1 Yohane 1:1-10

1  Tikukulemberani za iye amene analiko kuyambira pa chiyambi,+ amene amabweretsa mawu opatsa moyo,+ amene tamumva+ ndiponso kumuona ndi maso athu,+ amene tamuyang’anitsitsa+ mwachidwi ndi kumukhudza ndi manja athu.+  (Ife taona ndipo tikuchitira umboni+ ndi kunena kwa inu za moyo wosatha+ umene unachokera kwa Atate ndipo unaonetsedwa kwa ife.)+  Zimene taziona ndi kuzimva, tikukuuzani+ kuti inunso mugwirizane nafe.+ Ndipotu, ifeyo ndife ogwirizana+ ndi Atate ndi Mwana wake Yesu Khristu.+  Choncho tikulemba zimenezi kuti tikhale ndi chimwemwe chachikulu.+  Umenewu ndi uthenga umene taumva kuchokera kwa iye ndipo tikuulengeza kwa inu,+ kuti Mulungu ndiye kuwala+ ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.+  Ngati tinena kuti: “Ndife ogwirizana naye,” koma tikupitiriza kuyenda mu mdima,+ ndiye kuti tikunama ndipo sitikuchita choonadi.+  Komatu, ngati tikuyenda m’kuunika ngati mmene iye alili m’kuunika,+ ndiye kuti ndife ogwirizana,+ ndipo magazi+ a Yesu Mwana wake akutiyeretsa+ ku uchimo wonse.+  Tikanena kuti: “Tilibe uchimo,”+ ndiye kuti tikudzinamiza+ ndipo mwa ife mulibe choonadi.  Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu,+ adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.+ 10  Tikanena kuti: “Sitinachimwe,” ndiye kuti tikumuchititsa iye kukhala wabodza, ndipo mawu ake sali mwa ife.+

Mawu a M'munsi