1 Samueli 9:1-27

9  Tsopano panali mwamuna wina wochokera kudera la Benjamini dzina lake Kisi,+ mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. Iye anali wa fuko la Benjamini+ ndipo anali mwamuna wachuma kwambiri.+  Iyeyu anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Sauli,+ mnyamata wokongola, ndipo panalibe munthu wina mwa ana a Isiraeli wokongola ngati iyeyu. Sauli anali wam’tali kwambiri moti panalibe munthu aliyense amene anali kum’pitirira m’mapewa ake.+  Ndiyeno abulu aakazi+ a Kisi bambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anauza Sauli mwana wake kuti: “Tenga mmodzi mwa atumikiwa ndipo upite kukafunafuna abulu aakazi.”  Ndiyeno anayenda kudutsa m’dera lamapiri la Efuraimu+ mpaka kukadutsanso m’dera la Salisa,+ koma abuluwo sanawapeze. Atatero anadutsa m’dera la Saalimu, ndipo sanawapezenso kumeneko. Kenako anadutsa m’dera la Abenjamini, koma kumenekonso sanawapeze.  Ndiyeno iwo anafika m’dera la Zufi. Pamenepo Sauli anauza mtumiki wake kuti: “Tiye tibwerere kunyumba, chifukwa bambo anga angasiye kuganizira za abulu aakazi n’kuyamba kuda nkhawa za ife.”+  Koma mtumikiyo anamuyankha kuti: “Mumzinda uwu mulitu munthu wa Mulungu,+ ndipo ndi munthu wolemekezeka. Zonse zimene wanena sizilephera, zimachitikadi.+ Ndiye tiye tipite kumeneko, mwina angatiuze kumene tingalowere.”  Koma Sauli anafunsa mtumiki wakeyo kuti: “Ndiye tikapita kumeneko tikam’patsa chiyani?+ Tilibe mphatso+ imene tingapatse munthu wa Mulungu woonayo, chifukwanso mkate watha m’zotengera zathu. Tili ndi chiyani?”  Poyankha mtumikiyo anauzanso Sauli kuti: “Inetu ndili ndi gawo limodzi mwa magawo anayi a sekeli*+ la siliva loti ndingam’patse munthu wa Mulungu woonayo ndipo adzatiuza kumene tingalowere.”  (Kalekale mu Isiraeli, munthu akafuna kukafunsira kwa Mulungu ankanena kuti: “Tiyeni tipite kwa wamasomphenya.”*+ Pakuti amene amatchedwa mneneri masiku ano, kalekalelo anali kutchedwa kuti wamasomphenya.) 10  Pamenepo Sauli anauza mtumiki wakeyo kuti: “Wanena bwino.+ Tiye tizipita.” Ndipo analowera kumzindawo, kumene kunali munthu wa Mulungu woona. 11  Pokwezeka chitunda kuti akalowe mumzindawo, iwo anakumana ndi atsikana akupita kukatunga madzi,+ ndipo anawafunsa kuti: “Kodi wamasomphenya+ alipo mumzindawu?” 12  Iwo anawayankha kuti: “Ee, alipo. Mum’peza kumene mukupitaku. Fulumirani, wafika lero mumzinda chifukwa lero anthu apereka nsembe+ pamalo okwezeka.+ 13  Mukangolowa mumzinda, mum’peza ndithu asanapite kukadya kumalo okwezeka. Anthu sangayambe kudya pokhapokha iye atafika, chifukwa ndiye amadalitsa nsembeyo.+ Kenako oitanidwa amadya. Choncho pitani chifukwa mum’peza posachedwapa.” 14  Chotero, anapita kukalowa mumzindawo. Pamene anali kuyandikira pakati pa mzinda, anangoona Samueli watulukira kudzakumana nawo kuti apite kumalo okwezeka. 15  Koma dzulo lake, Sauli asanafike, Yehova anali atauziratu+ Samueli kuti: 16  “Mawa nthawi ngati ino ndikutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini,+ ndipo udzam’dzoze+ kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli. Iye adzapulumutsa anthu anga m’manja mwa Afilisiti,+ chifukwa ndaona kusautsika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”+ 17  Samueli ataona Sauli, Yehova anamuuza kuti: “Ameneyu ndiye munthu ndimakuuza uja kuti, ‘Ameneyo ndiye adzalamulire anthu anga.’”+ 18  Pamenepo Sauli analunjika Samueli pakati pa mzinda ndi kunena kuti: “Ndifunseko, Kodi nyumba ya wamasomphenya ili kuti?” 19  Ndipo Samueli anayankha Sauli kuti: “Wamasomphenyayo ndineyo. Tsogola tipite kumalo okwezeka ndipo inuyo mudya ndi ine lero.+ Ndidzakulolani kupita mawa m’mawa, ndipo ndikuuzani zonse zimene mukufuna kudziwa.+ 20  Koma za abulu aakazi amene anasowa masiku atatu apitawo+ musadandaule,+ chifukwa anapezeka. Kodi zabwino zonse mu Isiraeli ndi za ndani?+ Kodi si zako ndi nyumba yonse ya bambo ako?” 21  Pamenepo Sauli anayankha kuti: “Kodi ine si wa m’fuko la Benjamini, fuko laling’ono kwambiri+ pa mafuko onse a Isiraeli?+ Ndipo kodi banja langa sindilo laling’ono kwambiri pa mabanja onse a m’fuko la Benjamini?+ Ndiye n’chifukwa chiyani mwalankhula mawu otere kwa ine?”+ 22  Ndiyeno Samueli anatenga Sauli pamodzi ndi mtumiki wake n’kupita nawo m’chipinda chodyera. Mmenemo anawapatsa malo apamwamba kwambiri+ pakati pa oitanidwa. M’chipindamo munali anthu 30. 23  Kenako Samueli anauza wophika kuti: “Ndipatse nyama ndinakupatsa ija, imene ndinakuuza kuti uisunge.” 24  Pamenepo wophikayo anatenga mwendo wonse n’kuuika patsogolo pa Sauli. Atatero anati: “Nyama imene inasungidwa ija ndi imeneyi. Tenga, udye chifukwa anasungira iweyo kuti udzaidye pa nthawi ino pamodzi ndi oitanidwa.” Chotero Sauli anadya pamodzi ndi Samueli pa tsikulo. 25  Zitatero, anatsika kumalo okwezeka+ aja n’kukalowa mumzinda, ndipo Samueli anapitiriza kulankhula ndi Sauli ali padenga* la nyumba.+ 26  Ndiyeno Samueli ndi Sauli anadzuka m’mawa kwambiri, m’bandakucha, ndipo Samueli, ali padenga la nyumba, anaitana Sauli ndi kumuuza kuti: “Konzekera ulendo.” Pamenepo Sauli ananyamuka ndipo onse awiri, iyeyo ndi Samueli, anatuluka kupita panja. 27  Pamene anali kupita kumalire a mzindawo, Samueli anauza Sauli kuti: “Uza mtumiki wako+ kuti atsogole, koma iwe ima kaye kuti ndikuuze mawu a Mulungu.” Atatero, mtumikiyo anatsogola.

Mawu a M'munsi

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29.
Kapena kuti “patsindwi.”