2 Mafumu 14:1-29

14  M’chaka chachiwiri cha Yehoasi mwana wa Yehoahazi+ mfumu ya Isiraeli, Amaziya+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, anakhala mfumu.  Amaziya anali ndi zaka 25 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadini.+  Iye anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova,+ koma osati ngati Davide kholo lake.+ Anachita mogwirizana ndi zonse zimene Yehoasi bambo ake anachita.+  Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+  Ndiyeno ufumuwo utangokhazikika m’manja mwake, iye anayamba kupha+ atumiki ake amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+  Koma ana a anthu akuphawo sanawaphe, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku la chilamulo cha Mose chimene Yehova analamula. Iye analamula kuti:+ “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo. Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+  Amaziya anapha Aedomu+ okwana 10,000 m’chigwa cha Mchere+ n’kulanda mzinda wa Sela pankhondo. Kenako mzindawo anayamba kuutcha Yokiteeli ndipo dzina lake ndi lomweli mpaka lero.  Tsopano Amaziya anatumiza amithenga kwa Yehoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Isiraeli, ndi uthenga wakuti: “Bwera tidzamenyane.”+  Yehoasi mfumu ya Isiraeli itamva inamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza+ wa ku Lebanoni, wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija.+ 10  Chifukwa chakuti iweyo wagonjetsa+ Edomu, mtima wako wayamba kudzikuza.+ Sangalala ndi ulemu umene wapeza+ ndipo khala m’nyumba mwako momwemo. N’chifukwa chiyani ukufuna kumenya nkhondo+ pamene zinthu sizikukuyendera bwino?+ Iweyo ndi Ayuda amene uli nawowo mugonja.” 11  Koma Amaziya sanamvere.+ Chotero Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anabwera, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anamenyana+ ku Beti-semesi+ m’dziko la Yuda. 12  Pankhondoyo, Ayuda anagonja pamaso pa Aisiraeli+ moti aliyense anathawira kuhema wake. 13  Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi mwana wa Ahaziya ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya n’kupita naye ku Yerusalemu, ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efuraimu+ mpaka kukafika pa Chipata cha Pakona.+ Anagumula mpata waukulu mikono 400.* 14  Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense, ndi ziwiya zonse zimene anazipeza panyumba ya Yehova+ ndi m’nyumba yosungiramo chuma cha mfumu. Anagwiranso anthu ena n’kubwerera ku Samariya. 15  Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zimene anachita, ndiponso zochita zake zamphamvu, komanso mmene anamenyanirana ndi Amaziya mfumu ya Yuda, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 16  Pomalizira pake, Yehoasi anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda ku Samariya+ pamodzi ndi mafumu a Isiraeli. Kenako Yerobowamu*+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 17  Amaziya+ mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, anakhalabe ndi moyo zaka 15+ pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli. 18  Nkhani zina zokhudza Amaziya zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.+ 19  Patapita nthawi, anthu ena anagwirizana zom’chitira chiwembu+ ku Yerusalemu, choncho iye anathawira ku Lakisi.+ Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko n’kukamuphera komweko.+ 20  Atatero anamunyamula pa mahatchi n’kukamuika m’manda+ ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ 21  Kenako anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya,*+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16,+ n’kumulonga ufumu m’malo mwa bambo ake Amaziya.+ 22  Mfumuyo itagona m’manda ndi makolo ake, Azariya anamanga mzinda wa Elati+ n’kuubwezera ku Yuda. 23  M’chaka cha 15 cha Amaziya mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Isiraeli anakhala mfumu ku Samariya, ndipo analamulira zaka 41. 24  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye machimo onse a Yerobowamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli.+ 25  Yerobowamu ndiye anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kunyanja ya Araba.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri amene anachokera ku Gati-heferi.+ 26  Yehova anali ataona mavuto aakulu omwe Aisiraeli anali kukumana nawo.+ Kunalibe ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake, ngakhalenso munthu aliyense woti akanathandiza Aisiraeli.+ 27  Yehova anali atalonjeza kuti sadzachotseratu dzina la Isiraeli padziko lapansi,+ choncho anawapulumutsa+ ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehoasi. 28  Nkhani zina zokhudza Yerobowamu ndi zonse zimene anachita, zochita zake zamphamvu ndiponso mmene anamenyera nkhondo, ndi mmene anabwezeretsera Damasiko+ ndi Hamati+ ku Yuda mu Isiraeli, zinalembedwa m’buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 29  Pomalizira pake, Yerobowamu anagona pamodzi ndi makolo ake, mafumu a Isiraeli, ndipo Zekariya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Uyu ndi Yerobowamu Wachiwiri.
Azariya amatchedwanso Uziya.