1 Samueli 25:1-44

25  Patapita nthawi, Samueli+ anamwalira ndipo Aisiraeli onse anasonkhana pamodzi ndi kulira+ maliro ake. Iwo anamuika m’manda panyumba yake ku Rama.+ Kenako Davide ananyamuka ndi kupita kuchipululu cha Parana.+  Tsopano mwamuna wina anali kukhala ku Maoni,+ koma ntchito yake anali kugwirira ku Karimeli.*+ Mwamuna ameneyu anali wotchuka kwambiri, ndipo anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina, iye anali kugwira ntchito yometa ubweya+ wa nkhosa zake ku Karimeli.  Mwamuna ameneyu dzina lake anali Nabala,+ ndipo mkazi wake anali Abigayeli.+ Mkazi wakeyu anali wanzeru kwambiri+ ndi wokongola, koma mwamunayu anali wouma mtima ndi wokonda kuchita zinthu zoipa.+ Mwamuna ameneyu anali wa m’banja la Kalebe.+  Davide ali kuchipululu, anamva kuti Nabala akumeta ubweya+ wa nkhosa zake.  Choncho Davide anatumiza anyamata ake 10 ndi kuwauza kuti: “Pitani ku Karimeli kwa Nabala mukam’funse za moyo wake m’dzina langa.+  M’bale wangayo mukamuuze kuti, ‘Mtendere ukhale nawe+ pamodzi ndi onse a m’nyumba yako ndi zonse zimene uli nazo.  Ine ndamva kuti ukumeta ubweya wa nkhosa zako. Abusa ako anali ndi ife.+ Sitinawavutitse,+ ndipo masiku onse amene tinali nawo ku Karimeli, palibe kanthu kawo kamene kanasowa.  Funsa anyamata ako zimenezi ndipo akuuza. Motero uwakomere mtima anyamata anga chifukwa tabwera tsiku labwino. Chonde, ugawire atumiki ako ndi mwana wako Davide chilichonse chimene dzanja lako lingapeze.’”+  Chotero anyamata a Davide anapita kukauza Nabala mawu onsewa m’dzina la Davide ndi kuyembekezera. 10  Pamenepo Nabala anayankha atumiki a Davide kuti: “Kodi Davide ndani,+ ndipo mwana wa Jese ndani? Masiku ano atumiki amene akuthawa ambuye awo achuluka kwabasi.+ 11  Ndiye ine nditenge mkate wanga,+ madzi ndi nyama imene ndaphera anyamata anga ometa ubweya wa nkhosa n’kupereka kwa amuna amene sindikudziwa m’pang’ono pomwe kumene achokera?”+ 12  Atamva zimenezi, anyamata a Davide anatembenuka ndi kubwerera, ndipo atafika anamuuza mawu onsewa. 13  Nthawi yomweyo, Davide anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Aliyense amange lupanga lake m’chiuno!”+ Pamenepo aliyense anamangadi lupanga lake m’chiuno, ndipo Davide nayenso anamanga lupanga lake m’chiuno. Zitatero, amuna pafupifupi 400 anapitira limodzi ndi Davide, koma amuna 200 anatsala kuti ayang’anire katundu.+ 14  Izi zili choncho, mmodzi mwa anyamata a Nabala anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala kuti: “Davide anatumiza nthumwi zake kuchokera m’chipululu kudzafunira zabwino mbuyanga, koma mbuyanga walalatira+ nthumwizo. 15  Amuna amenewa anatichitira zabwino kwambiri, sanativutitse, moti masiku onse amene tinali kuyenda nawo kutchire sitinataye kanthu ngakhale kamodzi.+ 16  Iwo anali ngati khoma+ lotizungulira usana ndi usiku, masiku onse amene tinakhala nawo pamene tinali kuweta nkhosa. 17  Choncho mudziwe zimenezi ndi kuona zimene mungachite, chifukwa atsimikiza kudzetsa tsoka+ pa mbuyanga ndi onse a m’nyumba yake, pakuti mbuye wathu ndi munthu wopanda pake,+ sitingathe kulankhula naye.” 18  Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anafulumira kutenga mitanda 200 ya mkate, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo,+ anapha nkhosa zisanu,+ anatenganso miyezo ya seya* isanu ya tirigu wokazinga,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100+ ndi nkhuyu zouma zoumba pamodzi 200+ ndi kuzikweza pa abulu. 19  Kenako anauza anyamata ake kuti: “Tsogolani,+ ine ndikubwera m’mbuyo mwanu.” Koma mwamuna wake Nabala sanamuuze kalikonse. 20  Ndiyeno pamene Abigayeli anali kutsika phiri atakwera bulu,+ mwadzidzidzi, anaona Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye akubwera, ndipo iye anakumana nawo. 21  Davide anali atanena kuti: “Ine ndinalondera zinthu zake m’chipululu ndipo palibe chinthu chake ngakhale chimodzi chimene chinasowa.+ N’zokhumudwitsa kuti munthu ameneyu akundibwezera zoipa pa zabwino zimene ndinam’chitira.+ 22  Choncho Mulungu alange mowirikiza+ adani a Davide, ngati ine ndidzasiya munthu aliyense wa m’nyumba ya Nabala wokodzera khoma*+ ali wamoyo kufikira m’mawa.”