2 Akorinto 13:1-14

13  Aka ndi kachitatu+ tsopano kukonza ulendo wobwera kwanuko. “Muzitsimikizira nkhani iliyonse mutamva umboni wa pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.”+  Ngakhale kuti panopa ndili kutali ndi inu, koma muone mawu angawa ngati kuti ndili limodzi nanu kachiwiri. Choncho, monga mmene ndinachitira kale, ndikuchenjeza anthu amene anachimwa, komanso ena onse, kuti ndikadzabweranso kumeneko sindidzalekerera munthu.+  Ndatero chifukwa mukufunafuna umboni wosonyeza kuti Khristu akulankhuladi mwa ine.+ Iye si wofooka kwa inu koma ndi wamphamvu pakati panu.  Zoonadi, iye anapachikidwa pamtengo+ chifukwa anadzakhala wofooka,+ koma ali ndi moyo mwa mphamvu ya Mulungu.+ Inde, ifenso ndife ofooka limodzi naye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye+ mwa mphamvu ya Mulungu+ imene ikugwira ntchito mwa inu.  Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.+ Kodi simukudziwa kuti Yesu Khristu ndi wogwirizana ndi inu?+ Muyenera kudziwa zimenezi, kupatulapo ngati muli osavomerezeka.  Ndikukhulupirira kuti mudzadziwa kuti ndife ovomerezeka.  Tsopano tikupemphera+ kwa Mulungu kuti musachite cholakwa chilichonse. Cholinga changa pochita zimenezi si chakuti ifeyo tioneke kuti ndife ovomerezeka ayi, koma kuti inuyo muzichita zabwino.  Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma zinthu zokhazo zogwirizana ndi choonadi.+  Ndithudi timasangalala nthawi zonse inu mukakhala amphamvu, pamene ife tili ofooka.+ Ndipo chimene tikupempherera+ n’chakuti musinthe zinthu zimene mukuyenera kusintha. 10  N’chifukwa chake ndikulemba zinthu zimenezi pamene sindili kumeneko, kuti ndikadzakhalako ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwamphamvu,+ chifukwa Ambuye anandipatsa ulamulirowu kuti ndizikulimbikitsani,+ osati kukufooketsani. 11  Pomalizira abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu, kulimbikitsidwa,+ kukhala ndi maganizo ogwirizana,+ ndiponso kukhala mwamtendere.+ Mukatero, Mulungu wachikondi ndi wamtendere+ adzakhala nanu. 12  Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwaubale.+ 13  Oyera onse akupereka moni kwa inu. 14  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu, chikondi cha Mulungu, komanso mzimu woyera umene mukupindula nawo limodzi, zikhale nanu nonsenu.+

Mawu a M'munsi