1 Samueli 2:1-36

2  Ndiyeno Hana anayamba kupemphera+ kuti:“Mtima wanga ukukondwera mwa Yehova,+Nyanga* yanga yakwezekadi kudzera mwa Yehova.+Ndikutsutsana ndi adani anga molimba mtima,Pakuti ndikukondwera ndi chipulumutso chochokera kwa inu.+   Palibe woyera ngati Yehova. Palibe aliyense koma inu nokha.+Palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.+   Musalankhule modzikweza kwambiri anthu inu,Pakamwa panu pasatuluke mawu odzikuza,+Pakuti Yehova ndi Mulungu wodziwa zonse.+Ndipo zochita za anthu, iye amaziyeza molondola.+   Oponya mivi ndi uta mwaluso agwidwa ndi mantha,+Koma olefuka apeza mphamvu zochuluka.+   Amene anali okhuta ayenera kugwira ganyu kuti apeze chakudya,+Koma anjala, njala yawo yawathera.+ Ngakhale wosabereka, wabereka ana 7,+Koma amene anali ndi ana aamuna ambiri, wasiya kubereka.+   Yehova ndi Wakupha ndi Wosunga moyo,+Iye ndi Wotsitsira Kumanda,+ ndiponso Woukitsa.+   Yehova ndi Wopereka Umphawi+ ndi Wolemeretsa,+Wotsitsa ndiponso Wokweza,+   Iye amadzutsa wonyozeka, kumuchotsa pafumbi.+Amachotsa osauka padzala,+Kuti awakhazike pakati pa anthu olemekezeka,+ ndipo amawapatsa mpando wachifumu waulemerero.+Pakuti michirikizo ya dziko lapansi ndi ya Yehova,+Ndipo anakhazika dziko lapansi pamichirikizo imeneyo.   Mapazi a okhulupirika ake amawateteza.+Koma anthu oipa amawawononga mu mdima,+Pakuti munthu sakhala wapamwamba chifukwa cha mphamvu zake.+ 10  Onse olimbana ndi Yehova adzagwidwa ndi mantha.+Motsutsana nawo, iye adzagunda ngati mabingu kumwamba.+Yehova mwiniwake adzaweruza dziko lonse lapansi,+Kuti apereke mphamvu kwa mfumu yake,+Ndi kuti akweze nyanga ya wodzozedwa wake.”+ 11  Kenako Elikana anapita kunyumba kwake ku Rama, koma mwanayo anakhala mtumiki+ wa Yehova pamaso pa wansembe Eli. 12  Tsopano ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake.+ Iwo anali kunyalanyaza Yehova.+ 13  Munthu aliyense akamapereka nsembe ankayeneranso kupereka gawo la nyamayo kwa wansembe.+ Ndiyeno zimene zinali kuchitika n’zakuti, pamene nyama imeneyi inali kuwira, mtumiki wa wansembe anali kubwera ndi foloko ya mano atatu m’manja mwake.+ 14  Akatero anali kupisa mumphika kapena chophikira cha zigwiriro ziwiri, munkhali, kapena m’chophikira cha chigwiriro chimodzi. Ndipo wansembe anali kutenga chilichonse chimene folokoyo yatulutsa. Umu ndi mmene anali kuchitira ku Silo, kwa Aisiraeli onse opita kumeneko.+ 15  Komanso, asanapsereze mafuta,+ mtumiki wa wansembe anali kubwera kudzauza munthu wopereka nsembeyo kuti: “Ndipatse nyama yaiwisi kuti ndikamuwotchere wansembe, kuti wansembe asalandire nyama yophika koma yaiwisi.”+ 16  Wopereka nsembeyo akanena kuti: “Yembekeza kaye apsereze mafutawo,+ kenako utenge chilichonse chimene mtima wako ukufuna,”+ iye anali kuyankha kuti: “Ayi, ndipatse pompano, ukapanda kundipatsa, ndichita kulanda!”+ 17  Tchimo la atumikiwa linakula kwambiri pamaso pa Yehova,+ chifukwa amuna amenewa sanali kulemekeza nsembe ya Yehova.+ 18  Ndiyeno Samueli anali kutumikira+ pamaso pa Yehova, ali mwana ndipo anali kuvala efodi wansalu.+ 19  Komanso chaka ndi chaka mayi ake anali kumusokera kamalaya kakunja kodula manja. Iwo anali kumubweretsera kamalayako akabwera ndi mwamuna wawo kudzapereka nsembe ya pachaka.+ 20  Ndiyeno Eli anadalitsa+ Elikana ndi mkazi wake, ndipo anati: “Yehova akupatsenso mwana kudzera mwa mkazi uyu kulowa m’malo mwa amene anam’pereka kwa Yehova.”