2 Atesalonika 2:1-17

2  Komabe abale, za kukhalapo*+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhanitsidwa kwathu kwa iye,+ tikukupemphani  kuti musafulumire kugwedezeka pa maganizo anu, kapena kutengekatengeka ndi mawu ouziridwa+ onena kuti tsiku la Yehova lafika.+ Musatero ayi, ngakhale utakhala uthenga wapakamwa,+ kapena kalata+ yooneka ngati yachokera kwa ife.  Wina asakunyengeni pa nkhani imeneyi m’njira iliyonse. Pakuti tsikulo silidzayamba kufika mpatuko+ usanachitike, ndiponso asanaonekere+ munthu wosamvera malamulo,+ amene ndiye mwana wa chiwonongeko.+  Iye ndi wotsutsa+ amene amadzikweza pamwamba pa aliyense wotchedwa “mulungu” kapena chilichonse chopembedzedwa, moti amakhala pansi m’kachisi wa Mulungu, n’kumadzionetsera ngati mulungu.+  Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu ndinali kukuuzani+ zimenezi?  Ndipo inu mukudziwa chimene+ chikuchititsa kuti panopa asaonekere,+ kuti adzaonekere mu nthawi yake yoyenera.+  Zoona, chinsinsi cha kusamvera malamulo kumeneku chilipo kale,+ koma chingokhalapo kufikira atachoka amene panopa ali choletsa.+  Pamenepo, wosamvera malamuloyo adzaonekera ndithu, amene Ambuye Yesu adzamuthetsa ndi mzimu wa m’kamwa mwake,+ pomuwonongeratu pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere.+  Koma kukhalapo kwa wosamvera malamuloyo kukutheka mwa mphamvu+ za Satana. Adzachita ntchito iliyonse yamphamvu ndi zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa,+ 10  ndi kusalungama ndi chinyengo chilichonse.+ Zonsezi adzazichita kwa amene akupita kukawonongedwa.+ Izi zidzakhala chilango kwa iwo chifukwa sanasonyeze kuti akulakalaka+ choonadi, kuti apulumuke.+ 11  Ichi n’chifukwa chake Mulungu walola kuti iwo anyengedwe ndipo azikhulupirira bodza,+ 12  kuti onsewo adzaweruzidwe chifukwa sanakhulupirire choonadi,+ koma anakonda zosalungama.+ 13  Komabe, tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenera kutero chifukwa Mulungu anakusankhani+ kuchokera pachiyambi kuti mudzapulumuke mwa kukuyeretsani+ ndi mzimu,+ ndiponso mwa chikhulupiriro chanu m’choonadi.+ 14  Anakuitanani ku chipulumutso chimenechi kudzera mu uthenga wabwino umene tikulengeza,+ kuti mudzapeze ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 15  Choncho abale, khalani olimba+ ndipo gwirani mwamphamvu miyambo+ imene munaphunzitsidwa, kaya mwa uthenga wapakamwa kapena mwa kalata yochokera kwa ife. 16  Komanso, Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda+ ndipo amatilimbikitsa m’njira yosalephera ndiponso anatipatsa chiyembekezo chabwino,+ mwa kukoma mtima kwakukulu, 17  alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani muntchito yabwino iliyonse ndiponso m’mawu.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 8.