1 Samueli 29:1-11

29  Ndiyeno Afilisiti+ anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, pamene Aisiraeli anamanga msasa pafupi ndi kasupe amene anali ku Yezereeli.+  Olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anali kudutsa m’magulu a asilikali 100, ndi 1,000, ndipo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anadutsa pambuyo pawo limodzi ndi Akisi.+  Ndiyeno akalonga a Afilisiti anayamba kunena kuti: “Kodi Aheberi+ awa akufuna chiyani kuno?” Pamenepo Akisi anayankha akalonga a Afilisitiwo kuti: “Kodi uyu si Davide, mtumiki wa Sauli, mfumu ya Isiraeli? Iyetu wakhala ndi ine kuno kwa chaka chimodzi kapena ziwiri,+ ndipo kuyambira tsiku limene anathawira kwa ine kufikira lero, sindinam’peze+ ndi chifukwa ngakhale chimodzi.”  Pamenepo akalonga a Afilisiti anam’psera mtima kwambiri Akisi, ndipo anati: “Muuze abwerere,+ apite kumalo amene unam’patsa. Usamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa angakatitembenukire+ kumeneko. Ukuganiza kuti munthu ameneyu adzakometsera dzina lake ndi chiyani kwa mbuye wake? Si mitu ya asilikali athu kodi?  Kodi uyu si Davide uja amene ankamuimbira nyimbo molandizana mawu, akuvina n’kumati, ‘Sauli wakantha adani ake masauzande, ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi’?”+  Choncho Akisi+ anaitana Davide ndi kumuuza kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ iweyo ndiwe wowongoka mtima, ndipo ndasangalala+ kuti wabwera nane+ kunkhondo, pakuti sindinapeze choipa chilichonse mwa iwe kuyambira tsiku limene unabwera kwa ine kufikira lero.+ Koma olamulira ogwirizana+ sakukuona bwino.  Choncho, bwerera mwamtendere, kuti usachite chilichonse chimene olamulira ogwirizana a Afilisiti angachione kukhala choipa.”  Koma Davide anayankha Akisi kuti: “Ndibwerere chifukwa chiyani? Ndalakwa chiyani,+ ndipo mwapeza chiyani mwa ine mtumiki wanu kuchokera pa tsiku limene ndinabwera kudzakhala nanu kufikira lero,+ kuti ndisapite kukamenyana ndi adani anu mbuyanga mfumu?”  Pamenepo Akisi anayankha Davide kuti: “Ndikudziwa bwino kuti wakhala ukundichitira zinthu zabwino, ngati mngelo wa Mulungu.+ Koma akalonga a Afilisiti ndi amene anena kuti, ‘Musalole kuti ameneyu apite nafe kunkhondo.’ 10  Choncho udzuke m’mawa kwambiri pamodzi ndi atumiki a mbuye wako amene anabwera nawe pamodzi. Mukangoona kuti kwayera mudzuke ndi kunyamuka.”+ 11  Chotero Davide anadzuka m’mawa kwambiri+ pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye ndi kubwerera kudziko la Afilisiti m’mawa umenewo. Koma Afilisitiwo anapita ku Yezereeli.+

Mawu a M'munsi