1 Samueli 27:1-12
27 Koma Davide anati mumtima mwake: “Tsiku lina Sauli adzandipha ndithu. Palibe chimene ndingachite choposa kuthawira+ kudziko la Afilisiti.+ Ndiyeno Sauli adzagwa ulesi ndipo adzasiya kundifunafuna m’dziko lonse la Isiraeli.+ Pamenepo ndidzakhala nditapulumuka m’manja mwake.”
2 Choncho Davide pamodzi ndi amuna 600+ amene anali kuyenda naye ananyamuka ndi kupita kwa Akisi+ mfumu ya Gati, mwana wa Maoki.
3 Davide anapitiriza kukhala ndi Akisi ku Gati. Iye anakhala kumeneko pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye, ndipo aliyense mwa amunawo anali ndi banja lake.+ Davide anali ndi akazi ake awiri aja, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala.
4 Patapita nthawi, uthenga unafika kwa Sauli wonena kuti Davide anathawira ku Gati. Atamva zimenezo sanapitenso kukam’sakasaka.+
5 Kenako Davide anauza Akisi kuti: “Ngati mungandikomere mtima tsopano, lolani kuti andipatse malo mu umodzi mwa mizinda ing’onoing’ono kuti ndikakhale kumeneko. Nanga ine mtumiki wanu ndikhalirenji mumzinda wachifumu pamodzi ndi inu?”
6 Choncho Akisi anam’patsa mzinda wa Zikilaga+ pa tsiku limenelo. N’chifukwa chake mzinda wa Zikilaga wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero.
7 Choncho nthawi yonse imene Davide anakhala kumidzi ya Afilisiti inakwana chaka chimodzi ndi miyezi inayi.+
8 Ndiyeno Davide pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye anapita kukathira nkhondo Agesuri,+ Agirezi ndi Aamaleki.+ Mitundu imeneyi inali kukhala m’dera loyambira ku Telami+ kukafika ku Shura,+ mpaka kukafika kudziko la Iguputo.
9 Davide anakantha dzikolo ndipo sanasiye mwamuna kapena mkazi aliyense ali wamoyo.+ Iye anatenga nkhosa, ng’ombe, abulu, ngamila ndi zovala. Atatero anabwerera ndi kupita kwa Akisi.
10 Ndiyeno Akisi anawafunsa kuti: “Kodi amunanu, lero munakamenya kuti nkhondo?” Poyankha, Davide anati:+ “Kum’mwera kwa dziko la Yuda,+ kum’mwera kwa dziko la Yerameeli+ ndi kum’mwera kwa Akeni.”+
11 Davide sanasiye mwamuna ndi mkazi aliyense ali wamoyo kuti abwere nawo ku Gati, chifukwa ananena kuti: “Angakatinenere kuti, ‘Davide watichita zakutizakuti.’”+ (Izi n’zimene iye anali kuchita masiku onse amene anakhala kumidzi ya Afilisiti.)
12 Akisi anakhulupirira+ Davide, ndipo mumtima mwake anati: “Mosakayikira, Davide wakhala fungo lonunkha kwa anthu akwawo Aisiraeli,+ ndipo iye akhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”