2 Atesalonika 3:1-18

3  Pomalizira abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova*+ apitirize kufalikira mofulumira+ ndi kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu.  Muzitero kutinso tilanditsidwe kwa anthu opweteka anzawo ndi oipa,+ pakuti chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.+  Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.+  Komanso ifeyo monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro+ mwa inu kuti mukuchita zimene tinalamula ndipo mudzapitiriza kutero.+  Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda+ Mulungu ndi kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.  Tsopano tikukulangizani+ abale m’dzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe+ m’bale aliyense woyenda mosalongosoka+ komanso mosagwirizana ndi mwambo umene tinakupatsani.+  Pakuti inuyo mukudziwa mmene muyenera kutitsanzirira.+ Sitinakhale mosalongosoka pakati panu,+  kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.+ M’malomwake, mwa ntchito yathu imene tinagwira mwakhama ndi thukuta lathu,+ tinagwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+  Sikuti tinatero chifukwa chopanda ulamuliro,+ koma kuti tikhale chitsanzo kwa inu, kuti inu mutitsanzire.+ 10  Ndiponso, pamene tinali ndi inu, tinali kukupatsani lamulo ili:+ “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11  Pakuti tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka+ pakati panu, sakugwira ntchito n’komwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12  Anthu otero tikuwalamula ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu kuti, mwa kugwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena, adye chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+ 13  Koma inu abale, musaleke kuchita zabwino.+ 14  Koma ngati wina sakumvera mawu athu+ a m’kalatayi, muikeni chizindikiro+ ndipo lekani kuchitira naye zinthu limodzi,+ kuti achite manyazi.+ 15  Komabe musamuone monga mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga m’bale. 16  Tsopano Ambuye wamtendere mwiniyo, akupatseni mtendere nthawi zonse m’njira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu. 17  Landirani moni wanga, ineyo Paulo, wolemba ndekha m’kalembedwe kanga,+ komwe ndi chizindikiro m’kalata yanga iliyonse. Aka ndiko kalembedwe kanga. 18  Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.