1 Timoteyo 4:1-16

4  Komabe, mawu ouziridwa amanenadi kuti m’nthawi zam’tsogolo,+ ena adzagwa+ pa chikhulupiriro, chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso ziphunzitso za ziwanda.+  Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera+ chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.  Anthu amenewo adzaletsa anthu kukwatira,+ ndipo adzalamula anthu kusala zakudya zina+ zimene Mulungu anazilenga+ kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro ndiponso odziwa choonadi molondola azidya moyamikira.+  Ndikutero chifukwa chakuti chilichonse cholengedwa ndi Mulungu n’chabwino,+ ndipo palibe chimene chiyenera kukanidwa+ ngati chalandiridwa moyamikira,+  pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndiponso pemphero.  Chifukwa chopereka malangizo awa kwa abale, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu. Ndipo udzakula bwino ndi mawu a chikhulupiriro ndiponso chiphunzitso chabwino+ chimene wachitsatira mosamala.+  Koma uzipewa nkhani zonama+ zimene zimaipitsa zinthu zoyera ndi zimene amayi okalamba amakamba. M’malomwake, ukhale ndi chizolowezi chochita zinthu zokuthandiza kuti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.+  Pakuti kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ n’kopindulitsa m’zonse,+ chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwerawo.+  Mawu amenewa ndi oona ndipo ndi oyenera kuwalandira ndi mtima wonse.+ 10  Pa chifukwa chimenechi, tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo+ chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi+ wa anthu a mtundu uliwonse,+ koma makamaka okhulupirika.+ 11  Pitiriza kuwaphunzitsa+ ndi kuwalamula kuti azichita zimenezi.+ 12  Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono.+ M’malomwake, ukhale chitsanzo+ kwa okhulupirika+ m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.+ 13  Pamene ukundiyembekezera, pitiriza kukhala wodzipereka powerenga+ pamaso pa anthu,+ powadandaulira, ndi powaphunzitsa. 14  Usamanyalanyaze mphatso+ imene uli nayo, yomwe unapatsidwa mwaulosi+ ndiponso pamene bungwe la akulu linaika manja+ pa iwe. 15  Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.+ Dzipereke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.+ 16  Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita+ komanso zimene umaphunzitsa.+ Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.+

Mawu a M'munsi