2 Mafumu 13:1-25

13  M’chaka cha 23 cha Yehoasi+ mwana wa Ahaziya+ mfumu ya Yuda, Yehoahazi+ mwana wa Yehu+ anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya, kwa zaka 17.  Yehoahazi anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda motsatira tchimo la Yerobowamu+ mwana wa Nebati, limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+ Iye sanapatuke pa tchimolo.  Choncho mkwiyo wa Yehova+ unawayakira Aisiraeli, moti nthawi zonse ankawapereka m’manja mwa Hazaeli+ mfumu ya Siriya ndi m’manja mwa Beni-hadadi+ mwana wa Hazaeli.  Patapita nthawi Yehoahazi anakhazika pansi+ mtima wa Yehova, kotero kuti Yehova anamumvera,+ popeza anaona kuponderezedwa kwa Aisiraeli,+ chifukwa mfumu ya Siriya inali kuwapondereza.+  Chotero Yehova anapatsa Aisiraeli mpulumutsi,+ moti anachoka m’manja mwa Siriya. Kenako ana a Isiraeli anayamba kukhala m’nyumba zawo ngati kale.+  (Koma sanasiye tchimo la nyumba ya Yerobowamu limene anachimwitsa nalo Isiraeli.+ Anayenda m’tchimolo,+ ndipo mzati wopatulika+ unali ulipobe ku Samariya.)  Yehoahazi sanatsale ndi anthu alionse kupatulapo amuna 50 okwera pamahatchi, magaleta 10, ndi asilikali 10,000 oyenda pansi,+ chifukwa mfumu ya Siriya inawawononga+ ndi kuwapondaponda ngati fumbi la popunthira mbewu.+  Nkhani zina zokhudza Yehoahazi ndi zonse zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.  Pomalizira pake Yehoahazi anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo anamuika m’manda ku Samariya.+ Kenako Yehoasi+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 10  M’chaka cha 37 cha Yehoasi+ mfumu ya Yuda, Yehoasi mwana wa Yehoahazi anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya kwa zaka 16. 11  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Sanasiye machimo onse a Yerobowamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Isiraeli,+ koma anayenda m’machimowo. 12  Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zonse zimene anachita ndiponso zochita zake zamphamvu, komanso momwe anamenyanirana+ ndi Amaziya mfumu ya Yuda, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli. 13  Pomalizira pake Yehoasi anagona pamodzi ndi makolo ake, ndipo Yerobowamu*+ anakhala pampando wake wachifumu. Kenako Yehoasi anaikidwa m’manda ku Samariya pamodzi ndi mafumu a Isiraeli.+ 14  Tsopano Elisa+ anadwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo.+ Choncho Yehoasi mfumu ya Isiraeli anapita kwa iye n’kuyamba kulira atam’kumbatira n’kumati: “Bambo anga,+ bambo anga! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera pamahatchi ake!”+ 15  Ndiyeno Elisa anauza Yehoasi kuti: “Tengani uta ndi mivi.” Choncho iye anatenga uta ndi miviyo. 16  Kenako iye anauza mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Gwirani utawo.” Mfumuyo inaugwiradi, ndipo Elisa anaika manja ake pamanja+ a mfumuyo. 17  Kenako Elisa anati: “Tsegulani windo lakum’mawa.” Iye analitsegula. Ndiyeno Elisa anati: “Ponyani muviwo!” Choncho iye anauponya. Tsopano Elisa anati: “Muvi wa Yehova wopulumutsa! Muvi wopulumutsa+ kwa Asiriya! Ndithu mudzapha Asiriya ku Afeki+ mpaka kuwamaliza.” 18  Ananenanso kuti: “Tengani miviyo.” Pamenepo iye anaitenga. Ndiyeno Elisa anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Lasani pansi ndi miviyo.” Mfumuyo inalasa katatu n’kusiya.+ 19  Munthu wa Mulungu woonayo+ anakwiyira mfumuyo kwambiri, ndipo anati: “Mukanalasa maulendo asanu kapena maulendo 6! Mukanatero mukanaphadi Asiriya mpaka kuwamaliza, koma tsopano mudzawagonjetsa katatu kokha.”+ 20  Pambuyo pa zimenezi Elisa anamwalira ndipo anamuika m’manda.+ Tsopano panali magulu a achifwamba+ achimowabu+ amene ankabwera m’dzikolo kumayambiriro kwa chaka chilichonse. 21  Tsiku lina pamene anthu anali kuika munthu m’manda, anaona gulu la achifwamba. Nthawi yomweyo iwo anaponya mtembo wa munthuyo m’manda a Elisa n’kuthawa. Mtembowo utangokhudza mafupa a Elisa, munthuyo anakhalanso wamoyo+ ndipo anaimirira.+ 22  Hazaeli+ mfumu ya Siriya inapondereza+ Aisiraeli masiku onse a Yehoahazi. 23  Koma Yehova anakomera mtima+ Aisiraeli ndi kuwachitira chifundo+ ndipo anatembenukira kwa iwo chifukwa cha pangano lake+ ndi Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Yakobo.+ Iye sanafune kuwawononga+ ndipo sanawachotse pamaso pake mpaka lero. 24  Pomaliza pake Hazaeli mfumu ya Siriya anamwalira, ndipo Beni-hadadi mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 25  Ndiyeno Yehoasi mwana wa Yehoahazi, analandanso kwa Beni-hadadi mwana wa Hazaeli, mizinda imene iye analanda Yehoahazi bambo ake pankhondo. Yehoasi anagonjetsa Beni-hadadi katatu, ndipo analandanso mizinda ya Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Uyu ndi Yerobowamu Wachiwiri.