.+ 14  Ndiyeno Menahemu+ mwana wa Gadai, anachoka ku Tiriza+ kubwera ku Samariya n’kudzapha Salumu+ mwana wa Yabesi ku Samariyako. Kenako iye anayamba kulamulira m’malo mwake. 15  Nkhani zina zokhudza Salumu ndi chiwembu+ chimene anachita, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 16  Panali pa nthawi imeneyi pamene Menahemu anachoka ku Tiriza n’kupita kukaukira mzinda wa Tifisa, n’kupha anthu onse amene anali mmenemo. Anawononganso dera lozungulira mzindawo chifukwa anthu ake sanamutsegulire chipata, ndipo akazi onse apakati a mumzindawo anawatumbula.+ 17  M’chaka cha 39+ cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadai anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 10. 18  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Masiku ake onse, sanasiye machimo onse a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 19  Tsopano Puli+ mfumu ya Asuri+ inabwera m’dzikomo. Choncho Menahemu anapatsa+ Puli matalente* 1,000 a siliva,+ kuti amuthandize kulimbitsa ufumu umene unali m’manja mwake.+ 20  Menahemu anatenga ndalama zasilivazo kwa Aisiraeli. Iye anatenga masekeli* 50 a siliva kwa mwamuna aliyense wachuma,+ ndipo anawapereka kwa mfumu ya Asuri. Pamenepo mfumu ya Asuri inabwerera ndipo sinakhale m’dzikomo. 21  Nkhani zina zokhudza Menahemu+ ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 22  Pomalizira pake Menahemu anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo Pekahiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 23  M’chaka cha 50 cha Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya+ kwa zaka ziwiri. 24  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 25  Kenako Peka+ mwana wa Remaliya, yemwe anali msilikali wake wom’thandiza pagaleta,+ anam’konzera chiwembu+ n’kumupha ku Samariya. Iye anapha mfumuyo ali limodzi ndi Arigobi ndi Ariye ndiponso amuna 50 a ku Giliyadi. Anaiphera munsanja yokhalamo ya panyumba ya mfumu,+ n’kuyamba kulamulira m’malo mwake. 26  Nkhani zina zokhudza Pekahiya ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 27  M’chaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka+ mwana wa Remaliya+ anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 20. 28  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 29  M’masiku a Peka mfumu ya Isiraeli, Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri+ inabwera n’kulanda Iyoni,+ Abele-beti-maaka,+ Yanoa, Kedesi,+ Hazori,+ Giliyadi,+ ndi Galileya,+ dziko lonse la Nafitali.+ Inatenga anthu a m’madera amenewa n’kupita nawo ku Asuri.+ 30  Pamapeto pake, Hoshiya+ mwana wa Ela anakonzera chiwembu+ Peka mwana wa Remaliya n’kumupha.+ Kenako iye anayamba kulamulira m’malo mwake m’chaka cha 20 cha Yotamu+ mwana wa Uziya. 31  Nkhani zina zokhudza Peka ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 32  M’chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, Yotamu+ mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 33  Yotamu anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 34  Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Uziya bambo ake anachita.+ 35  Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo. Iye ndiye anamanga chipata chakumtunda cha nyumba ya Yehova.+ 36  Nkhani zina zokhudza Yotamu ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.+ 37  M’masiku amenewo Yehova anayamba kutumiza+ Rezini+ mfumu ya Siriya, ndi Peka+ mwana wa Remaliya kuti akalimbane ndi Yuda. 38  Pomalizira pake, Yotamu anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake. Kenako Ahazi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Azariya amatchedwanso Uziya.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.