1 Samueli 3:1-21

3  Zili choncho, mwanayo Samueli anali kutumikira+ Yehova pamaso pa Eli, ndipo mawu a Yehova+ anali osowa masiku amenewo,+ moti masomphenya sanali kuonekaoneka.+  Ndiyeno tsiku lina Eli anali atagona m’chipinda chake. Pa nthawiyi, maso ake anali atayamba kuchita mdima+ moti sanali kuona.  Nyale ya Mulungu inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona m’kachisi+ wa Yehova, mmene munali likasa la Mulungu.  Ndiyeno Yehova anayamba kuitana Samueli. Ndipo Samueli anayankha kuti: “Ine mbuyanga.”+  Pamenepo anathamangira kwa Eli, n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane. Pita ukagone.” Choncho Samueli anapita kukagonanso.  Ndiyeno Yehova anamuitananso, kuti: “Samueli!”+ Pamenepo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli, n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, chifukwa ndamva kuitana ndithu.” Koma Eli anamuuza kuti: “Sindinakuitane mwana wanga.+ Pita ukagone.”  (Pa nthawiyi Samueli anali asanadziwe Yehova, ndipo anali asanayambe kulandira mawu a Yehova.)+  Ndiyeno Yehova anaitananso kachitatu kuti: “Samueli!” Pamenepo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli, n’kunenanso kuti: “Ndabwera, chifukwa mwandiitana ndithu.” Atatero, Eli anazindikira kuti Yehova ndi amene anali kuitana mwanayo.  Chotero Eli anauza Samueli kuti: “Pita ukagone, ndipo akakuitananso unene kuti, ‘Lankhulani Yehova, chifukwa ine mtumiki wanu ndikumvetsera.’” Choncho Samueli anapita kukagona m’chipinda chake. 10  Kenako Yehova anabwera ndi kuima pamalopo n’kuitananso ngati poyamba paja, kuti: “Samueli, Samueli!” Poyankha Samueli anati: “Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumvetsera.”+ 11  Pamenepo Yehova anayamba kuuza Samueli kuti: “Tamvera! Ndichita+ zinazake mu Isiraeli zoti munthu aliyense akadzamva m’makutu ake onse mudzalira!+ 12  Tsiku limenelo ndidzachitira Eli zonse zimene ndinanena, zoyambirira mpaka zomalizira, zokhudza nyumba yake.+ 13  Umuuze kuti ndidzaweruza nyumba yake+ mpaka kalekale chifukwa cha cholakwa ichi: Iye akudziwa+ kuti ana ake akunyoza Mulungu+ koma sakuwadzudzula.+ 14  N’chifukwa chake ndalumbirira a m’nyumba ya Eli kuti mpaka kalekale sadzapewa chilango chifukwa cha cholakwa cha anthu a m’nyumba yakewo, ngakhale atapereka nsembe.”+ 15  Ndiyeno Samueli anagonabe mpaka m’mawa. Atadzuka anatsegula zitseko za nyumba ya Yehova,+ koma anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.+ 16  Tsopano Eli anaitana Samueli, n’kunena kuti: “Samueli, mwana wanga!” Ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.” 17  Ndiyeno Eli anamuuza kuti: “Kodi Mulungu wakuuza chiyani? Chonde usandibisire ayi.+ Mulungu akulange ndi kuwonjezerapo,+ ukandibisira ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene iye wakuuza.” 18  Choncho Samueli anamuuza mawu onse ndipo sanam’bisire kanthu. Pamenepo Eli anati: “Ndi Yehova amene wanena. Achite zimene akuona kuti n’zabwino.”+ 19  Samueli anapitiriza kukula ndipo Yehova anali naye,+ moti palibe mawu ake alionse amene anapita padera.+ 20  Tsopano Aisiraeli onse kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba,+ anadziwa kuti Samueli ndiye anali wovomerezeka kukhala mneneri wa Yehova.+ 21  Ndipo Yehova anaonekeranso+ ku Silo, pakuti n’kumene Yehova anadzisonyeza kwa Samueli mwa mawu a Yehova.+

Mawu a M'munsi