2 Mafumu 12:1-21

12  M’chaka cha 7 cha Yehu,+ Yehoasi+ anakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 40. Mayi ake anali a ku Beere-seba ndipo dzina lawo linali Zibiya.  Yehoasi anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova, masiku onse amene wansembe Yehoyada anali kumulangiza.+  Koma sanachotse malo okwezeka.+ Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.  Tsopano Yehoasi anauza ansembe kuti:+ “Ndalama zonse zimene anthu akubweretsa kunyumba ya Yehova+ za zopereka zopatulika,+ kutanthauza ndalama za msonkho zimene munthu aliyense akupereka,+ ndalama zoperekedwa ndi anthu amene achita chowinda,+ ndiponso ndalama zonse zimene munthu aliyense watsimikiza mumtima mwake kuti abweretse kunyumba ya Yehova,+  wansembe aliyense atenge ndalama zimenezi kwa anthu owadziwa,+ ndipo anthuwo kumbali yawo akonze ming’alu ya nyumbayo paliponse pamene pali mng’alu.”+  Koma pofika m’chaka cha 23 cha Mfumu Yehoasi, ansembe anali asanakonzebe ming’alu ya nyumbayo.+  Chotero Mfumu Yehoasi+ anaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena n’kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simukukonza ming’alu ya nyumbayi? Tsopano musatengenso ndalama zina kwa anthu owadziwa, koma muzipereke kuti akonzere ming’alu ya nyumbayi.”+  Pamenepo ansembewo anavomera kuti satenganso ndalama kwa anthu, ndipo sakonza ming’alu ya nyumbayo.  Tsopano wansembe Yehoyada anatenga bokosi+ n’kuboola kachibowo pachivundikiro chake. Kenako anaika bokosilo pambali pa guwa lansembe kumanja, munthu akamalowa m’nyumba ya Yehova. Ansembe omwe anali alonda a pakhomo+ anaika m’bokosilo ndalama zonse+ zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Yehova. 10  Akangoona kuti m’bokosilo muli ndalama zambiri, mlembi+ wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera n’kuwerenga ndi kumanga pamodzi ndalama zimene zinali kupezeka panyumba ya Yehova.+ 11  Iwo ankapereka ndalama zimene awerengazo kwa anthu ogwira ntchito+ amene anaikidwa panyumba ya Yehova. Anthu ogwira ntchitowo ankagwiritsa ntchito ndalamazo polipira amisiri a matabwa, omanga amene anali kugwira ntchito panyumba ya Yehovayo, 12  amisiri omanga ndi miyala, ndi anthu osema miyala.+ Ndalamazo anaguliranso matabwa ndi miyala yosema yokonzera ming’alu ya nyumba ya Yehova ndiponso analipirira zonse zimene anagwiritsa ntchito pokonza nyumbayo. 13  Koma sanapange mabeseni asiliva, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ malipenga,+ ndi ziwiya zilizonse zagolide kapena zasiliva za m’nyumba ya Yehova kuchokera pa ndalama zimene anthu anali kubweretsa kunyumba ya Yehova,+ 14  chifukwa ankapereka ndalamazo kwa anthu ogwira ntchitoyo, ndipo anthuwo anakonza nyumba ya Yehova ndi ndalamazo.+ 15  Amuna amene ankapatsidwa ndalama kuti azipereke kwa anthu ogwira ntchito,+ sankafunsidwa+ mmene ayendetsera ndalamazo chifukwa ankagwira ntchito mokhulupirika.+ 16  Ndalama za nsembe za kupalamula ndi ndalama za nsembe zamachimo+ sanali kuzibweretsa kuti adzazigwiritse ntchito yokonzetsera nyumba ya Yehova, choncho zinakhala za ansembe.+ 17  Panthawi imeneyo Hazaeli+ mfumu ya Siriya anapita kukamenyana ndi mzinda wa Gati+ n’kuulanda. Kenako Hazaeli anatsimikiza zopita*+ kukaukira Yerusalemu.+ 18  Pamenepo Yehoasi mfumu ya Yuda anatenga zopereka zonse zopatulika+ zimene Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya makolo ake, mafumu a Yuda anaziyeretsa. Anatenganso zopereka za iyeyo zopatulika, ndi golide yense yemwe anali mosungira chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi cha m’nyumba ya mfumu n’kutumiza+ zonsezi kwa Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Hazaeli anabwerera osaukira Yerusalemu. 19  Nkhani zina zokhudza Yehoasi ndi zonse zimene anachita zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 20  Koma atumiki+ a Yehoasi anagwirizana zom’chitira chiwembu+ ndipo anamupha panyumba+ ya Chimulu cha Dothi*+ panjira yotsetserekera ku Sila. 21  Atumiki ake amene anamupha anali Yozakara+ mwana wa Simeyati ndi Yehozabadi mwana wa Someri. Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide pamodzi ndi makolo ake, ndipo Amaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Anatembenuza nkhope yake kuti apite.”
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 5:9.