2 Akorinto 5:1-21
5 Tikudziwa kuti nyumba yathu ya padziko lapansi pano,+ msasa uno,+ ikadzaphwasuka,+ tidzalandira nyumba yochokera kwa Mulungu. Imeneyo idzakhala nyumba yosamangidwa ndi manja,+ koma yamuyaya,+ ndipo idzakhala kumwamba.
2 Pakuti tikubuula m’nyumba imene tikukhalamoyi+ pofunitsitsa kuvala yathu yakumwamba,+
3 kuti tikadzaivala, tisadzapezeke amaliseche.+
4 Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula chifukwa cholemedwa. Kwenikweni si chifukwa chofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo,+ kuti chokhoza kufachi chilowedwe m’malo ndi moyo.+
5 Tsopano amene anatikonzekeretsa kuti tilandire zimenezi ndi Mulungu.+ Iye ndiye anatipatsa chikole+ cha zinthu zam’tsogolo, chomwe ndi mzimu.+
6 Chotero nthawi zonse timakhala olimba mtima ndipo tikudziwa kuti pamene tikukhala m’thupi, tili kutali ndi Ambuye,+
7 pakuti tikuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.+
8 Koma tikulimba mtima ndipo ndife okondwa kukakhala ndi Ambuye, m’malo mokhala m’thupi linoli.+
9 Choncho n’cholinga chathunso kuti, kaya tikhale ndi iye kapena tikhale kutali naye,+ tikhale ovomerezeka kwa iye.+
10 Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+
11 Choncho popeza timaopa+ Ambuye, tikupitiriza kukopa+ anthu. Mulungu akudziwa bwino zolinga zathu. Koma ndili ndi chikhulupiriro kuti inunso, mwachikumbumtima chanu, mukudziwa bwino zolinga zathu.+
12 Sikuti tayambanso kudzichitira umboni+ tokha kwa inu ayi, koma tikukupatsani chifukwa chodzitamandira, ndipo chifukwacho ndifeyo,+ kuti muwayankhe amene amadzitama chifukwa cha maonekedwe akunja,+ osati chifukwa cha mtima.+
13 Pakuti ngati tinachita misala,+ tinachitira Mulungu. Ngati tili olongosoka,+ cholinga ndi kupindulitsa inuyo.
14 Pakuti chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse,+ chifukwatu onsewo anali atafa kale.
15 Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha,+ koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera+ n’kuukitsidwa.+
16 Ndiye chifukwa chake kuyambira tsopano sitiona munthu mwakuthupi.+ Ngakhale kuti Khristu tinamuona mwakuthupi,+ tsopano sitikumuonanso motero.+
17 Choncho ngati aliyense ali wogwirizana ndi Khristu, iye ndi cholengedwa chatsopano.+ Zinthu zakale zinatha,+ ndipo pali zatsopano.+
18 Koma zinthu zonse n’zochokera kwa Mulungu, amene anatigwirizanitsa+ ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki+ wokhazikitsanso mtendere.
19 Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwirizanitsa dziko+ ndi iyeyo+ kudzera mwa Khristu,+ moti sanawawerengere anthuwo machimo awo,+ ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga+ umenewu wokhazikitsanso mtendere.+
20 Chotero ndife+ akazembe+ m’malo mwa Khristu,+ ngati kuti Mulungu akuchonderera anthu kudzera mwa ife.+ Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti:+ “Gwirizananinso ndi Mulungu.”
21 Amene analibe uchimoyo,+ Mulungu anamupanga kukhala uchimo+ chifukwa cha ife, kuti tikhale olungama pamaso pa Mulungu+ kudzera mwa iye.