1 Timoteyo 1:1-20

1  Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu molamulidwa ndi Mulungu+ Mpulumutsi wathu,+ ndi Khristu Yesu yemwe ali chiyembekezo chathu,+  ndikulembera iwe Timoteyo,+ mwana wanga weniweni+ m’chikhulupiriro: Kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu, zikhale nawe.+  Paja nditatsala pang’ono kupita ku Makedoniya, ndinakulimbikitsa kuti ukhalebe ku Efeso.+ Ndikukulimbikitsanso kuti ukhalebe komweko, uletse+ anthu ena ake kuti asaphunzitse chiphunzitso chosiyana ndi chathu,+  ndiponso kuti asamamvere nkhani zonama+ ndi kukumbana mibadwo ya makolo. Zimenezi n’zosapindulitsa,+ koma zimangoyambitsa mafunso ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro.  Ndithu, cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi+ chochokera mumtima woyera,+ m’chikumbumtima chabwino,+ ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.+  Anthu ena akana kutsatira zimenezi ndipo asocheretsedwa+ n’kuyamba kutsatira nkhani zopanda pake.+  Amenewa amafuna kukhala aphunzitsi+ a chilamulo+ koma sazindikira zimene akunena kapena mfundo zimene akuzilimbikira.  Tikudziwa kuti Chilamulo n’chabwino+ ngati munthu akuchigwiritsa ntchito moyenera.+  Zili choncho podziwa mfundo iyi yakuti, lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ osalamulirika,+ osaopa Mulungu, ochimwa, osakoma mtima,*+ onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu, 10  adama,+ amuna ogonana ndi amuna anzawo, oba anthu, onama, olumbira monama,+ ndiponso ochita china chilichonse chosagwirizana+ ndi chiphunzitso cholondola.+ 11  Chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero umene anauika m’manja mwanga,+ wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.+ 12  Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika,+ ndipo anandipatsa utumiki.+ 13  Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake+ ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo+ chifukwa ndinali wosadziwa+ ndi wopanda chikhulupiriro. 14  Koma ndinalandira kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu. Ndinalandiranso chikhulupiriro ndi chikondi chodzera mwa Khristu Yesu.+ 15  Mawu akuti Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse.+ Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+ 16  Komabe, anandichitira chifundo+ kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa kwambiri, kuti chikhale chitsanzo kwa amene adzamukhulupirire+ n’cholinga chakuti adzapeze moyo wosatha.+ 17  Kwa Mfumu yamuyaya,+ imene siifa,+ yosaoneka,+ yekhayo amene ali Mulungu,+ kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.+ Ame. 18  Mwana wanga Timoteyo, ndikukulamulira+ kuchita izi malinga ndi maulosi+ amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+ 19  Ukhale ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino+ chimene ena achikankhira kumbali,+ moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.+ 20  Ena mwa amenewa ndi Hemenayo+ ndi Alekizanda,+ ndipo ndawapereka kwa Satana+ kuti akalangidwa,* aphunzire kuti sayenera kulankhula zonyoza Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “opanda kukoma mtima kosatha.”
Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.