1 Samueli 7:1-17

7  Chotero amuna a ku Kiriyati-yearimu+ anabweradi ndi kutenga likasa la Yehova n’kupita nalo kwawo, ndipo analiika m’nyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Anapatula Eleazara mwana wake kuti azilondera likasa la Yehova.  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, kuchokera pamene Likasa linayamba kukhala ku Kiriyati-yearimu, panapita nthawi yaitali mpaka zinakwana zaka 20. Izi zili choncho, nyumba yonse ya Isiraeli inayamba kulirira Yehova.+  Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+  Pamenepo ana a Isiraeli anachotsa Abaala+ ndi zifaniziro za Asitoreti+ pakati pawo n’kuyamba kutumikira Yehova yekha.  Ndiyeno Samueli anawauza kuti: “Sonkhanitsani Aisiraeli onse+ pamodzi ku Mizipa,+ kuti ndikupempherereni+ kwa Yehova.”  Choncho iwo anasonkhana pamodzi ku Mizipa, ndipo anali kutunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova ndi kusala kudya tsiku limenelo.+ Ali kumeneko, anayamba kunena kuti: “Tachimwira Yehova.”+ Pamenepo, Samueli anayamba kuweruza+ ana a Isiraeli ku Mizipa.  Tsopano Afilisiti anamva kuti ana a Isiraeli asonkhana pamodzi ku Mizipa. Zitatero olamulira ogwirizana+ a Afilisiti ananyamuka kuti akamenyane ndi Isiraeli. Ana a Isiraeli atamva zimenezi, anachita mantha chifukwa cha Afilisiti.+  Chotero ana a Isiraeli anauza Samueli kuti: “Usakhale chete, koma utipempherere kwa Yehova Mulungu kuti atithandize,+ kuti atipulumutse m’manja mwa Afilisiti.”  Ndiyeno Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa ndi kum’pereka nsembe yopsereza, nsembe yathunthu,+ kwa Yehova. Atatero anayamba kupempherera Aisiraeli+ kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anamuyankha.+ 10  Pamene Samueli anali kupereka nsembe yopsereza, Afilisiti anayandikira kuti amenyane ndi Isiraeli. Zitatero, Yehova anachititsa mabingu amphamvu kwambiri+ pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.+ Choncho Afilisitiwo anagonjetsedwa pamaso pa Isiraeli.+ 11  Pamenepo amuna a Isiraeli anatuluka kuchokera ku Mizipa ndi kuthamangitsa Afilisiti, ndipo anawakantha mpaka kum’mwera kwa Beti-kara. 12  Kenako Samueli anatenga mwala+ ndi kuuimika pakati pa Mizipa ndi Yesana ndipo anautcha dzina lakuti Ebenezeri,* n’kunena kuti: “Lero Yehova watithandiza ngati kale.”+ 13  Chotero Afilisiti anagonjetsedwa ndipo sanabwerenso m’dziko la Isiraeli.+ Dzanja la Yehova linapitiriza kukankhira kutali Afilisiti masiku onse a moyo wa Samueli.+ 14  Pamenepo, mizinda imene Afilisitiwo analanda Isiraeli inayamba kubwerera kwa Isiraeli, kuyambira ku Ekironi mpaka ku Gati, ndipo Aisiraeli analanda dera la mizindayo m’manja mwa Afilisiti. Choncho panakhala mtendere pakati pa Isiraeli ndi Aamori.+ 15  Samueli anapitiriza kuweruza Isiraeli masiku onse a moyo wake.+ 16  Chaka ndi chaka Samueli anali kuzungulira m’madera a Beteli,+ Giligala+ ndi Mizipa,+ ndipo anali kuweruza+ Isiraeli m’malo onsewa. 17  Akazungulirazungulira, anali kubwerera ku Rama,+ chifukwa kumeneko n’kumene kunali nyumba yake, ndipo anali kuweruza Isiraeli ali kumeneko. Komanso iye anamangira Yehova guwa lansembe kumeneko.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Mwala wa Thandizo.” “Ebenezeri” uyu ndi wosiyana ndi amene ali pa 1Sa 4:1 ndi pa 1Sa 5:1.