1 Samueli 6:1-21

6  Likasa+ la Yehova linakhala m’dziko la Afilisiti miyezi 7.  Ndiyeno Afilisiti anaitana ansembe ndi alauli,+ ndi kuwafunsa kuti: “Kodi likasa la Yehova tichite nalo chiyani? Tiuzeni zimene tingapereke polibweza kwawo.”  Iwo anayankha kuti: “Ngati mukubweza likasa la Mulungu wa Isiraeli, musalibweze osapereka nsembe. Mulimonse mmene zingakhalire, muyenera kupereka nsembe ya kupalamula+ kwa iye. Mukatero mudzachira, ndipo mudzadziwa chifukwa chake sanali kuchotsa dzanja lake pa inu.”  Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe ya kupalamula imene tiyenera kupereka ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi alauli aja anati: “Mupereke zifanizo zisanu zagolide za matenda a mudzi, ndi zifanizo zisanu zagolide za mbewa zoyenda modumpha, malinga ndi chiwerengero cha olamulira ogwirizana+ a Afilisiti. Muchite zimenezi pakuti mliri umene wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu ogwirizana ndi umodzi.  Ndipo muyenera kupanga zifanizo za matenda anu a mudzi ndi zifanizo za mbewa zoyenda modumpha+ zimene zikuwononga dziko, ndipo mupereke ulemerero+ kwa Mulungu wa Isiraeli. Mukatero, mwina adzachepetsako mphamvu ya dzanja lake pa inu, mulungu wanu ndi dziko lanu.+  Komanso, mukuumitsiranji mitima yanu mmene Aiguputo ndi Farao anaumitsira mitima yawo?+ Si paja Mulungu atangowakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita, ndipo iwo anapitadi?+  Choncho pangani ngolo+ yatsopano, ndipo mutenge ng’ombe ziwiri zoyamwitsa zimene sizinanyamulepo goli+ ndi kuzimangirira kungoloyo. Ana a ng’ombezo muwabweze kunyumba kuti asatsatire amayi awo.  Ndiyeno mutenge likasa la Yehova ndi kuliika m’ngoloyo. Zinthu zagolide+ zimene muyenera kupereka monga nsembe ya kupalamula+ muziike m’bokosi lina pambali pa likasa, kenako mulitumize, ndipo lichoke.  Ndiyeno muonetsetse izi: Likasalo likadzalowera njira yopita kwawo, ku Beti-semesi,+ ndiye kuti iye ndi amenedi watichitira choipa chachikuluchi. Koma ngati sililowera kumeneko, tidziwa kuti si dzanja lake limene latikhudza, koma ngozi+ yangotigwera.” 10  Chotero anthuwo anachitadi zomwezo. Anatenga ng’ombe ziwiri zoyamwitsa n’kuzimangirira kungoloyo, ndipo ana a ng’ombezo anawatsekera kunyumba. 11  Ndiyeno anaika likasa la Yehova m’ngoloyo.+ Anaikamonso bokosi lina lija lokhala ndi mbewa zoyenda modumpha zagolide ndi zifanizo za matenda awo a mudzi. 12  Ng’ombezo zinayamba kuyenda, kulunjika msewu wa ku Beti-semesi.+ Zinali kuyenda pamsewu waukulu wopita kumeneko zikulira, ndipo sizinapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. Apa n’kuti olamulira ogwirizana+ a Afilisiti akuzitsatira pambuyo mpaka kukafika m’malire a Beti-semesi. 13  Anthu a ku Beti-semesi anali kukolola tirigu+ m’chigwa. Atakweza maso ndi kuona Likasa, anasangalala kwambiri. 14  Ngoloyo inafika m’munda wa Yoswa, amene kwawo kunali ku Beti-semesi, ndi kuima pamalo pamene panali mwala waukulu. Ndiyeno anthuwo anawaza matabwa a ngoloyo ndipo ng’ombezo+ anazipereka nsembe yopsereza kwa Yehova.+ 15  Tsopano Alevi+ anatsitsa likasa la Yehova, pamodzi ndi bokosi lina lija mmene munali zinthu zagolide, n’kuliika pamwala waukulu uja. Kenako amuna a ku Beti-semesi+ anapereka nsembe zopsereza, ndipo anapitiriza kupereka nsembe kwa Yehova tsiku limenelo. 16  Olamulira asanu ogwirizana+ a Afilisiti aja anaona zimenezo ndipo anabwerera ku Ekironi tsiku limenelo. 17  Ndiyeno zifanizo zagolide za matenda a mudzi zimene Afilisiti anapereka kwa Yehova monga nsembe ya kupalamula ndi izi:+ mzinda wa Asidodi+ unapereka chifanizo chimodzi, wa Gaza+ chimodzi, wa Asikeloni+ chimodzi, wa Gati+ chimodzi ndi wa Ekironi+ chimodzi. 18  Chiwerengero cha mbewa zoyenda modumpha zagolide chinali chofanana ndi mizinda yonse ya Afilisiti ya olamulira asanu ogwirizana, kuyambira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mpaka ku mudzi wopanda mpanda. Mwala waukulu umene anakhazikapo likasa la Yehova ndiwo mboni mpaka lero m’munda wa Yoswa, amene kwawo kunali ku Beti-semesi. 19  Chotero Mulungu anakantha anthu a ku Beti-semesi,+ chifukwa anayang’anitsitsa likasa la Yehova. Anakantha anthu 70 [[anthu 50,000]]* pakati pawo, ndipo anthu anayamba kulira chifukwa Yehova anakantha anthuwo koopsa.+ 20  Kenako amuna a ku Beti-semesi ananena kuti: “Ndani angaime pamaso pa Yehova Mulungu woyera,+ ndipo kodi sangatileke n’kupita kwa ena?”+ 21  Pamapeto pake anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-yearimu+ kuti: “Afilisiti abweza likasa la Yehova, bwerani kuno mudzalitenge.”+

Mawu a M'munsi

Ena amaganiza kuti mawu akuti “anthu 50,000” anachita kuwawonjezera pambuyo pake.