1 Timoteyo 3:1-16

3  Mawu awa ndi oona.+ Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira,+ akufuna ntchito yabwino.  Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera,+ mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire,+ woganiza bwino,+ wadongosolo,+ wochereza alendo,+ ndiponso wotha kuphunzitsa.+  Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,*+ kapena wandewu,+ koma wololera.+ Asakhale waukali,+ kapena wokonda ndalama.+  Akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake+ ndiponso akhale woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+  (Ndithudi, ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?)  Asakhale wotembenuka kumene,+ kuopera kuti angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada,+ n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira.+  Komanso, akhale woti ngakhale anthu akunja* akumuchitira umboni wabwino,+ kuti asatonzedwe ndi kukodwa mumsampha+ wa Mdyerekezi.  Nawonso atumiki othandiza+ akhale opanda chibwana, osanena pawiri, osakonda kumwa vinyo wambiri, ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+  Akhale ogwira chikhulupiriro mwamphamvu, chimene ndi chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, ali ndi chikumbumtima choyera.+ 10  Ndiponso, amenewa ayesedwe+ kaye ngati ali oyenerera, ndiyeno atumikire monga atumiki, popeza ndi opanda chifukwa chowanenezera.+ 11  Nawonso amayi akhale opanda chibwana, osati amiseche.+ Akhale ochita zinthu mosapitirira malire,+ ndi okhulupirika m’zinthu zonse.+ 12  Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi,+ oyang’anira bwino ana awo ndi mabanja awo.+ 13  Pakuti amuna otumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino+ ndi ufulu waukulu wa kulankhula+ za chikhulupiriro, mwa Khristu Yesu. 14  Ndikukulembera zimenezi, ngakhale kuti ndikuyembekezera kuti ndibwera kwa iwe posachedwapa.+ 15  Koma ngati ndingachedwe, ndalemba izi kuti udziwe mmene uyenera kuchitira m’nyumba ya Mulungu,+ imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi umene umalimbikitsa ndi kuteteza+ choonadi. 16  Ndithudi, chinsinsi chopatulikachi+ chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu n’chachikulu ndithu: ‘Iye anaonekera ngati munthu,+ anaonedwa kuti ndi wolungama pamene anali mzimu,+ anaonekera kwa angelo,+ analalikidwa kwa mitundu ya anthu,+ anthu padziko lapansi anamukhulupirira,+ ndiponso analandiridwa kumwamba mu ulemerero.’+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “munthu womwa mowa mwauchidakwa amene amakonda kulongolola ndi kuchita ndewu akaledzera.”
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.