2 Akorinto 11:1-33

11  Ndikanakonda kuti mundilole kuti ndidzikweze pang’ono.+ Ndipotu zoona zake n’zakuti, mwandilola kale.  Ndikukuchitirani nsanje,+ ngati imene Mulungu amakuchitirani, popeza ndine ndinakuchititsani kulonjezedwa ukwati+ ndi mwamuna mmodzi,+ Khristu,+ ndipo ndikufuna kukuperekani ngati namwali woyera+ kwa iye.  Koma nkhawa yanga ndi yakuti mwina, monga mmene njoka inanamizira Hava+ ndi chinyengo chake, maganizo anunso angapotozedwe+ kuti musakhalenso oona mtima ndi oyera ngati mmene muyenera kuchitira kwa Khristu.+  Chifukwa panopa wina akabwera kwa inu n’kulalikira za Yesu wosiyana ndi amene tinamulalikira,+ kapena wina akakubweretserani mzimu wosiyana ndi umene munalandira kale,+ kapena uthenga wabwino+ wosiyana ndi umene munaulandira, inu mumangomulolera munthu woteroyo.+  Koma ine ndikuona kuti sindikuchepa+ mwanjira ina iliyonse kwa atumwi anu apamwambawo.+  Ngati ndilibe luso la kulankhula,+ si kuti ndine wosadziwanso zinthu.+ Koma m’njira iliyonse tinakusonyezani kuti ndife odziwa zinthu pa zonse.+  Kapena kodi ndinachita tchimo pamene ndinadzichepetsa+ kuti inuyo mukwezedwe, muja ndinalengeza mosangalala uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu, popanda inuyo kutayirapo ndalama?+  Ndinalanda mipingo ina zinthu zawo polandira chithandizo chawo kuti nditumikire inuyo.+  Koma pamene ndinasowa zofunika zina ndili kwanuko, sindinalemetse ngakhale munthu mmodzi,+ popeza abale amene anachokera ku Makedoniya+ anandipatsa zonse zimene ndinali kuzisowa. Ndithu, sindinakulemetseni m’njira iliyonse, ndipo ndipitirizabe kutero.+ 10  Ndikulankhula choonadi+ cha Khristu, choncho palibe angandiletse kudzitamandira+ m’madera a ku Akaya. 11  Kodi ndachita zimenezi chifukwa chiyani? Chifukwa sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani.+ 12  Tsopano ndipitiriza kuchita zimene ndikuchita,+ kuti nditsekereze anthu amene akuyesayesa kupeza chifukwa choti anamizire kuti ndi ofanana ndi ife, podzitamandira chifukwa cha udindo wawo. 13  Pakuti amuna oterowo ndi atumwi onama, antchito achinyengo,+ odzisandutsa atumwi a Khristu.+ 14  Ndipo zimenezo n’zosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.+ 15  Choncho n’zosadabwitsa ngati atumiki ake+ nawonso amadzisandutsa atumiki a chilungamo. Koma mapeto awo adzakhala monga mwa ntchito zawo.+ 16  Ndikubwerezanso kunena kuti, munthu asandiyese wodzikweza. Koma ngati mukundionabe motero, ndilandirenibe monga wodzikweza yemweyo, kuti nanenso ndidzitame pang’ono.+ 17  Zimene ndikulankhulazi, ndikulankhula ngati mmene amalankhulira anthu odzitama ndiponso odzidalira kwambiri. Sindikulankhula motsatira chitsanzo cha Ambuye ayi, koma ngati mmene amalankhulira anthu opanda nzeru.+ 18  Popeza anthu ambiri akudzitama pa zinthu za m’dzikoli,+ inenso ndidzitama. 19  Pakuti mumalolera mosangalala anthu odzikweza, chifukwa mumadziona kuti ndinu ololera. 20  Ndipo mumalolera aliyense wokumangani ukapolo,+ womeza zimene muli nazo, wokulandani zimene muli nazo, wodzikweza pa inu, ndiponso aliyense wokuwombani mbama.+ 21  Ndikunena zimenezi mopeputsa ifeyo, ngati kuti ndife ofooka. Koma ngati wina aliyense akuchita chinachake molimba mtima, ndikulankhula ngati wodzitama,+ inenso ndikuchita chinthu chomwecho molimba mtima. 22  Kodi iwo ndi Aheberi? Inenso ndine Mheberi.+ Kodi ndi Aisiraeli? Inenso ndine Mwisiraeli. Kapena iwo ndi mbewu ya Abulahamu? Inenso chimodzimodzi.+ 23  Ndi atumiki a Khristu kapena? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye weniweni woposanso iwowo:+ m’ntchito zovuta mowirikiza koposa,+ m’ndende osachita kunena,+ kumenyedwa kosawerengeka, kutsala pang’ono kufa kawirikawiri.+ 24  Kasanu Ayuda anandikwapula zikoti 40+ kuchotsera chimodzi. 25  Katatu anandimenya ndi ndodo.+ Kamodzi anandiponya miyala.+ Chombo chinandiswekerapo katatu.+ Kamodzi ndinakhala pamadzi akuya usiku ndi usana wonse. 26  Pa maulendo kawirikawiri, zoopsa za m’mitsinje, zoopsa za achifwamba pamsewu,+ zoopsa zochokera kwa anthu a mtundu wanga,+ zoopsa zochokera kwa anthu a mitundu ina,+ zoopsa mumzinda,+ zoopsa m’chipululu, zoopsa za panyanja, zoopsa pakati pa abale onyenga, 27  m’ntchito yolimba ndi m’thukuta, kawirikawiri osagona tulo usiku,+ njala ndi ludzu,+ nthawi zambiri osadya chakudya,+ kuzizidwa ndi kukhala wosavala. 28  Kuwonjezera pa zinthu za kunja kwa thupi zimenezo, palinso chimene chimandivutitsa maganizo tsiku ndi tsiku, ndicho nkhawa imene ndimakhala nayo pa mipingo yonse.+ 29  Ndani ali wofooka,+ ine osakhalanso wofooka? Ndani wakhumudwitsidwa, ine osakwiya nazo? 30  Ngati ndiyenera kudzitama, ndidzadzitama+ pa zinthu zokhudza kufooka kwanga. 31  Mulungu ndi Atate wa Ambuye Yesu, amene ali woyenera kutamandidwa kwamuyaya, akudziwa kuti sindikunama. 32  Ku Damasiko, bwanamkubwa wa mfumu Areta anali kulondera mzinda wa Adamasiko kuti andigwire,+ 33  koma ndinaikidwa m’dengu n’kutsitsidwa pawindo la mpanda wa mzindawo,+ ndipo ndinapulumuka m’manja mwake.

Mawu a M'munsi