1 Samueli 22:1-23

22  Choncho Davide anachoka kumeneko+ ndi kuthawira+ kuphanga+ la Adulamu.+ Abale ake ndi nyumba yonse ya bambo ake anamva zimenezo, ndipo ananyamuka kumutsatira.  Amuna onse amene anali kusautsidwa,+ onse amene anali ndi ngongole,+ ndi onse amene anali ndi zodandaula+ anayamba kusonkhana kwa iye,+ ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo.+ Anthu onse amene anali naye anakwana 400.  Kenako Davide anachoka kupita ku Mizipe, ku Mowabu ndi kupempha mfumu ya Mowabu+ kuti: “Chonde, lolani kuti bambo ndi mayi anga+ akhale nanu kufikira nditadziwa zimene Mulungu adzandichitira.”  Chotero iye anawasiya m’manja mwa mfumu ya Mowabu, moti iwo anapitiriza kukhala kumeneko masiku onse amene Davide anakhala m’malo ovuta kufikako.+  Patapita nthawi, Gadi+ mneneri anauza Davide kuti: “Usakhalenso m’malo ovuta kufikako. Uchokeko ndi kubwera m’dziko la Yuda.”+ Choncho Davide anachokako ndi kulowa munkhalango ya Hereti.  Ndiyeno Sauli anamva kuti Davide ndi anthu amene anali naye apezeka. Iye anamva zimenezi ali ku Gibeya pamalo okwezeka, atakhala pansi pa mtengo wa bwemba.+ Sauliyo anali atagwira mkondo+ m’manja mwake ndipo atumiki ake onse anali atamuzungulira.  Iye anauza atumiki ake amene anali atamuzungulirawo kuti: “Tamverani inu Abenjamini. Kodi nayenso mwana wa Jese+ adzakupatsani minda ya mpesa ndi minda ya mbewu zina?+ Kodi nonsenu adzakuikani kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 100?  Pakuti nonsenu mwandikonzera chiwembu chifukwa palibe aliyense amene anaulula kwa ine+ pamene mwana wanga anachita pangano+ ndi mwana wa Jese. Palibenso aliyense wa inu amene wandimvera chifundo ndi kuulula kwa ine kuti mwana wanga weniweni wasandutsa mtumiki wanga kukhala wondibisalira kuti andichite chiwembu monga mmene zililimu.”  Pamenepo Doegi,+ Mwedomu, amene anali mkulu wa atumiki a Sauli anayankha kuti: “Ineyo ndinaona mwana wa Jese atabwera ku Nobu kwa Ahimeleki,+ mwana wa Ahitubu.+ 10  Ndipo Ahimeleki anafunsira+ kwa Yehova m’malo mwa Davide, kenako anam’patsa chakudya+ ndi lupanga+ la Goliyati Mfilisiti.” 11  Nthawi yomweyo mfumu inatumiza anthu kuti akaitane Ahimeleki wansembe, mwana wa Ahitubu, pamodzi ndi nyumba yonse ya bambo ake, ansembe a ku Nobu.+ Choncho onsewo anabwera kwa mfumu. 12  Pamenepo Sauli anati: “Tamvera iwe mwana wa Ahitubu.” Ndipo Ahimeleki anayankha kuti: “Ndikumva mbuyanga.” 13  Ndiyeno Sauli anapitiriza kumuuza kuti: “N’chifukwa chiyani anthu inu mwandikonzera chiwembu,+ iweyo ndi mwana wa Jese? Iweyo wamupatsa mkate ndi lupanga, komanso wamufunsira kwa Mulungu kuti andiukire pondibisalira monga mmene zililimu.”+ 14  Ahimeleki anayankha mfumuyo kuti: “Ndani pakati pa atumiki anu onse ali ngati Davide,+ munthu wokhulupirika,+ mkamwini+ wa mfumu, mtsogoleri wa asilikali okulonderani ndiponso munthu wolemekezeka m’nyumba yanu?+ 15  Kodi ndayamba lero kumufunsira+ kwa Mulungu? Sindingachite zimene mukunenazo! Chonde, mfumu isaimbe mlandu ine mtumiki wanu ngakhalenso nyumba yonse ya bambo anga, pakuti ndinachita zonsezi mosadziwa chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu.”+ 16  Koma mfumu inati: “Ufa ndithu+ Ahimeleki, pamodzi ndi nyumba yonse ya bambo ako.”+ 17  Pamenepo mfumu inauza asilikali othamanga+ amene anaima pamaso pake kuti: “Tembenukani ndi kupha ansembe a Yehova chifukwa ali kumbali ya Davide. Iwo anali kudziwanso kuti Davide ndi wothawa koma sanaulule kwa ine!”+ Koma atumiki a mfumuwo sanafune kutambasula manja awo kuti akanthe ansembe a Yehova.+ 18  Pamapeto pake mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, tembenuka ukanthe ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi, Mwedomu,+ anatembenuka n’kukantha ndi kupha+ ansembewo tsiku limenelo, amuna 85 ovala efodi+ wa nsalu. 19  Iye anakanthanso ndi lupanga Nobu,+ mzinda wa ansembe. Anapha amuna, akazi, ana aang’ono ndi ana oyamwa, komanso ng’ombe zamphongo, abulu ndi nkhosa. 20  Koma mwana mmodzi wamwamuna wa Ahimeleki, mwana wa Ahitubu, dzina lake Abiyatara+ anapulumuka n’kuthawa kutsatira Davide. 21  Ndiyeno Abiyatara anauza Davide kuti: “Sauli wapha ansembe a Yehova.” 22  Pamenepo Davide anauza Abiyatara kuti: “Tsiku lomwe lija ndinadziwa+ kuti mosalephera, Doegi, Mwedomu uja, akauza Sauli+ chifukwa Doegiyo anali kumeneko. Ineyo ndalakwira aliyense wa m’nyumba ya bambo ako. 23  Koma iwe khala ndi ine. Usachite mantha. Chifukwa aliyense amene akufunafuna moyo wanga akufunafunanso moyo wako, ndipo ndifunika kukuteteza.”+

Mawu a M'munsi