1 Yohane 5:1-21

5  Onse amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, ndi ana a Mulungu,+ ndipo onse amene amakonda Atate amakondanso mwana wake.+  Tikamakonda+ ana a Mulungu,+ ndiye kuti tikukonda Mulungu ndiponso tikusunga malamulo ake.+  Chifukwa kukonda+ Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo+ ndi osalemetsa.+  Onse amene ali ana+ a Mulungu amagonjetsa dziko.+ Ndipo tagonjetsa+ dziko ndi chikhulupiriro chathu.+  Kodi ndani amene amagonjetsa+ dziko?+ Kodi si amene amakhulupirira+ kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?+  Ameneyu ndi Yesu Khristu, amene anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi. Sanabwere kudzera mwa madzi+ okha, koma anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi.+ Ndipo mzimu+ ndi umene ukuchitira umboni, chifukwa mzimu ndiwo choonadi.  Pakuti pali mboni zitatu,  mzimu,+ madzi,+ ndi magazi,+ ndipo zitatuzi n’zogwirizana.+  Ngati timakhulupirira umboni umene anthu amapereka,+ n’zoonekeratu kuti umboni umene Mulungu amapereka ndi woposa umboni wa anthu. Timakhulupirira umboni wa Mulungu chifukwa chakuti amachitira umboni+ za Mwana wake. 10  Munthu wokhulupirira Mwana wa Mulungu ndiye kuti walandira umboni+ umene wapatsidwa. Munthu wosakhulupirira Mulungu ndiye kuti akumuona ngati wonama,+ chifukwa sanakhulupirire kuti zimene Mulungu wanena+ zokhudza Mwana wake, ndi zoona.+ 11  Umboni umene waperekedwa ndi wakuti, Mulungu anatipatsa moyo wosatha,+ ndipo tinaulandira kudzera mwa Mwana wake.+ 12  Munthu amene wavomereza Mwana ndiye kuti ali ndi moyo umenewu ndipo amene sanavomereze Mwana wa Mulungu alibe moyo umenewu.+ 13  Ndikukulemberani izi kuti mudziwe kuti inu amene mumakhulupirira m’dzina la Mwana wa Mulungu+ muli ndi moyo wosatha.+ 14  Ifetu timamudalira+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.+ 15  Komanso, popeza timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse,+ timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.+ 16  Ngati wina waona m’bale wake akuchita tchimo losabweretsa imfa,+ amupempherere, ndipo Mulungu adzamupatsa moyo.+ Panotu ndikunena za ochita machimo osabweretsa imfa.+ Koma palinso tchimo lobweretsa imfa. Ndipo sindikunena kuti mupempherere munthu amene wachita tchimo loterolo.+ 17  Kusalungama kulikonse ndi tchimo.+ Komabe pali tchimo limene silibweretsa imfa. 18  Tikudziwa kuti munthu aliyense amene ali mwana wa Mulungu+ sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, koma mwana*+ wa Mulungu amamuyang’anira, ndipo woipayo samugwira.+ 19  Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu,+ koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.+ 20  Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anabwera,+ ndipo anatipatsa nzeru+ kuti timudziwe woonayo.+ Ndipo ife ndife ogwirizana+ ndi woonayo, kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona+ ndiponso wopereka moyo wosatha.+ 21  Inu ana okondedwa, pewani mafano.+

Mawu a M'munsi

“Mwana” ameneyu ndi Yesu Khristu.