2 Akorinto 7:1-16

7  Chotero okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi,+ tiyeni tidziyeretse+ ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu,+ kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.+  Tipatseni malo m’mitima mwanu.+ Ifetu sitinalakwire aliyense, sitinaipitse aliyense, ndipo sitinachenjerere aliyense.+  Sikuti ndanena izi kuti ndikutsutseni ngati olakwa ayi. Pajatu ndanena kale kuti inuyo muli m’mitima yathu, kaya tife kapena tikhale moyo.+  Ndimalankhula nanu momasuka kwambiri. Ndimakunyadirani kwambiri.+ Mtima wanga walimbikitsidwa kwambiri,+ ndipo ndikusefukira ndi chimwemwe m’masautso athu onse.+  Ndipotu, pamene tinafika ku Makedoniya,+ thupi lathu silinapumule,+ koma masautso amitundumitundu anapitirizabe kutigwera.+ Kunja anali kulimbana nafe, mkati tinali kukhala mwamantha.  Komabe Mulungu, amene amalimbikitsa+ osautsika mtima, anatilimbikitsa ndi kukhalapo* kwa Tito.  Koma osati chabe chifukwa tinali ndi Tito, komanso chifukwa cha mmene inuyo munamulimbikitsira, pamene anatibweretsera uthenga+ wakuti mukufunitsitsa kulapa, muli ndi chisoni, ndiponso mukundidera nkhawa. Nditamva zimenezi ndinakondweranso kwambiri.  Choncho ngakhale kuti ndinakuchititsani kumva chisoni ndi kalata yanga,+ sindikudandaula. (Ndikuona kuti kalatayo inakuchititsani kumva chisoni, koma kwa kanthawi kochepa.) Chotero, ngakhale kuti poyambapo ndinadandaula,  panopa ndikukondwera. Sikuti ndikukondwera chifukwa munamva chisoni, koma chifukwa chakuti chisoni chimene munamvacho chinakuchititsani kulapa.+ Pakuti munamva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu,+ chotero simunapwetekedwe m’njira iliyonse chifukwa cha zimene tinalemba. 10  Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+ 11  Ndipo taonani zimene chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu+ chimenechi chakuchitirani. Chakuchititsani kukhala akhama kwambiri, chakuchititsani kudziyeretsa, kuipidwa, mantha, kufunitsitsa kulapa, kudzipereka, ndiponso kukonza cholakwacho.+ Mwanjira ina iliyonse, munasonyeza kuti ndinu oyera pa nkhani imeneyi. 12  Ndithudi, ngakhale kuti ndinakulemberani, sindinatero chifukwa cha wolakwayo+ kapena wolakwiridwayo ayi, koma kuti khama lanu lofuna kumvera mawu athu lionekere pamaso pa Mulungu. 13  N’chifukwa chake talimbikitsidwa. Komabe, kuwonjezera pa kulimbikitsidwa, tinakondweranso kwambiri chifukwa chakuti Tito ali ndi chimwemwe, popeza nonsenu mwatsitsimutsa mtima wake.+ 14  Pakuti ngati ndinalankhula mokunyadirani kwa iyeyo, simunandichititse manyazi. Koma zimene tinalankhula monyadira kwa Tito n’zoona,+ monganso mmene zilili zinthu zonse zimene tinalankhula nanu. 15  Ndiponso iyeyo amakukondani kwambiri nonsenu akakumbukira kumvera kwanu,+ komanso mmene munamulandirira ndi mantha ndiponso kunjenjemera. 16  Ndine wosangalala kuti m’njira iliyonse mukundilimbikitsa.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 8.