2 Mafumu 1:1-18

1  Ahabu+ atamwalira, Amowabu+ anayamba kupandukira+ Isiraeli.  Kenako Ahaziya ali m’nyumba yake ku Samariya, anagwa+ kuchokera pachipinda chapadenga+ kudzera pachibowo chotchinga, ndipo anavulala. Atatero anatuma amithenga kuti: “Pitani kwa Baala-zebubu+ mulungu wa ku Ekironi,+ mukafunse+ ngati ndichire matenda angawa.”+  Ndiyeno mngelo+ wa Yehova anauza Eliya wa ku Tisibe+ kuti: “Nyamuka ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu+ kuti mupite kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi?  Tsopano Yehova wanena kuti: “Pabedi wakwerapo sutsikapo, chifukwa umwalira ndithu.”’”+ Eliya atalankhula mawu amenewa, anachoka.  Amithenga aja atabwerera kwa Ahaziya, nthawi yomweyo iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mwabwerera?”  Amithengawo anamuyankha kuti: “Munthu winawake anabwera kudzakumana nafe ndipo watiuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene yakutumani ndipo mukaiuze kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Kodi ku Isiraeli kulibe Mulungu kuti utumize anthu kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi? Pa chifukwa chimenechi, pabedi wakwerapo sutsikapo, chifukwa umwalira ndithu.’”’”+  Pamenepo mfumuyo inawafunsa kuti: “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo n’kukuuzani zimenezi anali kuoneka bwanji?”  Iwo anayankha kuti: “Munthuyo anavala chovala chaubweya+ ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake.”+ Mfumuyo itangomva zimenezi, inanena kuti: “Ndi Eliya wa ku Tisibe.”  Ndiyeno mfumuyo inatumiza kwa Eliya mtsogoleri wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Mtsogoleriyo atafika, anam’peza atakhala pamwamba pa phiri ndipo anamuuza kuti: “Munthu wa Mulungu woona+ iwe, mfumu yanena kuti, ‘Tsika!’” 10  Koma Eliya anayankha mtsogoleri wa asilikali 50 uja kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu, moto+ utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Ndipo moto unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50.+ 11  Kenako mfumuyo inam’tumiziranso mtsogoleri wina wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Mtsogoleriyo anauza Eliya kuti: “Munthu wa Mulungu woona iwe, mfumu yanena kuti, ‘Tsika msanga!’”+ 12  Koma Eliya anawayankha kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu woona, moto utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Ndipo moto wa Mulungu unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50. 13  Mfumuyo inatumizanso mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 pamodzi ndi asilikali ake 50.+ Koma mtsogoleri wachitatu wa asilikali 50 ameneyo anabwera n’kugwada+ pamaso pa Eliya ndipo anayamba kumuchonderera+ kuti awachitire chifundo. Iye anati: “Inu munthu wa Mulungu woona, chonde moyo wanga+ ndi moyo wa atumiki anu 50 awa ukhale wamtengo wapatali+ m’maso mwanu. 14  Pajatu moto unatsika kumwamba n’kunyeketsa+ atsogoleri awiri aja ndi magulu awo a asilikali 50, koma tsopano moyo wanga ukhale wamtengo wapatali m’maso mwanu.” 15  Pamenepo mngelo wa Yehova anauza Eliya kuti: “Tsika upite naye limodzi, usamuope.”+ Choncho Eliya ananyamuka n’kupita pamodzi ndi mtsogoleri uja kwa mfumu. 16  Atafika, Eliya anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti watumiza anthu+ kukafunsa kwa Baala-zebubu mulungu wa ku Ekironi+ ngati kuti ku Isiraeli kulibe Mulungu amene ungafunsireko mawu ake, sutsika pabedi wakwerapo, chifukwa umwalira ndithu.’” 17  Patapita nthawi, Ahaziya anamwalira,+ mogwirizana ndi mawu+ a Yehova amene Eliya ananena. Kenako Yehoramu*+ anayamba kulamulira m’malo mwake chifukwa Ahaziya analibe mwana wamwamuna. Iye anayamba kulamulira m’chaka chachiwiri cha Yehoramu+ mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda. 18  Zinthu zina zimene Ahaziya+ anachita zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Ameneyu anali m’bale wake wa Ahaziya.