1 Samueli 30:1-31

30  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Davide ndi asilikali ake anali kubwerera ku Zikilaga+ tsiku lachitatu, Aamaleki+ anaukira anthu a kum’mwera* ndi a mumzinda wa Zikilaga ndi kufunkha zinthu zawo. Iwo anathira nkhondo mzindawo ndi kuutentha ndi moto.  Aamalekiwo anatenga akazi+ a mumzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo. Sanaphe aliyense koma anawatenga ndi kupita nawo.  Davide atafika mumzindawo pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye, anangoona kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo aamuna ndi ana awo aakazi agwidwa ndi kutengedwa.  Pamenepo Davide ndi anthu amene anali naye anayamba kulira mofuula+ mpaka kulefuka osathanso kulira.  Akazi awiri a Davide nawonso anali atatengedwa, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala.  Zimenezi zinam’vutitsa maganizo kwambiri Davide+ chifukwanso anthu anali kukambirana zom’ponya miyala.+ Anthuwo anali kukambirana zimenezi chifukwa aliyense wa iwo anali wokwiya kwambiri+ poona zimene zachitikira ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Choncho, Davide anadzilimbitsa mwa Yehova Mulungu wake.+  Zitatero, Davide anauza Abiyatara+ wansembe, mwana wa Ahimeleki kuti: “Chonde, bweretsa efodi+ kuno.” Pamenepo Abiyatara anapereka efodi kwa Davide.  Ndiyeno Davide anayamba kufunsira kwa Yehova,+ kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali? Kodi ndiwapeza?” Pamenepo anamuyankha+ kuti: “Inde athamangitse chifukwa uwapezadi ndi kulanditsa zinthu zimene afunkha.”+  Mwamsanga, Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna 600+ amene anali kuyenda naye. Iwo anayenda mpaka kukafika kuchigwa* cha Besori, ndipo amuna ena anatsala pamenepo. 10  Davide pamodzi ndi amuna 400 anapitiriza kuwathamangitsa,+ koma amuna 200 amene anatopa kwambiri ndipo sanathe kuwoloka chigwa cha Besori+ anaima pomwepo. 11  Ndiyeno anapeza mwamuna wina wa ku Iguputo+ patchire. Choncho anamutengera kwa Davide ndi kumupatsa mkate kuti adye ndi madzi kuti amwe. 12  Anamupatsanso chidutswa cha nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndi zidutswa ziwiri za mphesa zouma zoumba pamodzi.+ Iye anadya ndipo anapezanso mphamvu,+ chifukwa sanadye mkate kapena kumwa madzi kwa masiku atatu, usana ndi usiku. 13  Ndiyeno Davide anamufunsa kuti: “Uli mbali ya ndani, ndipo kwanu n’kuti?” Mwamunayo anayankha kuti: “Ndine Mwiguputo, kapolo wa Mwamaleki, koma mbuyanga anandisiya pano masiku atatu apitawa chifukwa cha kudwala.+ 14  Ndife amene tinakaukira kum’mwera kwa dziko la Akereti+ ndi dera la Yuda komanso kum’mwera kwa dera la Kalebe.+ Ndipo mzinda wa Zikilaga tinautentha ndi moto.” 15  Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Kodi ungandiperekeze kumene kuli gulu la achifwambali?” Poyankha, iye anati: “Ndilumbirire+ pamaso pa Mulungu kuti sundipha, komanso kuti sundipereka m’manja mwa mbuyanga.+ Ukatero ndikuperekeza kumene kuli gulu la achifwambali.” 16  Chotero mwamunayo anaperekeza+ Davide ndi kupita kumene kunali achifwambawo, ndipo anawapeza atamwazikana m’dziko lonselo, akudya ndi kumwa, kuchita chiphwando+ chifukwa chakuti anafunkha zinthu zambiri m’dziko la Afilisiti ndi la Yuda.+ 17  Ndiyeno Davide anawakantha ndi kuwawononga, kuyambira m’bandakucha kufikira madzulo. Palibe aliyense wa iwo amene anathawa,+ kupatulapo anyamata 400 amene anakwera ngamila n’kuthawa. 18  Davide analanditsa zonse zimene Aamaleki anatenga,+ n’kulanditsanso akazi ake awiri aja. 19  Palibe chinthu chawo chilichonse chimene chinasowa, ana aamuna kapena ana aakazi, ngakhalenso zinthu zimene anafunkha kwa iwo komanso chilichonse chimene anawatengera.+ Davide analanditsa zonsezo. 20  Choncho Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng’ombe zonse za Aamaleki komanso ziweto zonse zimene Aamaleki anawalanda. Kenako iwo anati: “Izi ndi zofunkha za Davide.”+ 21  Patapita nthawi, Davide anafika kwa amuna 200+ amene anawasiya kuchigwa cha Besori, amene sanathe kupita ndi Davide pakuti anali otopa kwambiri. Pamenepo iwo ananyamuka kudzakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye. Davide atawayandikira, anawafunsa za moyo wawo. 22  Koma mwamuna aliyense woipa ndi wopanda pake+ mwa amuna onse amene anatsatira Davide anayamba kunena kuti: “Chifukwa chakuti amenewa sanapite nafe, sitiwapatsa zofunkha zimene talanditsazi. Koma aliyense tingomupatsa mkazi wake ndi ana ake basi, awatenge ndipo azipita.” 23  Koma Davide anati: “Ayi abale anga, musatero ndi zinthu zimene Yehova watipatsa.+ Iye watiteteza+ ndi kupereka m’manja mwathu gulu la achifwamba limene linadzatiukira.+ 24  Ndani angamve zimene mukunenazo? Pakuti gawo limene munthu amene anapita kunkhondo alandire, likhala lofanana ndi gawo limene munthu amene anali kulondera katundu alandire.+ Aliyense alandirapo kenakake.”+ 25  Ndiyeno kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo, limeneli linakhala lamulo ndi chigamulo+ kwa Aisiraeli kufikira lero. 26  Davide atafika ku Zikilaga anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa mabwenzi ake,+ akulu a ku Yuda, n’kunena kuti: “Landirani mphatso*+ iyi kuchokera pa zimene tafunkha kwa adani a Yehova.” 27  Anatumiza zimenezi kwa akulu a ku Beteli,+ a ku Ramoti+ wakum’mwera, a ku Yatiri,+ 28  a ku Aroweli, a ku Sifimoti, a ku Esitemowa,+ 29  ndi a ku Rakala. Anatumizanso zimenezi kwa akulu okhala m’mizinda ya Ayerameeli+ ndi m’mizinda ya Akeni,+ 30  komanso kwa akulu a ku Horima,+ a ku Borasani,+ a ku Ataki, 31  a ku Heburoni+ ndi kumalo onse kumene Davide anafikako pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye.

Mawu a M'munsi

Kumeneku ndi kum’mwera kwa Yuda.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Kapena kuti “dalitso.”