+ 23  Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika mofulumira pabulu wake. Iye anagwada pamaso pa Davide ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 24  Kenako anagwada pamapazi+ a Davide ndi kunena kuti: “Zolakwa zonse zikhale pa ine+ mbuyanga. Chonde, lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu+ ndipo mvetserani mawu a kapolo wanu. 25  Chonde mbuyanga, musaganizire za Nabala, munthu wopanda pakeyu,+ chifukwa zochita zake ndi zogwirizana ndi dzina lake. Dzina lake ndi Nabala* ndipo ndi wopandadi nzeru.+ Koma ine kapolo wanu wamkazi sindinawaone anyamata amene inu mbuyanga munawatuma. 26  Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+ 27  Ndiyeno mphatso*+ imene kapolo wanu wamkazi wabweretsa kwa inu mbuyanga, muipereke kwa anyamata amene akutsatira mapazi anu.+ 28  Chonde, khululukani kulakwa kwa kapolo wanu wamkazi,+ pakuti mosalephera Yehova adzakukhazikitsirani nyumba yachifumu, inu mbuyanga, ndipo idzakhalapo kwa nthawi yaitali,+ chifukwa inu mbuyanga mukumenya nkhondo za Yehova.+ Ndipo mwa inu simudzapezeka choipa chilichonse masiku onse a moyo wanu.+ 29  Munthu akakuukirani ndi kufunafuna moyo wanu, Yehova Mulungu+ adzakulunga ndi kuteteza moyo wanu m’phukusi la moyo+ monga mmene munthu amatetezera chuma chake. Koma moyo wa adani anu adzauponya ndi kuutaya kutali ngati mmene munthu amaponyera mwala ndi gulaye.*+ 30  Ndiye zimene zidzachitika n’zakuti, chifukwa chakuti Yehova adzachitira inu mbuyanga zabwino zimene wanena kwa inu, iye adzakuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli.+ 31  Choncho musalole kuti zimenezi zikhale zokuvutitsani chikumbumtima ndi zokhumudwitsa mumtima mwanu mbuyanga, mwa kukhetsa magazi popanda chifukwa+ ndi kudzipulumutsa nokha ndi dzanja lanu.+ Mukatero, Yehova adzakuchitirani zabwino mbuyanga, ndipo mudzandikumbukire+ ine kapolo wanu wamkazi.” 32  Pamenepo Davide anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene wakutumiza kudzakumana nane lero! 33  Iwenso udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako.+ Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi+ ndi kudzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.+ 34  Komabe, pali Yehova Mulungu wamoyo wa Isiraeli, amene wandigwira kuti ndisakuchitire choipa,+ ukanapanda kufulumira kudzakumana nane,+ ndithu sipakanatsala munthu wokodzera khoma+ m’banja la Nabala pofika mawa m’mawa.” 35  Atatero, Davide analandira zimene Abigayeli anamubweretsera ndiyeno anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako mwamtendere.+ Taona, ndamvera mawu ako kuti ndichite zinthu mokuganizira.”+ 36  Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake. 37  Tsopano m’mawa mwake, vinyo atamuthera m’mutu, mkazi wake anayamba kumuuza zinthu zonsezi. Nabala atamva zimenezi, mtima wake+ unaferatu mkati mwake ndipo iye anakhala ngati mwala. 38  Patapita masiku 10, Yehova anakantha+ Nabala ndipo anafa. 39  Ndiyeno Davide anamva kuti Nabala wamwalira. Atatero, iye anati: “Adalitsike Yehova amene wandiweruzira mlandu+ ndi kundimasula ku chitonzo+ cha Nabala, komanso wagwira ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa.+ Yehova wabwezera zoipa za Nabala pamutu pake!”+ Pamenepo Davide anatumiza anthu kuti akamufunsirire Abigayeli, kuti akhale mkazi wake.+ 40  Choncho atumiki a Davide anapita ku Karimeli ndi kulankhula naye kuti: “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukakhale mkazi wake.” 41  Nthawi yomweyo, ananyamuka ndi kugwada mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Ine kapolo wanu ndine wokonzeka kukhala mtumiki wosambitsa mapazi+ a atumiki a mbuyanga.”+ 42  Kenako Abigayeli+ ananyamuka mofulumira ndi kukwera pabulu,+ atsikana ake asanu antchito akumutsatira pambuyo. Iye anatsatira nthumwi za Davide ndipo anakakhala mkazi wake. 43  Davide anali atatenganso Ahinowamu+ wa ku Yezereeli,+ ndipo onse awiriwa anakhala akazi ake.+ 44  Koma Sauli anali atapereka Mikala+ mwana wake wamkazi, mkazi wake wa Davide, kwa Paliti,+ mwana wamwamuna wa Laisi wa ku Galimu.+

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mzinda wa m’dera lamapiri la Yuda, umene unali pamtunda wa makilomita 12 kum’mwera kwa Heburoni. Si wofanana ndi phiri la Karimeli. Onani Yos 15:20, 54, 55.
Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita pafupifupi 8.
Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.
Kutanthauza, “Wopanda Nzeru.”
Kapena kuti “dalitso.”
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 17:40.