1 Samueli 4:1-22

4  Samueli anapitiriza kulankhula ndi Aisiraeli onse. Tsopano Aisiraeli anapita kukamenyana ndi Afilisiti. Choncho anamanga msasa pafupi ndi Ebenezeri,+ ndipo Afilisiti nawonso anamanga msasa ku Afeki.+  Afilisitiwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo+ kuti amenyane ndi Aisiraeli. Nkhondoyo sinawayendere bwino Aisiraeli, moti anagonjetsedwa ndi Afilisiti.+ Iwo anakantha amuna achiisiraeli pafupifupi 4,000 nkhondoyo ili mkati.  Ndiyeno anthuwo atabwerera kumsasa, akulu a Isiraeli anayamba kunena kuti: “N’chifukwa chiyani lero Yehova watigonjetsa pamaso pa Afilisiti?+ Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova+ ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.”  Motero anthuwo anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa makamu, amene akukhala pa akerubi.+ Ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anali pamenepo ndi likasa la pangano la Mulungu woona.+  Likasa la pangano la Yehova litafika mumsasa, Aisiraeli onse anafuula mokweza kwambiri,+ moti kunali chisokonezo m’dziko lonse.  Nawonso Afilisiti anamva phokoso la kukuwa, ndipo anayamba kufunsa kuti: “Kodi phokoso+ limeneli mumsasa wa Aheberi likutanthauza chiyani?” Pamapeto pake, anamva kuti likasa la Yehova labwera mumsasawo.  Pamenepo Afilisitiwo anachita mantha, ndipo anati: “Mulungu wafika mumsasa wawo!”+ Ndiyeno anati: “Tsoka latigwera, pakuti zinthu zotere sizinachitikepo ndi kale lonse!  Tsoka ife! Adzatipulumutsa ndani m’manja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anakantha Iguputo ndi masautso amtundu uliwonse m’chipululu.+  Limbani mtima ndi kuchita chamuna Afilisitinu, kuti musatumikire Aheberi ngati mmene iwo akutumikirirani.+ Chitani chamuna ndi kumenya nkhondo!” 10  Chotero Afilisiti anamenyadi nkhondo, ndipo Aisiraeli anagonja+ moti aliyense wa iwo anayamba kuthawira kuhema wake.+ Ndipo amene anaphedwa anali ochuluka kwambiri.+ Panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanira 30,000.+ 11  Ngakhalenso likasa la Mulungu linalandidwa,+ ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anafa.+ 12  Tsopano mwamuna wina wa fuko la Benjamini anathamanga kuchoka kumalo ankhondowo kukafika ku Silo tsiku limenelo, atang’amba zovala zake+ ndi kudzithira dothi kumutu.+ 13  Atafika, anapeza Eli atakhala pampando m’mbali mwa msewu, maso ali kunjira, pakuti anali kuchita mantha mumtima mwake chifukwa cha likasa la Mulungu woona.+ Ndiyeno mwamunayo analowa mumzindawo kukanena za nkhondoyo, ndipo anthu onse mumzindawo anayamba kulira. 14  Choncho Eli anamva phokoso la kulira kwa anthuwo, ndipo anati: “Kodi chisokonezo chikuchitika kumeneku n’chachiyani?”+ Kenako mwamuna uja anathamanga kukauza Eli. 15  (Eli anali ndi zaka 98, ndipo maso ake anangokhala tong’o koma sanali kuona.)+ 16  Tsopano mwamuna uja anauza Eli kuti: “Ine ndikuchokera kumalo omenyera nkhondo, ndithudi ndachita kuthawa kumeneko lero.” Pamenepo Eli anam’funsa kuti: “Chachitika n’chiyani mwana wanga?” 17  Choncho munthu wobweretsa uthengayo anayankha kuti: “Aisiraeli athawa pamaso pa Afilisiti, ndipo agonjetsedwa koopsa.+ Ana anunso awiri, Hofeni ndi Pinihasi,+ aphedwa. Ngakhalenso likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+ 18  Ndiyeno mwamunayo atangotchula za likasa la Mulungu woona, Eli anagwa chagada kuchoka pampando, ali pachipatapo. Chotero khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali wokalamba ndi wonenepa kwambiri. Eli anali ataweruza Isiraeli zaka 40. 19  Mpongozi wake, mkazi wa Pinihasi, anali ndi pakati moti anali pafupi kubereka. Ndiyeno anamva kuti likasa la Mulungu woona lalandidwa ndipo apongozi ake ndi mwamuna wake afa. Zitatero, anawerama n’kuyamba kubereka, chifukwa zowawa za pobereka zinam’fikira mwadzidzidzi.+ 20  Mkaziyu atatsala pang’ono kumwalira, amayi amene anaima pambali pake anayamba kulankhula kuti: “Usachite mantha, pakuti wabereka mwana wamwamuna.”+ Koma iye sanayankhe kapena kuikirapo mtima. 21  Iye anatcha mwanayo kuti Ikabodi,*+ n’kunena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.”+ Ananena zimenezi chifukwa cha likasa la Mulungu woona limene linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha apongozi ake ndi mwamuna wake.+ 22  Choncho ananena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina,+ chifukwa likasa la Mulungu woona lalandidwa.”+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Ulemerero Uli Kuti?”