1 Yohane 3:1-24
3 Taganizirani za chikondi chachikulu+ chimene Atate watisonyeza. Watitchula kuti ndife ana a Mulungu,+ ndipo ndifedi ana ake. N’chifukwa chake dziko+ silitidziwa, pakuti silimudziwa iyeyo.+
2 Okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu,+ koma padakali pano sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani.+ Tikudziwa kuti akadzaonekera,+ tidzakhala ngati iyeyo,+ chifukwa tidzamuona mmene alili.+
3 Ndipo aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi mwa iye, amadziyeretsa+ pakuti iye ndi woyera.+
4 Aliyense amene amachita tchimo+ samvera malamulo,+ choncho tchimo+ ndilo kusamvera malamulo.
5 Inu mukudziwanso kuti iye anaonekera kuti achotse machimo athu,+ ndipo mwa iye mulibe tchimo.+
6 Aliyense amene ali wogwirizana+ ndi Yesu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo.+ Aliyense amene amachita tchimo ndiye kuti sanamuone kapena kumudziwa.+
7 Ana inu, wina asakusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama ngati mmene Yesu alili wolungama.+
8 Amene amachitabe tchimo anachokera kwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi.+ Choncho, Mwana wa Mulungu anaonekera+ kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.+
9 Aliyense amene ali mwana wa Mulungu sapitiriza kuchita tchimo,+ chifukwa mbewu ya Mulungu yopatsa moyo imakhalabe mwa munthu ameneyo, ndipo sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.+
10 Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama+ sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake.+
11 Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambira pa chiyambi,+ kuti tizikondana,+
12 osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha+ m’bale wake. N’chifukwa chiyani iye anapha m’bale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za m’bale wake zinali zolungama.+
13 Abale, musadabwe kuti dziko limakudani.+
14 Tikudziwa kuti tinali akufa koma tsopano ndife amoyo+ chifukwa timakonda abale athu.+ Amene sakonda m’bale wake ndiye kuti adakali mu imfa.+
15 Aliyense amene amadana+ ndi m’bale wake ndi wopha munthu,+ ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu+ sadzalandira moyo wosatha.+
16 Tadziwa chikondi+ chifukwa chakuti iye anapereka moyo wake chifukwa cha ife,+ ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.+
17 Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+
18 Ana anga okondedwa,+ tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha,+ koma tizisonyezana chikondi chenicheni+ m’zochita zathu.+
19 Mwa njira imeneyi tidzadziwa kuti ndife ochokera m’choonadi,+ ndipo tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu
20 pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse,+ chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.+
21 Okondedwa, ngati mitima yathu sititsutsa, tikhoza kulankhula momasuka ndi Mulungu,+
22 ndipo chilichonse chimene tingapemphe, iye adzatipatsa,+ chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zinthu zomukondweretsa.+
23 Lamulo lake ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu+ ndiponso tizikondana,+ monga mmene iye anatilamulira.
24 Komanso, munthu wosunga malamulo ake amakhalabe wogwirizana naye.+ Iyenso amakhala wogwirizana ndi munthuyo, ndipo chifukwa cha mzimu+ umene anatipatsa, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+