1 Timoteyo 6:1-21

6  Onse amene ali m’goli laukapolo, aziona kuti ambuye awo ndi oyenera kuwapatsa ulemu wawo wonse,+ kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitsocho asazinenere zoipa.+  Komanso, akapolo amene ambuye awo ndi okhulupirira,+ asamawapeputse+ chifukwa chakuti ndi abale.+ M’malomwake, akhale akapolo odzipereka kwambiri, pakuti amene akupindula ndi utumiki wawo wabwinowo ndi okhulupirira ndiponso okondedwa. Pitiriza kuwaphunzitsa ndi kuwadandaulira kuti azichita zimenezi.+  Ngati munthu akuphunzitsa chiphunzitso china,+ ndipo sakuvomereza mawu olondola,+ mawu a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndiponso sakuvomereza chiphunzitso chogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+  munthu ameneyo ndi wodzitukumula ndiponso wonyada,+ ndipo samvetsa kanthu kalikonse.+ M’malomwake, amakonda kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.+ Zimenezi zimayambitsa kaduka,+ mikangano, kunenerana mawu achipongwe,+ ndiponso kuganizirana zoipa.  Zimayambitsanso mapokoso achiwawa pa zinthu zazing’ono pakati pa anthu opotoka maganizo+ ndi osadziwa choonadi,+ poganiza kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi njira yopezera phindu.+  Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo,+ ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.+  Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.+  Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.+  Komabe, anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero+ ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru.+ Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.+ 10  Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+ 11  Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+ 12  Menya nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro.+ Gwira mwamphamvu moyo wosatha. Anakuitanira moyo umenewu ndipo unalengeza momveka bwino+ zinthu zokhudzana ndi moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri. 13  Pamaso pa Mulungu, amene amasunga zinthu zonse kuti zikhalebe zamoyo, ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri+ pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula+ 14  kuti usunge lamulolo. Ulisunge uli wopanda banga ndi wopanda chifukwa chokunenezera, kufikira kuonekera+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 15  Wachimwemwe ndi Wamphamvu yekhayo,+ iye amene ali Mfumu+ ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye+ wa olamulira monga ambuye, adzaonekera pa nthawi zake zoikidwiratu.+ 16  Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa,+ amene amakhala m’kuwala kosafikirika.+ Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.+ Iye apatsidwe ulemu+ ndipo mphamvu zake zikhalebe kosatha. Ame. 17  Lamula achuma+ a m’nthawi* ino kuti asakhale odzikweza,+ ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.+ 18  Uwalamule kuti azichita zabwino,+ akhale olemera pa ntchito zabwino,+ owolowa manja, okonzeka kugawira ena,+ 19  ndiponso asunge+ maziko abwino+ a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+ 20  Ndithu Timoteyo, sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.+ Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiye “kudziwa zinthu.”+ 21  Pakuti ena apatuka pa chikhulupiriro chifukwa chodzionetsera kuti ndi odziwa zinthu chonchi.+ Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.