1 Samueli 5:1-12

5  Tsopano Afilisiti anatenga likasa+ la Mulungu woona kuchoka nalo ku Ebenezeri n’kupita nalo ku Asidodi.+  Kumeneko anatenga likasa la Mulungu woona ndi kulilowetsa m’nyumba ya Dagoni, n’kuliika pafupi ndi fano la Dagonilo.+  Tsiku lotsatira Aasidodi anadzuka m’mawa kwambiri, ndipo anapeza Dagoni atagwa pansi chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova.+ Zitatero, anatenga Dagoni ndi kumubwezeretsa pamalo ake.+  Atadzuka m’mawa kwambiri tsiku lotsatira, anapezanso kuti Dagoni wagwa pansi chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Anapeza mutu wa Dagoni ndi zikhatho zake zitaduka ndi kugwera pakhomo.+ Mbali yooneka ngati nsomba* ndi imene inatsala.  N’chifukwa chake ansembe a Dagoni ndi anthu onse olowa m’nyumba ya Dagoni ku Asidodi saponda pakhomo la nyumba ya Dagoni mpaka lero.  Ndiyeno dzanja la Yehova+ linakhala lamphamvu kwambiri pa Aasidodi, kutanthauza mzinda wa Asidodi ndi madera ake ozungulira, ndipo anayamba kuwasautsa ndi kuwakantha ndi matenda a mudzi.*+  Anthu a ku Asidodi ataona kuti zafika pamenepo, anati: “Musalole kuti likasa la Mulungu wa Isiraeli likhale ndi ife kuno, chifukwa dzanja lake latisautsa kwambiri pamodzi ndi Dagoni mulungu wathu.”+  Chotero anatumiza uthenga ndi kusonkhanitsa olamulira onse ogwirizana a Afilisiti ku Asidodi ndi kuwauza kuti: “Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Isiraeli?” Pamapeto pake iwo anati: “Likasa limeneli la Mulungu wa Isiraeli tilitumize kumzinda wa Gati.”+ Choncho anapititsa likasa la Mulungu wa Isiraeli kumeneko atayenda nalo mozungulira.  Kenako zimene zinachitika n’zakuti, atazungulira ndi likasalo n’kufika nalo kumeneko, dzanja la Yehova+ linasautsanso mzindawo ndi chisokonezo chachikulu kwambiri. Iye anayamba kukantha anthu onse a mumzindawo, osasiyapo aliyense moti onsewo anagwidwa ndi matenda a mudzi.+ 10  Choncho anatumiza likasa la Mulungu woona ku Ekironi.+ Ndiyeno likasa la Mulungu woona litangofika ku Ekironi, anthu a ku Ekironi anayamba kulira, kuti: “Atibweretsera likasa la Mulungu wa Isiraeli kuti atiphe ife tonse!”+ 11  Chotero anatumiza uthenga ndi kusonkhanitsa olamulira onse ogwirizana a Afilisiti, n’kuwauza kuti: “Chotsani likasa la Mulungu wa Isiraeli pakati pathu, libwerere kwawo kuti lisatiphe.” Ananena zimenezi chifukwa mumzinda wonsewo+ anthu anali kuopa kuti afa, pakuti dzanja la Mulungu woona linali kuwasautsa kumeneko.+ 12  Anthu amene sanafe anakanthidwa ndi matenda a mudzi.+ Ndipo anthu a mumzindawo anayang’ana kumwamba, kulirira+ thandizo.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mbali yooneka ngati nsomba,” mawu ake enieni ndi “Dagoni yekha,” pakuti zikuoneka kuti fano la Dagoni linali mbali ina munthu mbali ina nsomba.
Onani mawu a m’munsi pa De 28:27.