1 Samueli 26:1-25

26  Patapita nthawi, amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya,+ ndipo anamuuza kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kuphiri la Hakila+ moyang’anana ndi Yesimoni?”*+  Pamenepo Sauli ananyamuka+ ndi kupita kuchipululu cha Zifi, pamodzi ndi amuna osankhidwa mwapadera 3,000+ a mu Isiraeli, kuti akafunefune Davide kuchipululuko.  Pamene Davide anali kukhala m’chipululu, Sauli anamanga msasa m’mphepete mwa msewu, paphiri la Hakila moyang’anana ndi Yesimoni. Ndiyeno Davide anamva kuti Sauli wabwera kudzam’sakasaka m’chipululumo.  Choncho Davide anatumiza azondi+ kuti akaone ngati Sauli wabweradi.  Pambuyo pake, Davide ananyamuka ndi kupita kumene Sauli anamanga msasa. Atafika kumeneko, Davide anaona pamene Sauli komanso Abineri+ mwana wa Nera, mtsogoleri wa gulu lankhondo, anagona. Sauli anali atagona mkati mwa mpanda wa msasa,+ ndipo anthu ena onse anagona momuzungulira.  Ndiyeno Davide anauza Ahimeleki Mhiti+ ndi Abisai+ mwana wa Zeruya,+ m’bale wake wa Yowabu, kuti: “Ndani atsike nane kupita kwa Sauli kumsasa?” Abisai anayankha kuti: “Ine ndipita nawe.”+  Pamenepo Davide anapita kwa anthuwo usiku pamodzi ndi Abisai, ndipo atafika kumeneko anaona Sauli atagona mkati mwa mpanda wa msasawo, mkondo wake atauzika pansi chakumutu kwake. Ndipo Abineri ndi anthu ena onse anali atagona momuzungulira.  Tsopano Abisai anauza Davide kuti: “Lero Mulungu wapereka mdani wako m’manja mwako.+ Ndiye ndilole chonde, ndimubaye ndi kumukhomerera pansi ndi mkondo kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.”  Koma Davide anauza Abisai kuti: “Ayi, usamuphe. Kodi ndani anatambasula dzanja lake ndi kupha wodzozedwa wa Yehova,+ n’kukhala wopanda mlandu?”+ 10  Davide anapitiriza kunena kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ Yehova iye mwini adzamukantha,+ kapena tsiku lidzafika+ ndipo adzamwalira mmene amachitira wina aliyense, kapenanso adzapita kunkhondo+ ndipo adzaphedwa kumeneko.+ 11  Kwa ine, n’zosatheka!+ Sindingachite zimenezi pamaso pa Yehova.+ Sindingatambasule dzanja langa+ ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.+ Choncho, tiye titenge mkondo umene uli chakumutu kwakewo, ndi mtsuko wa madziwo tizipita.” 12  Chotero Davide anatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi zimene zinali chakumutu kwa Sauli n’kunyamuka. Palibe munthu anawaona+ kapena kuzindikira kalikonse kapenanso kudzuka, pakuti onse anali m’tulo. Tulo timene anagonato tinali tulo tofa nato,+ tochokera kwa Yehova. 13  Kenako Davide anapita kutsidya lina ndi kukaima pamwamba pa phiri, patali ndithu. Mtunda umene unali pakati pawo unali wautali kwambiri. 14  Tsopano Davide anayamba kuitana anthuwo ndi Abineri mwana wa Nera, kuti: “Kodi sukuyankha, Abineri?” Ndipo Abineri+ anayankha kuti: “Ndiwe ndani amene ukuitana mfumu?” 15  Pamenepo Davide anauza Abineri kuti: “Kodi iwe sindiwe mwamuna? Ndani angafanane nawe mu Isiraeli monse? Ndiye n’chifukwa chiyani sunayang’anire mbuye wako mfumu? Pakuti munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuye wako mfumu.+ 16  Zimene wachitazi si zabwino ayi. Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ anthu inu muyenera kufa ndithu,+ chifukwa simunayang’anire+ mbuye wanu. Ndithu simunayang’anire wodzozedwa wa Yehova.+ Tsopano taonani kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wake wa madzi+ zimene zinali chakumutu kwake.” 17  Pamenepo Sauli anazindikira mawu a Davide, ndipo anati: “Kodi ndi mawu ako, mwana wanga Davide?”+ Davide anayankha kuti: “Inde ndi mawu anga, mbuyanga mfumu.” 18  Davideyo anawonjezera kuti: “N’chifukwa chiyani inu mbuyanga mukuthamangitsa ine mtumiki wanu?+ Ndachita chiyani ine, ndipo ndalakwa chiyani?+ 19  Tsopano mbuyanga mfumu, mvetserani mawu a mtumiki wanu: Ngati Yehova ndiye wakutumani kuti mundiukire, iye alandire nsembe yanga yambewu.+ Koma ngati ndi ana a anthu,+ atembereredwe pamaso pa Yehova,+ chifukwa andipitikitsa ndi kundichotsa lero kuti ndisamve kuti ndili pafupi ndi cholowa cha Yehova,+ mwa kundiuza kuti, ‘Pita ukatumikire milungu ina!’+ 20  Tsopano musalole kuti magazi anga akhetsedwe pamaso pa Yehova,+ pakuti mfumu ya Isiraeli yapita kukasakasaka nthata imodzi,+ monga munthu wothamangitsa nkhwali imodzi m’mapiri.”+ 21  Poyankha Sauli anati: “Ndachimwa.+ Bwerera mwana wanga Davide, pakuti sindidzakuvulaza chifukwa moyo wanga wakhala wamtengo wapatali+ kwa iwe lero. Taona, ndachita zinthu mopusa ndipo ndalakwitsa kwambiri.” 22  Ndiyeno Davide anayankha kuti: “Nawu mkondo wa mfumu, tumizani mmodzi mwa anyamata anu abwere kudzautenga. 23  Yehova adzabwezera aliyense malinga ndi chilungamo+ ndi kukhulupirika kwake, pakuti lero Yehova anakuperekani m’manja mwanga, koma sindinafune kutambasula dzanja langa ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.+ 24  Monga mmene lero moyo wanu wakhalira wamtengo wapatali kwa ine, moyo wanganso ukhale wamtengo wapatali pamaso pa Yehova+ kuti andipulumutse m’masautso anga onse.”+ 25  Pamenepo Sauli anauza Davide kuti: “Udalitsike mwana wanga Davide. Mosakayikira iwe udzachita ntchito zazikulu ndipo udzapambana ndithu.”+ Pamenepo Davide anachoka ndipo Sauli anabwerera kwawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “chipululu.”