1 Samueli 23:1-29

23  Patapita nthawi, kunabwera anthu amene anauza Davide kuti: “Afilisiti akuthira nkhondo mzinda wa Keila,+ ndipo akufunkha zokolola zimene zili pamalo opunthira mbewu.”+  Ndiyeno Davide anayamba kufunsira+ kwa Yehova, kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa?” Yehova anayankha Davide kuti: “Pita, ukamenyane ndi Afilisitiwo ndipo ukapulumutse Keila.”  Amuna amene anali kuyenda ndi Davide anamuyankha kuti: “Ngati tikuchita mantha tili mbali ino ya Yuda,+ ndiye kuli bwanji tikapita ku Keila kukamenyana ndi asilikali a Afilisiti!”+  Choncho Davide anafunsiranso kwa Yehova.+ Tsopano Yehova anamuyankha kuti: “Nyamuka, pita ku Keila, chifukwa ndikupereka Afilisitiwo m’manja mwako.”+  Chotero Davide anapita ku Keila ndi amuna amene anali kuyenda naye, kukamenyana ndi Afilisitiwo. Iye anawalanda ziweto zawo ndipo anapha Afilisiti ochuluka kwambiri, moti Davide anakhala mpulumutsi wa anthu a mumzinda wa Keila.+  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Abiyatara+ mwana wamwamuna wa Ahimeleki anathawira kwa Davide ku Keila, anapita kumeneko atatenga efodi+ m’manja mwake.  Patapita nthawi, Sauli analandira uthenga wonena kuti: “Davide ali ku Keila.”+ Pamenepo Sauli ananena kuti: “Mulungu wamugulitsa kwa ine,+ pakuti wadzitsekera yekha mwa kulowa mumzinda wokhala ndi zitseko ndi mipiringidzo.”  Choncho Sauli anaitanitsa anthu onse kuti apite ku Keila kukazungulira Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye, n’kuwathira nkhondo.  Davide anadziwa kuti Sauli akumukonzera chiwembu.+ Choncho anauza Abiyatara wansembe kuti: “Bweretsa efodi kuno.”+ 10  Atamupatsa, Davide anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ ine mtumiki wanu ndamva kuti Sauli akufuna kubwera kuno ku Keila kuti awononge mzindawu chifukwa cha ine.+ 11  Kodi anthu a mumzinda wa Keila adzandipereka m’manja mwake? Kodi Sauli abweradi kuno monga mmene ine mtumiki wanu ndamvera? Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndiuzeni ine mtumiki wanu, chonde.” Pamenepo Yehova anamuyankha kuti: “Abweradi kuno.”+ 12  Ndiyeno Davide anafunsanso kuti: “Kodi anthu a mumzinda wa Keila adzandiperekadi m’manja mwa Sauli pamodzi ndi amuna amene ndikuyenda nawowa?” Poyankha, Yehova anati: “Adzaterodi.”+ 13  Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi amuna pafupifupi 600+ amene anali kuyenda naye. Iwo anatuluka mu Keila ndi kumangoyendayenda kulikonse kumene akufuna. Ndiyeno uthenga unafika kwa Sauli kuti Davide wathawa ku Keila. Sauli atamva zimenezi sanapitekonso. 14  Tsopano Davide anayamba kukhala m’chipululu, m’malo ovuta kufikako. Iye anapitiriza kukhala m’dera lamapiri m’chipululu cha Zifi,+ ndipo Sauli anali kumufunafuna nthawi zonse,+ koma Mulungu sanam’pereke m’manja mwake.+ 15  Davide anapitiriza kukhala mwamantha chifukwa Sauli anali kufunafuna moyo wake, pamene Davideyo anali m’chipululu cha Zifi ku Horesi.*+ 16  Tsopano Yonatani mwana wa Sauli ananyamuka ndi kupita kwa Davide ku Horesi, kuti akalimbikitse+ Davide kudalira Mulungu.+ 17  Ndiyeno anamuuza kuti: “Usachite mantha,+ chifukwa dzanja la Sauli bambo anga silikupeza, moti iwe ukhaladi mfumu+ ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe. Sauli bambo anga akudziwa bwino zimenezi.”+ 18  Kenako awiriwo anachita pangano+ pamaso pa Yehova. Zitatero, Davide anapitiriza kukhala ku Horesi koma Yonatani anabwerera kwawo. 19  Kenako amuna a ku Zifi+ anapita kwa Sauli ku Gibeya+ kukamuuza kuti: “Kodi Davide si uyu akubisala+ pafupi ndi ife m’malo ovuta kufikamo ku Horesi,+ paphiri la Hakila+ limene lili kudzanja lamanja* la Yesimoni?*+ 20  Choncho, malinga ndi chokhumba cha moyo wanu,+ mfumu, chofuna kubwera kuno, bwerani, ndipo ife tidzam’pereka m’manja mwa mfumu.”+ 21  Pamenepo Sauli anati: “Yehova akudalitseni,+ chifukwa mwandichitira chisoni. 22  Chonde pitani, mukayesetsebe kufufuza kwa aliyense amene anamuonayo, ndipo mukaone kumene iye amafika, pakuti ndauzidwa kuti ndi wochenjera kwambiri.+ 23  Mukaonetsetse ndi kutsimikizira za malo onse obisika kumene iye amabisala. Kenako mudzabwerenso kwa ine ndi umboni, ndipo ine ndidzapita nanu. Ngati alidi m’dzikolo, ndidzam’funafuna mosamala pakati pa anthu masauzande+ ambirimbiriwo a Yuda.” 24  Chotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi,+ Sauli atamusiya kumbuyo. Izi zinachitika pamene Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali m’chipululu cha Maoni,+ mu Araba,+ kum’mwera kwa Yesimoni. 25  Kenako Sauli anafika ndi asilikali ake kudzafunafuna Davide.+ Davide atauzidwa zimenezi, nthawi yomweyo analowa mkatikati mwa chipululu n’kukabisala kuthanthwe,+ ndipo anapitiriza kukhala m’chipululu cha Maoni. Sauli atamva zimenezo anayamba kuthamangitsa+ Davide m’chipululu chimenecho cha Maoni. 26  Kenako Sauli anakhala mbali imodzi ya phiri ndipo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anali mbali inanso ya phirilo. Zitatero Davide ananyamuka mofulumira kuti athawe+ Sauli. Pa nthawiyi n’kuti Sauli ndi asilikali ake atatsala pang’ono kupeza ndi kugwira Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye.+ 27  Koma kunabwera mthenga kwa Sauli amene anamuuza kuti: “Bwererani mofulumira, Afilisiti aukira dziko!” 28  Pamenepo Sauli anasiya kum’thamangitsa Davide+ ndipo anabwerera kukakumana ndi Afilisiti. N’chifukwa chake malowo anawatcha Thanthwe Logawanitsa. 29  Ndiyeno Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala m’malo ovuta kufikako a ku Eni-gedi.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza “Malo a Mitengo.”
Mawu akuti “kudzanja lamanja” ayenera kuti akunena kum’mwera kwa Yesimoni. Yerekezerani ndi vesi 24.
Kapena kuti “chipululu.”