1 Samueli 21:1-15

21  Kenako Davide anafika ku Nobu+ kwa Ahimeleki wansembe. Ahimeleki+ ataona Davide anayamba kunjenjemera, ndipo anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani uli wekha popanda munthu wina?”+  Pamenepo Davide anauza Ahimeleki wansembe kuti: “Mfumu yandituma nkhani inayake,+ ndipo yandiuza kuti, ‘Usauze munthu aliyense nkhani imene ndikukutuma ndi zimene ndakulamula.’ Choncho ndapangana ndi anyamata kuti ndikumane nawo pamalo enaake.  Ndiye ngati muli ndi mitanda isanu ya mkate kapena chilichonse chimene chingapezeke, ndipatseni.”+  Koma wansembeyo anayankha Davide kuti: “Ndilibe mkate wamba, koma pali mkate wopatulika.+ Nditha kukupatsa umenewu ngati anyamatawo ayesetsa kudzisunga osagona ndi akazi.”+  Davide anayankha wansembeyo kuti: “Koma akazi sanatiyandikire monga mmene zinakhaliranso poyamba pamene ndinapita kukamenya nkhondo.+ Anyamatawo amakhala oyera ngakhale pamene tili pa ntchito wamba. Ndiye kuli bwanji lero pamene tili pa ntchito yapadera?”  Pamenepo wansembeyo anam’patsa mkate wopatulika,+ chifukwa panalibe mkate wina koma mkate wachionetsero wokha, umene anali atauchotsa pamaso pa Yehova+ pa tsiku limenelo kuti aikepo watsopano.  Tsopano tsiku limenelo, mmodzi wa atumiki a Sauli, dzina lake Doegi,+ Mwedomu,+ anali kumeneko chifukwa anali atamusunga+ pamaso pa Yehova. Iye anali mkulu wa abusa a Sauli.+  Davide anafunsa Ahimeleki kuti: “Kodi muli ndi chida chilichonse pano, mkondo kapena lupanga? Inetu sindinatenge lupanga kapena zida zanga, pakuti zimene mfumu yandituma zinali kufunika mofulumira.”  Wansembeyo poyankha anati: “Lupanga la Goliyati+ Mfilisiti amene unamukantha m’chigwa cha Ela+ lilipo. Lakulungidwa ndi nsalu ndipo lili kuseli kwa efodi.+ Ngati ungakonde kutenga limeneli, litenge, chifukwa palibenso lupanga lina.” Pamenepo Davide anati: “Palibe lina lingafanane nalo, ndipatseni limenelo.” 10  Pamenepo Davide ananyamuka tsiku limenelo, ndipo anapitiriza kuthawa+ chifukwa choopa Sauli. Patapita nthawi anafika kwa Akisi mfumu ya Gati.+ 11  Atafika kumeneko, atumiki a Akisi anayamba kunena kuti: “Kodi ameneyu si Davide+ mfumu ya dziko? Suja ankamuimbira nyimbo molandizana mawu, akuvina+ n’kumati,‘Sauli wakantha adani ake masauzande,Ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi’?”+ 12  Davide atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri+ chifukwa cha Akisi mfumu ya Gati. 13  Chotero iye anadzibisa+ kuti asadziwike kuti ndi munthu wabwinobwino,+ moti pamene anali m’manja mwawo anayamba kuchita zinthu ngati munthu wamisala. Iye anayamba kulembalemba pazitseko za pachipata, dovu lili chuchuchu, likuyenderera pandevu zake. 14  Pamapeto pake Akisi anauza atumiki ake kuti: “Mukuona kuti munthuyu ndi wamisala. N’chifukwa chiyani mwabwera naye kwa ine? 15  Kodi ine ndikufuna anthu amisala, kuti mundibweretsere munthu ameneyu kudzachita zamisala pamaso panga? Kodi ameneyu ndi woyenera kulowa m’nyumba mwanga?”

Mawu a M'munsi