+ Kenako makolowo anabwerera kwawo, 21  ndipo Yehova anakomera mtima Hana,+ moti anayamba kutenga pakati ndipo anabereka ana aamuna atatu ndi aakazi awiri.+ Mwanayo Samueli anapitiriza kukula, akukondedwa ndi Yehova.+ 22  Ndiyeno Eli anali wokalamba kwambiri ndipo anamva+ zonse zimene ana ake anali kuchitira+ Aisiraeli onse, komanso anamva kuti anali kugona ndi akazi+ otumikira pakhomo la chihema chokumanako.+ 23  Ndipo iye anali kuwauza kuti:+ “Mukuchitiranji zinthu zoterezi?+ Chifukwatu anthu onse akundiuza zinthu zoipa zokhazokha zokhudza inu.+ 24  Musatero+ ana anga, chifukwa nkhani imene ndikumva, imene anthu a Yehova akufalitsa, si yabwino ayi.+ 25  Munthu akachimwira mnzake,+ Mulungu adzam’pepesera,+ koma kodi akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndani?”+ Koma anawo sanali kumvera bambo awo+ chifukwa tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+ 26  Izi zili choncho, mwanayo Samueli anali kukula ndi kukondedwa kwambiri ndi Yehova komanso anthu.+ 27  Ndiyeno munthu wa Mulungu+ anapita kwa Eli ndi kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi ine sindinadzisonyeze kunyumba ya kholo lako pamene anali akapolo kunyumba ya Farao ku Iguputo?+ 28  Kholo lakolo ndinalisankha kuchokera m’mafuko onse a Isiraeli kuti akhale wansembe wanga,+ ndipo azikwera paguwa langa lansembe+ kuti utsi wa nsembezo uzikwera kumwamba, kutinso azivala efodi pamaso panga. Ndinachita izi kuti ndipatse nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za ana a Isiraeli.+ 29  N’chifukwa chiyani anthu inu mukunyozabe nsembe zanga+ zimene ndinalamula m’nyumba yanga,+ n’kumalemekezabe ana anu koposa ine mwa kudzinenepetsa+ ndi mbali yabwino kwambiri ya nsembe iliyonse ya anthu anga Aisiraeli?+ 30  “‘N’chifukwa chake Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ndinanenadi kuti, A m’nyumba yako ndiponso a m’nyumba ya kholo lako adzanditumikira mpaka kalekale.”+ Koma tsopano Yehova akuti: “Sindingachitenso zimenezo, chifukwa amene akundilemekeza+ ndiwalemekeza,+ koma amene akundinyoza ndi opanda pake kwa ine.”+ 31  Tsopano imva izi, masiku adzafika pamene ndidzadula dzanja lako ndi la nyumba ya kholo lako, moti m’nyumba yako simudzakhala munthu wokalamba.+ 32  Ndipo m’nyumba yanga udzangoona mdani pakati pa zinthu zonse zabwino zimene zidzachitikira Isiraeli.+ M’nyumba yako simudzapezeka munthu wokalamba. 33  Koma pali munthu wa m’nyumba yako amene sindidzamuchotsa paguwa langa lansembe kuti achititse maso ako mdima ndi kukufooketsa. Ngakhale zili choncho, ochuluka a m’nyumba yako, anthu adzawapha ndi lupanga.+ 34  Ndipo chizindikiro chako chimene chidzachitikira ana ako awiri Hofeni ndi Pinihasi+ ndi ichi: Onse awiri adzafa tsiku limodzi.+ 35  Pamenepo ndidzadziutsira wansembe wokhulupirika+ amene adzachita mogwirizana ndi zimene zili mumtima mwanga ndi zofuna zanga. Ndidzam’mangira nyumba* yokhalitsa, ndipo adzatumikira wodzozedwa wanga+ monga wansembe nthawi zonse. 36  Ndiyeno aliyense wotsala+ m’nyumba yako adzafika ndi kumugwadira kuti alandire ndalama za malipiro ndi mtanda wobulungira wa mkate, ndipo adzati: “Ndiloleni chonde ndigwire ntchito monga wansembe kuti ndipezeko kachakudya.”’”+

Mawu a M'munsi

Kawirikawiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “nyanga” monga chizindikiro cha nyonga, mphamvu kapena ulamuliro.
Mawu akuti “nyumba” akutanthauza mzere wa ansembe.