2 Mafumu 11:1-21

11  Tsopano Ataliya,+ mayi wa Ahaziya+ ataona kuti mwana wake wafa, anapha ana onse achifumu.+  Koma Yehoseba+ mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa+ m’chipinda chamkati chogona kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.  Anapitiriza kubisidwa m’nyumba ya Yehova zaka 6, pamene Ataliya anali kulamulira dzikolo.+  M’chaka cha 7, Yehoyada+ anatumiza uthenga kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 olondera mfumu Achikariya,+ ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100 othamanga.+ Anawaitanitsa kuti abwere kwa iye kunyumba ya Yehova ndipo anachita nawo pangano+ n’kuwalumbiritsa+ kunyumba ya Yehova. Kenako anawaonetsa mwana wa mfumu uja.  Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Gawo limodzi mwa magawo atatu a inu lidzabwere pa tsiku la sabata kudzalondera nyumba ya mfumu mosamala.+  Gawo lina limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata+ chotchedwa Maziko, ndipo gawo linanso limodzi mwa magawo atatu a inu lidzakhale pachipata kumbuyo kwa asilikali othamanga. Muzidzasinthana kulondera mosamala nyumbayo.+  Magulu awiri a inu amene adzatuluke pa sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu.  Mudzaizungulire mfumuyo kumbali zonse, aliyense atatenga zida zake m’manja, ndipo aliyense wolowa pakati pa mizere ya anthu adzaphedwe. Muzidzakhala limodzi ndi mfumuyo ikamatuluka ndiponso ikamalowa.”  Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachita mogwirizana ndi zonse zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga amuna ake amene anali kulowa pa sabata,+ pamodzi ndi amene anali kutuluka pa sabata, n’kupita kwa wansembe Yehoyada. 10  Tsopano wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira za Mfumu Davide, zomwe zinali m’nyumba ya Yehova.+ 11  Asilikali othamanga+ anaimirira, aliyense atatenga zida zake m’manja, kuyambira kumbali yakumanja* ya nyumbayo mpaka kukafika kumbali yakumanzere* ya nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 12  Kenako anatulutsa mwana+ wa mfumu uja. Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu+ n’kumudzoza.+ Ndiyeno anayamba kuwomba m’manja+ n’kumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+ 13  Ataliya atamva anthu akuchita phokoso komanso akuthamanga, nthawi yomweyo anapita kwa anthu amene anali panyumba ya Yehova.+ 14  Atafika anaona mfumu itaimirira pafupi ndi chipilala+ malinga ndi mwambo wawo. Anaonanso atsogoleri a asilikali ndi anthu oimba malipenga+ ali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a m’dzikolo anali kusangalala+ ndi kuimba malipenga. Nthawi yomweyo Ataliya+ anang’amba zovala zake n’kuyamba kukuwa kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!”+ 15  Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa,+ kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu! Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!”+ Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Muonetsetse kuti asaphedwere m’nyumba ya Yehova.” 16  Choncho anamugwira n’kumutulutsira pakhomo la kunyumba ya mfumu+ lolowera mahatchi,+ ndipo anam’phera pamenepo.+ 17  Kenako Yehoyada anachita pangano+ pakati pa Yehova,+ mfumu,+ ndi anthu, kuti anthuwo azisonyeza kuti ndi anthu a Yehova. Anachitanso pangano pakati pa mfumu ndi anthuwo.+ 18  Pambuyo pake, anthu onse a m’dzikolo anapita kukachisi wa Baala n’kukagwetsa maguwa ake ansembe.+ Mafano ake anawaphwanyaphwanya,+ ndipo Mateni+ wansembe wa Baala anamupha patsogolo pa maguwa ansembewo.+ Kenako wansembe Yehoyada anaika anthu kuti aziyang’anira nyumba ya Yehova.+ 19  Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100, asilikali olondera mfumu Achikariya,+ asilikali othamanga,+ ndi anthu onse a m’dzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anadzera njira ya pachipata+ cha asilikali othamanga, mpaka anafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu+ wa mafumu. 20  Anthu onse a m’dzikolo anapitiriza kusangalala,+ ndipo mumzindawo munali bata. Ataliya anali atamupha ndi lupanga panyumba ya mfumu.+ 21  Yehoasi+ anali ndi zaka 7 pamene anayamba kulamulira.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Phewa lakumanja,” kutanthauza mbali ya kum’mwera, munthu akayang’ana kum’mawa.
Mawu ake enieni, “Phewa lakumanzere,” kutanthauza mbali ya kumpoto, munthu akayang’ana kum’mawa.