2 Akorinto 6:1-18
6 Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+
2 Pakuti iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo m’tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa.+ Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.+
3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa,+ kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.+
4 Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta,+
5 kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende,+ kukumana ndi zipolowe, kugwira ntchito mwakhama, kusagona tulo, ndi kukhala osadya.+
6 Tikusonyezanso zimenezi mwa kukhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ okhala ndi mzimu woyera, osonyeza chikondi chopanda chinyengo,+
7 olankhula zoona, ndiponso okhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso, tikuchita zimenezi ponyamula zida+ za chilungamo kudzanja lamanja ndi lamanzere,
8 mwa kupatsidwa ulemerero ndi kutonzedwa, mwa kuneneredwa zoipa komanso zabwino. Mwa kukhala ngati achinyengo+ koma oona mtima,
9 ngati osadziwika koma odziwika bwino,+ ngati oti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa+ koma osakaphedwa,+
10 ngati ogwidwa ndi chisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri, ngati opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.+
11 Takhala tikulankhula mosabisa mawu kwa inu Akorinto, tafutukula mtima wathu.+
12 Malo sakukucheperani mumtima mwathu,+ koma m’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa.+
13 Choncho mutibwezere zofanana ndi zimene takuchitirani. Ndikulankhula nanu ngati ana anga,+ inunso futukulani mtima wanu.
14 Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+
15 Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Kapena munthu wokhulupirira angagawane+ chiyani ndi wosakhulupirira?
16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+
17 “‘Choncho tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+
18 “‘Ndidzakhala atate wanu,+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova Wamphamvuyonse.”+