2 Akorinto 8:1-24

8  Tsopano abale, tikufuna kukudziwitsani za kukoma mtima kwakukulu kumene mipingo ya ku Makedoniya yasonyezedwa ndi Mulungu.+  Pamene iwo anali kuyesedwa kwambiri chifukwa cha mavuto, anali achimwemwe kwambiri ndiponso anasonyeza kuwolowa manja kwakukulu, ndipo anachita zimenezi ngakhale kuti anali pa umphawi wadzaoneni.+  Pakuti anachita malinga ndi zimene akanatha,+ komanso ndikuwachitira umboni kuti anachita ngakhale zoposa pamenepo,  ndipo anapitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima ndiponso mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo ndi kutinso achite nawo utumiki wothandiza oyerawo.+  Ndipo iwo sanangochita zimene tinali kuyembekeza zokha, koma choyamba anadzipereka kwa Ambuye+ ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.  Zimenezi zinatichititsa kuti timulimbikitse Tito+ kuti, popeza iye ndiye anayambitsa zoperekazi pakati panu, iyeyo amalizitse kusonkhanitsa mphatso zanu zachifundo.  Inuyo mukusefukira mu ntchito+ monga chikhulupiriro, kudziwa kulankhula, kudziwa zinthu,+ khama pa zonse zimene mumachita, ndipo mumasonyeza chikondi chofanana ndi chimene tili nacho pa inu. Chotero musefukirenso chimodzimodzi pa nkhani ya kupereka kumene tikunenaku.  Sindikukulamulani,+ koma ndikulankhula izi chifukwa cha khama limene ena asonyeza, kutinso ndione ngati chikondi chanu chilidi chenicheni.  Pakuti mukudziwa kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale kuti iye anali wolemera, anakhala wosauka chifukwa cha inu,+ kuti inuyo mulemere+ kudzera m’kusauka kwake. 10  Ndipereke maganizo anga pamenepa:+ nkhani imeneyi ndi yopindulitsa kwa inu,+ poona kuti chaka chimodzi chatha kale kuyambira pamene munayambitsa zimenezi. Sikuti munangoziyambitsa chabe, komanso munazichita modzipereka kwambiri.+ 11  Ndiyeno tsopano, malizitsani kupatsa kumeneku, kuti monga mmene munalili ofunitsitsa kuchita zimenezi, mumalizitsenso kutero malinga ndi zimene muli nazo. 12  Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe,+ osati zimene sangathe. 13  Sindikufuna kuti kwa ena zikhale zosavuta,+ koma kwa inu zovuta ayi. 14  Koma ndikufuna kuti zochuluka zimene muli nazo zithandizire pa zimene iwowo akusowa, ndipo zochuluka zimene iwowo ali nazo zithandizire pa zimene inuyo mukusowa, kuti pakhale kufanana.+ 15  Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Munthu wokhala ndi zambiri sanakhale ndi zopitirira muyezo, ndipo munthu wokhala ndi zochepa sanakhale ndi zocheperatu.”+ 16  Tikuyamika Mulungu chifukwa Tito amakuderaninso nkhawa ngati mmene ifeyo timachitira,+ 17  chifukwa iyeyo wamveradi zimene tinamulimbikitsa kuti achite, ndipo popeza kuti ndi wakhama kwambiri, akubwera kwanuko mwa kufuna kwake. 18  Komanso pamodzi ndi iye, tikutumiza m’bale wina amene akutamandidwa m’mipingo yonse chifukwa cha zimene akuchita zokhudzana ndi uthenga wabwino. 19  Si zokhazo, koma anaikidwanso+ ndi mipingo kuti akhale woyenda nafe pamene tikubweretsa mphatso zachifundozi. Tikupereka mphatsozi kuti zipereke ulemerero+ kwa Ambuye, komanso kuti tisonyeze kuti ndife ofunitsitsa kuthandiza ena.+ 20  Choncho sitikufuna kuti munthu aliyense atipeze chifukwa+ pa zopereka zaufulu+ zimene tikubweretsazi. 21  Pakuti “timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.”+ 22  Pamodzi ndi abalewo, tatumizanso m’bale wathu amene mobwerezabwereza tamuona kuti ndi wakhama pa zinthu zambiri, ndipo tsopano wawonjezera khama lake chifukwa akukukhulupirirani kwambiri. 23  Koma ngati mukukayikira zilizonse zokhudza Tito, ndikufuna ndikuuzeni kuti iye ndi mnzanga komanso ndikugwira naye ntchito limodzi+ pothandiza inuyo. Kapena ngati mungakayikire zilizonse zokhudza abale athuwa, iwo ndi nthumwi za mipingo ndipo amabweretsa ulemerero kwa Khristu. 24  Choncho asonyezeni kuti chikondi+ chanu ndi chenicheni ndiponso kuti sitinakunyadireni pachabe.+

Mawu a M'munsi