1 Samueli 20:1-42

20  Ndiyeno Davide anathawa+ kuchoka ku Nayoti, ku Rama. Koma anapita kwa Yonatani ndi kumuuza kuti: “Kodi ine ndachita chiyani?+ Ndalakwanji, ndipo bambo ako ndawachimwira chiyani kuti azindifunafuna kuti andiphe?”  Pamenepo Yonatani anamuyankha kuti: “N’zosatheka zimenezo,+ suufa. Bambo anga sangachite chilichonse chachikulu kapena chaching’ono osandiuza ine.+ Ndiye bambo anga angandibisire nkhani imeneyi chifukwa chiyani?+ Sizingachitike zimenezo.”  Koma poyankha Davide analumbira+ kuti: “Bambo ako ayenera kuti akudziwa ndithu kuti iweyo umandikonda.+ Pa chifukwa chimenechi iwo adzanena kuti, ‘Musamuuze zimenezi Yonatani kuti zingamupweteketse mtima.’ Moti ndikunenetsa, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wako,+ imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+  Ndiyeno Yonatani anauza Davide kuti: “Ine ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene.”  Poyankha, Davide anauza Yonatani kuti: “Mawatu ndi tsiku lokhala mwezi,+ ndipo mosalephera ndiyenera kukadya pamodzi ndi mfumu. Ndiyeno iweyo undilole ndipite kuti ndikabisale+ kutchire mpaka mkuja madzulo.  Ngati bambo ako angafunse za ine, uwauze kuti, ‘Davide anandichonderera kuti ndimulole kuchoka kuti athamangire kumzinda wakwawo ku Betelehemu,+ chifukwa banja lawo lonse likukapereka nsembe ya pachaka.’+  Ngati anganene kuti, ‘Palibe vuto!’ ndiye kuti zinthu zili bwino kwa mtumiki wako. Koma ngati angakwiye, udziwe kuti atsimikiza mtima kuchita kenakake koipa.+  Ukatero undisonyeze kukoma mtima kosatha ine mtumiki wako,+ pakuti unandilowetsa m’pangano+ la Yehova pamodzi ndi iwe. Koma ngati ndili wolakwa,+ undiphe ndiwe, m’malo moti uchite kukandipereka kwa bambo ako.”  Pamenepo Yonatani anati: “N’zosatheka kuti iwe ukhale wolakwa! Koma ngati ndingadziwe zoipa zimene bambo anga akufuna kukuchitira, ukuganiza kuti sindingakuuze?”+ 10  Ndiyeno Davide anauza Yonatani kuti: “Nanga adzandiuza ndani ngati bambo ako akuyankha mwaukali?” 11  Poyankha, Yonatani anauza Davide kuti: “Tiye kuno, tipite kutchire.” Choncho onse awiri anapita kuthengo. 12  Yonatani anauzanso Davide kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli+ akhale mboni,+ ndidzalankhula ndi bambo anga mawa kapena mkuja, ndipo ngati alibe chifukwa ndi iwe Davide, ndithu ine ndikutumizira uthenga wokudziwitsa zimenezi. 13  Yehova andilange ine Yonatani mowirikiza,+ ndikadziwa kuti bambo anga akufuna kukuchitira choipa koma osakudziwitsa ndi kukulola kuti uchoke, moti iweyo n’kulepheradi kuchoka mwamtendere. Yehova akhale nawe+ monga mmene anakhalira ndi bambo anga.+ 14  Ndipo ine ndikadzakhalabe ndi moyo,+ kodi sudzandisonyeza kukoma mtima kosatha kwa Yehova kuti ndisafe?+ Kodi sudzatero? 15  Chonde, usadzasiye kusonyeza nyumba yanga kukoma mtima kosatha mpaka kalekale.+ Ngakhalenso pamene Yehova adzawononga mdani aliyense wa Davide padziko lapansi, 16  dzina la Yonatani lisadzadulidwe m’nyumba ya Davide.+ Yehova adzaimbe mlandu adani a Davide, pangano limeneli likadzasweka.” 17  Choncho Yonatani analumbiranso kwa Davide chifukwa chakuti anali kum’konda kwambiri. Pakuti Yonatani anali kukonda Davide monga mmene anali kudzikondera iye mwini.+ 18  Ndiyeno Yonatani anapitiriza kunena kuti: “Mawa ndi tsiku lokhala mwezi,+ ndipo tidzakusowa, chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu. 19  Ndipo mkuja tidzakusowanso kwambiri. Pa tsiku logwira ntchito, iweyo udzabwere pamalo amene unabisala,+ ndipo udzakhale pafupi ndi mwala uwu. 20  Ineyo ndidzaponya mivi itatu kumbali ina ya mwalawo, kuilunjikitsa pachinachake. 21  Ndiyeno ndidzatumiza mtumiki kuti, ‘Pita ukatole miviyo.’ Koma mtumikiyo ndikadzamuuza mawu akuti, ‘Mivi ili kumbali yakutiyakuti, pita ukatole,’ iweyo ukatuluke chifukwa ndiye kuti zinthu zili bwino ndipo palibe chodetsa nkhawa chilichonse. Ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo.+ 22  Koma mnyamatayo ndikadzamuuza kuti, ‘Mivi ili kutali kwambiri ndi iwe,’ ndiye kuti uyenera kuchoka, chifukwa Yehova wakulola kupita. 23  Yehova akhale mboni yathu mpaka kalekale,+ pa mawu awa amene tauzana+ ine ndi iwe.” 24  Davide anapita kutchire kukabisala.+ Pa tsiku lokhala mwezi, mfumu inakhala pamalo ake kuti idye chakudya.+ 25  Iyo inakhala pamalo ake a nthawi zonse, pampando umene unali kufupi ndi khoma. Yonatani anakhala moyang’anizana ndi mfumuyo, pamene Abineri+ anakhala pambali pa Sauli. Koma mpando wa Davide unali wopanda munthu. 26  Pa tsiku limeneli Sauli sananene chilichonse, pakuti mumtima mwake anaganiza kuti: “China chake chachitika, ayenera kuti wadetsedwa,+ ndipo sanayeretsedwe.” 27  Tsiku lotsatizana ndi tsiku lokhala mwezi, tsiku lachiwiri, mpando wa Davide unakhalabe wopanda munthu. Choncho Sauli anafunsa mwana wake Yonatani kuti: “N’chifukwa chiyani mwana wa Jese+ sanabwere ku chakudya dzulo ndi lero?” 28  Yonatani anayankha Sauli kuti: “Davide anandichonderera kuti ndimulole kuchoka kuti apite ku Betelehemu.+ 29  Anandiuza kuti, ‘Chonde ndilole ndipite kumzinda wakwathu kukapereka nsembe ya banja lathu. M’bale wanga ndi amene wandiitanitsa. Choncho ngati ungandikomere mtima, chonde ndilole ndichoke mwakachetechete ndiponso mofulumira kuti ndikaone abale anga.’ N’chifukwa chake sanabwere kudzadya chakudya pamodzi ndi mfumu.” 30  Ndiyeno Sauli anamukwiyira kwambiri+ Yonatani, ndipo anamuuza kuti: “Chimwana cha mkazi wopanduka iwe.+ Ukuganiza sindikudziwa kuti wasankha kugwirizana ndi mwana wa Jese, ndi kudzichititsa wekha manyazi ndiponso kuvula mayi ako?+ 31  Masiku onse amene mwana wa Jeseyo adzakhala ndi moyo, iweyo ndi ufumu wako sudzakhazikika ayi.+ Choncho tumiza anthu akamugwire ndi kumubweretsa kwa ine, pakuti ayenera kufa ndithu.”+ 32  Koma Yonatani anayankha Sauli bambo ake kuti: “Aphedwe chifukwa chiyani?+ Walakwanji?”+ 33  Atatero, Sauli anaponya mkondo wake kuti amulase.+ Pamenepo Yonatani anadziwa kuti bambo ake anatsimikiza mtima kupha Davide.+ 34  Nthawi yomweyo, Yonatani ananyamuka patebulopo atakwiya kwambiri,+ ndipo sanadye mkate tsiku lachiwiri lotsatizana ndi tsiku lokhala mwezi. Iye anachita zimenezi chifukwa chopwetekedwa mtima ndi nkhani ya Davide,+ pakuti bambo ake anam’chititsa manyazi.+ 35  M’mawa mwake, Yonatani pamodzi ndi mtumiki wake wachinyamata anapita kutchire kumene anapangana kukakumana ndi Davide.+ 36  Ndiyeno anauza mtumiki wakeyo kuti: “Chonde, thamanga kuti ukatole mivi imene ndikuponya.”+ Mtumikiyo anathamanga, ndipo Yonatani anaponya muvi kuti upitirire mtumikiyo. 37  Mtumiki uja atafika pamalo amene muvi wa Yonatani unagwera, Yonatani anayamba kumufuulira kumbuyo kwake kuti: “Kodi muvi sunagwere patali kwambiri ndi pamene iwe uli?”+ 38  Zitatero, Yonatani anapitiriza kufuulira mtumiki uja kuti: “Fulumira! Chita changu! Usaime!” Ndiyeno mtumiki wa Yonatani anatola miviyo ndi kubwera nayo kwa mbuye wake. 39  Koma mtumikiyo sanadziwe kalikonse. Yonatani ndi Davide okha ndi amene anali kudziwa zimene zinali kuchitika. 40  Kenako, Yonatani anapatsa mtumiki wakeyo zida zake ndi kumuuza kuti: “Tenga zidazi ndi kupita nazo kumzinda.” 41  Mtumikiyo anapitadi. Zitatero, Davide anatulukira pafupi, chakum’mwera. Ndiyeno anagwada ndi kugunditsa nkhope yake pansi+ n’kuwerama katatu. Atatero, anayamba kupsompsonana+ ndi kulirirana mpaka Davide analira kwambiri kuposa Yonatani.+ 42  Pamenepo Yonatani anauza Davide kuti: “Pita mu mtendere,+ pakuti tonse awiri talumbira+ m’dzina la Yehova kuti, ‘Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.’”+ Chotero Davide ananyamuka ndi kupita, koma Yonatani anabwerera kumzinda.

Mawu a M'munsi