1 Samueli 24:1-22

24  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Sauli atangobwerera kuchokera kothamangitsa Afilisiti,+ kunabwera uthenga wakuti: “Davide ali m’chipululu cha Eni-gedi.”+  Pamenepo Sauli anatenga amuna osankhidwa mwapadera 3,000+ mu Isiraeli monse, ndipo anapita kukafunafuna Davide+ ndi amuna amene anali kuyenda naye m’matanthwe amene mumakhala mbuzi za m’mapiri.+  Patapita nthawi, Sauli anafika kumakola a nkhosa amiyala m’mphepete mwa msewu, kumene kunali phanga. Choncho Sauli analowa mmenemo kukadzithandiza.+ Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali atakhala pansi m’zigawo za mkatikati za phangalo,+ kumbuyo kwambiri.  Amuna amene anali ndi Davidewo anayamba kumuuza kuti: “Lerotu ndi tsiku limene Yehova akukuuzani kuti, ‘Taona, ndapereka mdani wako m’manja mwako,+ ndipo umuchitire chilichonse chimene ukuona kuti n’chabwino.’”+ Choncho Davide ananyamuka ndipo mwakachetechete anadula kansalu m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Sauli.  Koma pambuyo pake, Davide anavutika mumtima mwake+ chifukwa chakuti anali atadula kansalu m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Sauli.  Choncho iye anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Sindinayenere m’pang’ono pomwe kuchitira mbuyanga zimenezi pamaso pa Yehova. Iye ndi wodzozedwa+ wa Yehova. Sindinayenere kutambasula dzanja langa ndi kumuukira, pakuti iye ndi wodzozedwa wa Yehova.”+  Chotero ndi mawu amenewa, Davide anabalalitsa amuna amene anali kuyenda naye, ndipo sanawalole kuti aukire Sauli.+ Koma Sauli ananyamuka ndi kutuluka m’phangamo.  Pambuyo pake, Davide nayenso anatuluka m’phangamo ndi kuitana Sauli kuti: “Mbuyanga+ mfumu!” Pamenepo Sauli anacheuka ndipo Davide anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+  Ndiyeno Davide anauza Sauli kuti: “N’chifukwa chiyani mukumvera mawu a anthu,+ akuti, ‘Davide akufuna kukuvulazani’? 10  Lero mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani m’manja mwanga m’phangamu. Winawake anandiuza kuti ndikupheni,+ koma ndinakumverani chisoni n’kunena kuti, ‘Sindingatambasule dzanja langa ndi kuukira mbuyanga, pakuti iye ndi wodzozedwa+ wa Yehova.’ 11  Tsopano, bambo anga,+ onani. Taonani kansalu ka m’munsi mwa malaya anu akunja odula manja. Pakuti mmene ndinali kudula kansalu kameneka sindinakupheni. Ndiyetu dziwani ndi kuona kuti ndilibe maganizo oipa+ kapena oukira, ndipo sindinakuchimwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.+ 12  Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu,+ ndipo Yehova andibwezerere,+ koma dzanja langali silidzakukhudzani.+ 13  Mwambi wa anthu akale umati, ‘Choipa chimachokera kwa munthu woipa,’+ koma dzanja langali silidzakukhudzani. 14  Kodi mfumu ya Isiraeli ikulondola ndani? Kodi mukuthamangitsa ndani? Zoona mukuthamangitsa galu wakufa?+ Nthata imodzi?+ 15  Yehova akhale woweruza, ndipo aweruze pakati pa ine ndi inu. Iye adzandiweruzira mlanduwu+ ndi kuchitapo kanthu kuti andimasule m’manja mwanu.” 16  Ndiyeno Davide atangomaliza kulankhula mawu amenewa kwa Sauli, Sauli anati: “Kodi ndi mawu ako, mwana wanga Davide?”+ Pamenepo Sauli anayamba kulira mokweza mawu.+ 17  Iye anapitiriza kuuza Davide kuti: “Ndiwe wolungama kwambiri kuposa ine,+ pakuti iwe wandichitira zabwino,+ koma ine ndakuchitira zoipa. 18  Lero iwe wasonyeza zabwino zimene wandichitira, pakuti Yehova anandipereka m’manja mwako+ koma iwe sunandiphe. 19  Tsopano ngati munthu wapeza mdani wake, kodi angamulole kupita mwamtendere?+ Chonchotu Yehova adzakufupa ndi zinthu zabwino,+ chifukwa chakuti lero wandichitira zabwino. 20  Taona! Ine ndikudziwa bwino kwambiri kuti mosalephera iweyo udzalamulira monga mfumu,+ ndipo ufumu wa Isiraeli udzakhazikika m’banja lako nthawi zonse. 21  Choncho ndilumbirire tsopano pali Yehova+ kuti sudzawononga mbewu yanga yobwera m’mbuyo mwanga, ndi kuti sudzafafaniza dzina langa m’nyumba ya bambo anga.”+ 22  Zitatero, Davide analumbirira Sauli. Kenako Sauliyo anapita kwawo,+ koma Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anapita kumalo ovuta kufikako.+

Mawu a M'munsi