1 Samueli 28:1-25

28  Ndiyeno masiku amenewo zinachitika kuti Afilisiti anayamba kusonkhanitsa asilikali awo kuti akamenyane ndi Isiraeli.+ Choncho, Akisi anauza Davide kuti: “Ndikukhulupirira kuti ukudziwa kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita ndi ine kunkhondo.”+  Pamenepo Davide anauza Akisi kuti: “Ndiponso inu mukudziwa bwino zimene mtumiki wanu ayenera kuchita.” Chotero Akisi anauza Davide kuti: “Ndidzakuika kukhala msilikali wondilondera nthawi zonse.”+  Tsopano Samueli anali atamwalira ndipo Aisiraeli anali atamulira ndi kumuika m’manda mumzinda wakwawo ku Rama.+ Ndipo Sauli anali atachotsa anthu olankhula ndi mizimu ndi akatswiri olosera zam’tsogolo m’dzikolo.+  Ndiyeno Afilisiti anasonkhana pamodzi ndi kupita kukamanga msasa ku Sunemu.+ Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisiraeli onse pamodzi ndi kumanga msasa ku Giliboa.+  Sauli ataona msasa wa Afilisiti anachita mantha kwambiri ndipo mtima wake unayamba kugunda.+  Ngakhale kuti anali kufunsira kwa Yehova,+ Yehova sanamuyankhe+ kaya kudzera m’maloto,+ Urimu+ kapena kudzera mwa aneneri.+  Pamapeto pake, Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mkazi waluso polankhula ndi mizimu,+ ndipo ine ndipita kukalankhula naye.” Pamenepo atumiki ake anamuuza kuti: “Ku Eni-dori alipo mkazi waluso polankhula ndi mizimu.”+  Choncho Sauli anadzisintha+ ndi kuvala zovala zina. Atatero, iyeyo ndi amuna ena awiri anapita kwa mkaziyo ndipo anafikako usiku.+ Ndiyeno Sauliyo anati: “Ndiloserere zam’tsogolo+ mwa kulankhula ndi mizimu ndipo undiutsire munthu amene ndikuuze.”  Koma mkaziyo anauza Sauli kuti: “Iwe ukudziwa bwino zimene Sauli anachita. Ukudziwa kuti m’dziko lino anachotsamo anthu olankhula ndi mizimu ndiponso akatswiri olosera zam’tsogolo.+ Ndiye n’chifukwa chiyani ukufuna kunditchera msampha kuti ndiphedwe?”+ 10  Nthawi yomweyo, Sauli anamulumbirira m’dzina la Yehova kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ sukhala ndi mlandu chifukwa cha nkhani imeneyi!” 11  Pamenepo mkaziyo anati: “Ukufuna ndikuutsire ndani?” Poyankha Sauli anati: “Ndiutsire Samueli.”+ 12  Mkaziyo ataona “Samueli”*+ anayamba kulira mofuula kwambiri. Kenako mkaziyo anauza Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani mwandipusitsa, pamene inuyo ndinu Sauli amene?” 13  Koma mfumu inamuuza kuti: “Usachite mantha. Waona chiyani?” Mkaziyo anayankha Sauli kuti: “Ndaona mulungu+ akutuluka m’nthaka.” 14  Nthawi yomweyo Sauli anafunsa mkaziyo kuti: “Akuoneka bwanji?” Ndipo mkaziyo anayankha kuti: “Amene watulukayu akuoneka kuti ndi mwamuna wokalamba ndipo wavala malaya akunja odula manja.”+ Atamva zimenezi, Sauli anazindikira kuti ameneyo ndi “Samueli”+ ndipo Sauliyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi, kenako anagona pansi. 15  Pamenepo “Samueli” anafunsa Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani wandisokoneza ndi kundidzutsa?”+ Sauli anayankha kuti: “Zinthu zandivuta kwambiri,+ pakuti Afilisiti akumenyana nane ndipo Mulungu wandichokera+ moti sakundiyankhanso, kaya kudzera mwa aneneri kapena m’maloto.+ N’chifukwa chake ndabwera kudzafunsa inu kuti mundiuze zimene ndiyenera kuchita.”+ 16  Ndiyeno “Samueli” anamuyankha kuti: “Ndiye ukudzandifunsiranji pamene Yehova wakuchokera+ ndipo wakhala mdani wako?+ 17  Yehova achitadi zimene ananena kudzera mwa ine, ndipo Yehova ang’amba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe+ ndi kuupereka kwa mnzako Davide.+ 18  Achita zimenezi chifukwa sunamvere mawu a Yehova,+ ndipo sunasonyeze mkwiyo wake woyaka moto umene anali nawo pa Amaleki.+ N’chifukwa chaketu lero Yehova achite zimenezi kwa iwe. 19  Yehova aperekanso Isiraeli pamodzi ndi iwe m’manja mwa Afilisiti,+ moti mawa iweyo+ ndi ana ako+ mukhala ndi ine. Komanso Yehova aperekadi asilikali a Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.”+ 20  Sauli atamva zimenezi, anadzigwetsa mofulumira ndi kugona pansi mantha atamugwira kwambiri chifukwa cha mawu a “Samueli.” Komanso analefuka kwambiri chifukwa chakuti sanadye chakudya masana onse ndi usiku wonse. 21  Ndiyeno mkazi uja anapita pamene panali Sauli ndipo anaona kuti wathedwa nzeru kwambiri. Choncho anamuuza kuti: “Ineyo mtumiki wanu ndamvera mawu anu ndipo ndaika moyo wanga pangozi*+ pomvera mawu amene mwandiuza. 22  Tsopano inunso, chonde, mverani mawu a ine mtumiki wanu. Ndiloleni ndikupatseni mkate kuti mudye, mupezenso mphamvu chifukwa muli pa ulendo.” 23  Koma iye anakana ndipo anati: “Sindidya.” Atatero, atumiki ake pamodzi ndi mkaziyo anapitiriza kumulimbikitsa kuti adye. Pamapeto pake, anamvera mawu awo ndipo anadzuka pamene anagonapo n’kukakhala pampando. 24  Tsopano mkaziyo anali ndi mwana wa ng’ombe wonenepa+ m’nyumba yake. Choncho anam’pereka nsembe msangamsanga,+ ndipo anatenga ufa n’kuukanda ndi kuphika mikate yopanda chofufumitsa. 25  Kenako anapereka chakudyacho kwa Sauli ndi atumiki ake ndipo iwo anadya. Atamaliza ananyamuka usiku womwewo.+

Mawu a M'munsi

Nkhaniyi ikutchula zinthu malinga ndi mmene mkazi wolankhula ndi mizimu uja anali kuonera. Iye ananyengedwa ndi chiwanda chimene chinadziyerekezera kukhala Samueli.
Mawu ake enieni, “ndaika moyo wanga m’dzanja langa.”