2 Akorinto 9:1-15
9 Tsopano ponena za utumiki+ wothandiza oyerawo, n’zosafuna kuti ndichite kukulemberani.
2 Pakuti ndikudziwa kuti muli ndi mtima wofunitsitsa ndipo ndikunena zimenezi monyadira kwa Amakedoniya. Ndikumawauza kuti, “Abale a ku Akaya akhala okonzeka kwa chaka chimodzi tsopano,”+ ndipo kudzipereka kwanu kwalimbikitsa ambiri a iwo.
3 Koma ndikutumiza abale kuti tisangokunyadirani pachabe pa nkhani imeneyi, koma kuti mukhaledi okonzeka,+ monga ndinali kuwauzira kuti mudzakhala okonzeka.
4 Koma ngati ndingadzafike kumeneko pamodzi ndi Amakedoniya n’kupeza kuti simuli okonzeka, manyazi adzagwira ifeyo ndi inu nomwe, chifukwa tinali kukudalirani.
5 N’chifukwa chake ndinaona kuti ndi bwino kuti ndilimbikitse abale abwere kwa inu ife tisanafike, n’cholinga choti adzakuthandizeni kukonzeratu mphatso imene mukuipereka chifukwa cha kuwolowa manja kwanu, imenenso munalonjeza pa chiyambi.+ Ndiye tikadzafika, mphatsoyi idzakhala itakonzedwa kale ndipo zidzaonekeratu kuti simukupereka mphatsoyi chifukwa choti takukakamizani, koma chifukwa choti ndinu owolowa manja.+
6 Koma ponena za nkhaniyi, wobzala moumira+ adzakololanso zochepa, ndipo wobzala mowolowa manja+ adzakololanso zochuluka.
7 Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika+ kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.+
8 Komanso, Mulungu akhoza kuchititsa kuti kukoma mtima kwake konse kwakukulu kusefukire kwa inu. Choncho nthawi zonse mudzakhala ndi zinthu zokwanira kusamalira zosowa zanu, ndipo mudzakhalanso ndi zinthu zambiri zogwiritsa ntchito pa ntchito iliyonse yabwino.+
9 (Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Iye wagawira ena mowolowa manja. Wapereka kwa anthu aumphawi, ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.”+
10 Tsopano amene amapereka mbewu kwa wobzala, amenenso amapereka chakudya kuti anthu adye,+ adzakupatsani mbewu zoti mubzale ndipo adzakupatsani zimenezi mowolowa manja. Adzawonjezeranso zipatso za chilungamo chanu.)+
11 Mulungu akukudalitsani m’njira iliyonse kuti muthe kupereka mowolowa manja m’njira zosiyanasiyana, ndipo kudzera m’zochita zathu, kuwolowa manja koteroko kukuchititsa anthu kuyamika Mulunguyo.+
12 Zili choncho chifukwa utumiki wothandiza anthu umenewu si kuti ukungopatsa oyerawo zinthu zochuluka zimene akufunikira,+ koma ukuchititsanso anthu ambiri kupereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu.
13 Chifukwa cha umboni umene utumikiwu ukupereka, iwo akulemekeza Mulungu. Akutero chifukwa inuyo mwagonjera uthenga wabwino wonena za Khristu,+ monga mmene mukulengezera poyera, ndiponso chifukwa chakuti mwapereka chopereka kwa iwowo ndi kwa onse mowolowa manja.+
14 Chotero iwo amakuperekerani mapembedzero kwa Mulungu ndiponso amakukondani kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu+ kumene Mulungu wakusonyezani.
15 Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.+