1 Timoteyo 2:1-15

2  Choncho, poyamba ndikuchonderera nonse kuti muzipereka mapembedzero kwa Mulungu, muzipereka mapemphero,+ muzipemphererana, ndipo muzipereka mapemphero oyamika Mulungu m’malo mwa anthu onse, kaya akhale a mtundu wotani.+  Muchite zimenezi m’malo mwa mafumu+ ndi m’malo mwa anthu onse apamwamba,+ kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso tikhale oganiza bwino.+  Zimenezi ndi zabwino ndiponso ndi zovomerezeka+ kwa Mpulumutsi wathu Mulungu,+  amene chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani,+ apulumuke+ ndi kukhala odziwa choonadi+ molondola.+  Pakuti pali Mulungu mmodzi+ ndi mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu+ ndi anthu.+ Ameneyo ndiye munthuyo Khristu Yesu.+  Iye anadzipereka kuti akhale dipo* lokwanira ndendende m’malo mwa onse.+ Zimenezi ndi zimene adzazichitire umboni pa nthawi zake.  Chifukwa cha umboni umenewu,+ ine ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki ndi mtumwi.+ Ndikunenatu zoona,+ sindikunama ayi. Ndinasankhidwa kuti ndikhale mphunzitsi wophunzitsa anthu a mitundu ina+ za chikhulupiriro+ ndi choonadi.  Choncho, ndikufuna kuti kulikonse amuna apitirize kupemphera, kukweza m’mwamba manja awo oyera+ popanda kukwiyirana+ ndi kutsutsana.+  Mofanana ndi zimenezi, ndikufunanso kuti akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu+ ndi mwanzeru, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.+ 10  Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.+ Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino.+ 11  Pophunzira, mkazi azikhala chete ndipo azikhala wogonjera ndi mtima wonse.+ 12  Sindikuvomereza kuti mkazi aziphunzitsa+ kapena kukhala ndi ulamuliro pa mwamuna,+ koma azikhala chete. 13  Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.+ 14  Komanso, Adamu sananyengedwe,+ koma mkaziyo ndiye amene ananyengedwa+ ndipo anachimwa.+ 15  Komabe, mkazi adzatetezeka mwa kubereka ana,+ malinga ngati akupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro, chikondi, ndi kukhala woyera ndiponso woganiza bwino.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.