1 Samueli 31:1-13

31  Tsopano Afilisiti anali kumenyana ndi Isiraeli,+ ndipo amuna a Isiraeli anathawa pamaso pa Afilisiti, moti anali kuphedwa+ m’phiri la Giliboa.+  Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo pamapeto pake anapha Yonatani,+ Abinadabu+ ndi Malikisuwa,+ ana aamuna a Sauli.  Nkhondo inam’kulira kwambiri Sauli, moti pamapeto pake oponya mivi ndi uta anamupeza ndipo anamuvulaza koopsa.+  Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+  Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa,+ nayenso anagwera palupanga lake ndipo anafera limodzi.+  Chotero Sauli, ana ake atatu, ndi womunyamulira zida komanso asilikali ake onse, anafera limodzi pa tsiku limenelo.+  Amuna a Isiraeli amene anali m’dera la m’chigwa ndiponso m’dera la Yorodano ataona kuti asilikali a Isiraeli athawa komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuchoka m’mizinda yawo ndi kuthawa.+ Kenaka Afilisiti anabwera n’kuyamba kukhala m’mizindayo.+  Ndiyeno tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzavula zovala anthu ophedwa,+ anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa paphiri la Giliboa.+  Iwo anadula mutu wa Sauli+ ndi kumuvula zida zake. Kenako anatumiza uthenga+ m’dziko lonse la Afilisiti, kunyumba za mafano awo+ ndi kwa anthu awo. 10  Pamapeto pake, anakaika zida zakezo+ m’nyumba ya zifaniziro za Asitoreti,+ ndipo anapachika mtembo wake pakhoma mumzinda wa Beti-sani.+ 11  Choncho, anthu okhala mumzinda wa Yabesi-giliyadi+ anamva zimene Afilisiti anamuchita Sauli. 12  Nthawi yomweyo, amuna olimba mtima ananyamuka ndi kuyenda usiku wonse kukachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pakhoma la ku Beti-sani. Kenako anabwerera ku Yabesi ndi kutentha mitemboyo kumeneko.+ 13  Atatero, anatenga mafupa awo+ ndi kuwaika m’manda+ pansi pa mtengo wa bwemba+ ku Yabesi. Pambuyo pake, anasala kudya masiku 7.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kugwaza.”